Chakudya Choyeretsedwa ndi Chodetsedwa
1Yehova anayankhula ndi Mose ndi Aaroni kuti, 2“Awuze Aisraeli kuti, ‘Nyama zomwe mukhoza kudya mwa nyama zonse za dziko lapansi ndi izi: 3Nyama iliyonse imene ili ndi chipondero chogawikana pakati ndi yobzikula mukhoza kudya.
4“ ‘Koma pali nyama zina zimene zimabzikula kokha kapena ndi zogawikana zipondero zimene simukuyenera kudya. Nyama zimenezi ndi ngamira, ngakhale imabzikula ilibe zipondero zogawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye. 5Ina ndi mbira, ngakhale imabzikula, zipondero zake nʼzosagawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye. 6Inanso ndi kalulu, ngakhale amabzikula, zipondero zake nʼzosagawikana. Choncho ndi wodetsedwa, musadye. 7Nkhumba simabzikula ngakhale ili ndi zipondero zogawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye. 8Musamadye nyama yake kapena kukhudza imene yafa chifukwa ndi yodetsedwa.
9“ ‘Mwa zamoyo zonse zimene zimakhala mʼmadzi a mʼnyanja ndi a mʼmitsinje mukhoza kudya chilichonse chimene chili ndi minga ya pa msana ndi mamba. 10Koma zamoyo zonse za mʼnyanja kapena za mʼmitsinje zimene zilibe minga ya pa msana ndi mamba, kaya ndi tizirombo tonse ta mʼmadzi ndi zamoyo zonse zopezeka mʼmenemo ndi zodetsedwa kwa inu. 11Pakuti zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu, nyama yake musadye, ndipo zikafa zikhalebe zodetsedwa kwa inu. 12Chamoyo chilichonse cha mʼmadzi chimene chilibe minga ya pa msana kapena mamba ndi chodetsedwa kwa inu.
13“ ‘Mbalame zimene simukuyenera kudya chifukwa ndi zodetsedwa ndi izi: mphungu, nkhwazi, mwimba, 14nankapakapa, akamtema a mitundu yonse, 15akhungubwi a mitundu yonse, 16kadzidzi wamphondo, kadzidzi wodzuma, chipudo ndi mtundu uliwonse wa akabawi 17kadzidzi wamngʼono, chiswankhono ndi mantchichi, 18tsekwe, vuwo, dembo, 19indwa, zimeza za mitundu yonse, nsadzu ndi mleme.
20“ ‘Zowuluka zonse za miyendo inayi ndi zodetsedwa. 21Komabe mwa zowuluka zokhala ndi miyendo inayi zimene mukhoza kudya ndi zokhazo zimene zili ndi miyendo yolumphira. 22Pa zimenezo mungathe kudya izi: dzombe la mitundu yonse, atsokonombwe a mitundu yonse, nkhululu za mitundu yonse, ndi ziwala za mitundu yonse. 23Koma za mapiko zina zonse zokhala ndi miyendo inayi muzitenge kukhala zodetsedwa kwa inu.
24“ ‘Zimenezi zidzakudetsani. Aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 25Aliyense wonyamula chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
26“ ‘Nyama iliyonse imene ili ndi ziboda zogawikana koma mapazi ake wosagawikana, kapena imene sibzikula muyiyese yodetsedwa kwa inu ndipo munthu aliyense akakhudza nyama yakufayo, adzakhala wodetsedwa. 27Mwa nyama zonse zoyenda ndi miyendo inayi, nyama zonse zokhala ndi zikhadabo kuphazi muzitenge kukhala zodetsedwa ndipo aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 28Aliyense wonyamula nyamazi zitafa ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu.
