Levitiko 10 – CCL & CARST

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 10:1-20

Imfa ya Nadabu ndi Abihu

1Ana a Aaroni, Nadabu ndi Abihu, aliyense anatenga chofukizira lubani chake nayikamo makala a moto ndi kuthiramo lubani. Iwo anapereka pamaso pa Yehova moto wachilendo, moto umene Yehova sanawalamule. 2Choncho moto unatuluka pamaso pa Yehova ndi kuwapsereza, ndipo anafa pamaso pa Yehova. 3Pamenepo Mose anawuza Aaroni kuti, “Pajatu Yehova ananena kuti,

“ ‘Kwa iwo amene amandiyandikira

ndidzaonetsa ulemerero wanga;

pamaso pa anthu onse

ndidzalemekezedwa.’ ”

Aaroni anakhala chete wosayankhula.

4Mose