29“ ‘Mwa nyama zokwawa, zimene zili zodetsedwa kwa inu ndi izi: likongwe, mbewa, msambulu za mitundu yonse, 30gondwa, mngʼazi, buluzi, dududu ndi nanzikambe. 31Mwa nyama zonse zoyenda pansi, zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu. Munthu aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 32Iliyonse mwa nyama zimenezi ikafa ndi kugwera pa chiwiya chilichonse, kaya chimagwira ntchito yotani, kaya ndi chopangidwa ndi mtengo, kaya ndi cha nsalu, kaya ndi cha chikopa kapena chiguduli chiwiyacho chidzakhala chodetsedwa. Muchiviyike mʼmadzi chiwiyacho komabe chidzakhala chodetsedwa mpaka madzulo, ndipo kenaka chidzakhala choyeretsedwa. 33Tsono nyama ina iliyonse mwa zimenezi ikagwera mʼmbiya ya dothi, ndiye kuti chilichonse cha mʼmbiyamo chidzakhala chodetsedwa, ndipo muyenera kuswa mbiyayo. 34Chakudya chilichonse chimene mungadye chikakhala kuti chathiridwa mʼmbiyamo, ndiye kuti chakudyacho chidzakhala chodetsedwa, ndipo madzi akumwa wochokera mʼmbiya zotere ndi wodetsedwa. 35Chiwalo chilichonse cha nyama yakufa chikagwera pa chinthu chilichonse kaya pa uvuni, kapena pa mʼphika, ndiye kuti zinthuzo zidzakhala zodetsedwa, ndipo ziphwanyidwe popeza ndi zodetsedwa. 36Koma kasupe kapena chitsime chamadzi chidzakhala choyeretsedwa ngakhale kuti chilichonse chokhudza nyama yakufayo chidzakhala chodetsedwa. Zimenezi muzitenge kukhala zodetsedwa. 37Chiwalo chilichonse cha nyama yakufayo chikagwera pa mbewu zimene akuti adzale, mbewu zimenezo zidzakhalabe zabwino. 38Koma mbewuzo zikakhala zonyowa ndi madzi, ndipo chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo chikagwera pa mbewuzo, mbewuzo zikhale zodetsedwa kwa inu.
39“ ‘Ngati nyama imene mumaloledwa kudya yafa yokha, ndiye kuti aliyense wokhudza nyama yakufayo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 40Aliyense amene adyako nyama yakufayo achape zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Aliyense amene wanyamula nyama yakufayo ayenera kuchapa zovala zake, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
41“ ‘Chinthu chilichonse chokwawa pansi ndi chonyansa, simuyenera kudya. 42Musadye chilichonse chokwawa pansi, choyenda chamimba kapena choyenda ndi miyendo inayi kapenanso yambiri popeza ndi chodetsedwa. 43Musadzisandutse nokha odetsedwa ndi chokwawa chilichonse. Musadziyipitse nazo, kuti mukhale odetsedwa. 44Ine ndine Yehova Mulungu wanu, choncho dziyeretseni kuti mukhale woyera, chifukwa Ine ndine woyera. Musadzisandutse odetsedwa ndi chokwawa chilichonse. 45Ine ndine Yehova amene ndinakutulutsani ku Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Tsono mukhale woyera, chifukwa Ine ndine woyera.
46“ ‘Amenewa ndi malamulo onena za nyama, mbalame, chamoyo chilichonse choyenda mʼmadzi ndiponso chamoyo chilichonse chokwawa. 47Muzisiyanitsa pakati pa chodetsedwa ndi choyeretsedwa, komanso pakati pa zomwe mutha kudya ndi zomwe simuyenera kudya.’ ”
Прописи о чистој и нечистој храни
1Господ рече Мојсију и Арону: 2„Реците Израиљцима: ’Од свих животиња на земљи, ово су оне које смете јести: 3сваку која има папке, и то раздвојене папке, и која прежива, можете јести.
4Међутим, од оних животиња што преживају, или имају раздвојене папке не једите: камилу, јер иако прежива, нема раздвојене папке; нечиста је за вас; 5даман11,5 Сисар величине зеца који настањује Африку и југозападну Азију., јер иако прежива, нема раздвојене папке; нечист је за вас; 6дивљег зеца, јер иако прежива, нема раздвојене папке; нечист је за вас; 7свињу, јер иако има раздвојене папке, не прежива; обредно је нечиста за вас. 8Не једите њихово месо, и не дотичите њихову стрвину; нечисте су за вас.
Водене животиње
9Од свега што је у води, ове једите: све што је у води, у морима или рекама, и има пераје и крљушт, то можете јести. 10А све што је у морима и рекама, а нема пераје и крљушт, од свега што врви у води, и од свих других живих бића – за вас је одвратно. 11Држите их за одвратне; не једите њихово месо, и нека вам њихова лешина буде одвратна. 12Све што је у води, а нема пераје и крљушт – за вас је одвратно.
Птице
13Ово су птице које морате сматрати нечистима. Не једите их, јер су одвратне за вас: орао, лешинар, јастреб, 14крагуј, кобац сваке врсте, 15све врсте гаврана, 16ној, сова, галеб, све врсте крагуја, 17ћук, корморан, буљина, 18лабуд, буљина, белоглави суп, 19рода, све врсте чапљи, пупавац и слепи миш.
Остале животиње
20Сва крилата бића која гамижу и иду на четири ноге, за вас су одвратна. 21Од свих бића која гамижу и иду на четири ноге, ове можете јести: оне које изнад својих ногу имају зглобове којима скачу по земљи. 22Од ових можете јести: све врсте скакаваца, све врсте цврчака, и све врсте аргола и зрикаваца. 23А свако крилато биће које гамиже, а има четири ноге, за вас је одвратно.
24Ова ће вас учинити нечистима; ко год дотакне њихову лешину биће нечист до вечери. 25Ко год понесе њихову лешину, нека опере своју одећу; биће нечист до вечери.
26Свака животиња која има нераздвојене папке и не прежива, за вас је нечиста и нечист ће бити свако ко их се дотакне. 27Све што хода на шапама међу животињама које ходају на четири ноге, за вас су нечисте. Ко год се дотакне њихове лешине, биће нечист до вечери. 28Ко понесе њихову лешину, нека опере своју одећу; биће нечист до вечери. За вас су нечисте.
Гмизавци
29Од животиња што пузе по земљи за вас су нечисте: ласица, миш, и све врсте великих гуштера, 30гекон, крокодил, зелембаћ, даждевњак и камелеон. 31Од животиња што пузе те су нечисте за вас. Ко год их дотакне кад угину биће нечист до вечери. 32Кад нека од ових животиња мртва падне на нешто, то ће бити нечисто, било то дрвена посуда, одећа, кожа, или кострет, то јест, сваки предмет који служи чему. То нека се замочи у воду, и биће нечисто до вечери. Потом ће бити чисто. 33Ако нека од њих упадне у било коју земљану посуду, све што је у њој биће нечисто. Зато је разбијте.
34Свака храна која се једе, ако у њу доспе вода из такве посуде, постаће нечиста, и свако пиће које се пије биће нечисто ако је било у таквој посуди. 35Ако лешина неке од ових животиња падне на нешто, то ће бити нечисто, било пећ или огњиште. То нека се развали. Оне су нечисте и за вас ће остати нечисте. 36Ипак, извор или чатрња где се скупља вода биће чисти, али онај ко дотакне њихову лешину биће нечист. 37Ако таква стрвина падне на семе за сетву, семе ће остати чисто. 38Али ако вода овлажи семе и стрвина падне на њега, за вас ће бити нечисто.
39Ако угине животиња коју смете јести, свако ко је додирне биће нечист до вечери. 40Онај који поједе од њене стрвине биће нечист до вечери, а ко понесе њену стрвину нека опере своју одећу и буде нечист до вечери.
41Свака животиња која пузи по земљи је одвратна. Нека се не једе! 42Све што иде на трбуху, и све што се креће на четири ноге, и све што има много ногу, и сва бића што пузе по земљи, то не смете јести, јер су одвратне. 43Немојте се поганити ниједним бићем које пузи; не скрнавите се њима да не постанете нечисти. 44Јер ја сам Господ, Бог ваш! Зато будите свети, јер сам ја свет. Не скрнавите се ниједним бићем што пузи по земљи. 45Ја сам Господ који вас је извео из земље египатске да вам будем Бог. Стога будете свети, јер ја сам свет!
46Ово су закони о животињама, птицама и сваком живом бићу које врви у води, и сваком бићу које пузи по земљи, 47да се прави разлика између нечистог и чистог; између животиња која се могу јести и животиња која се не могу јести.’“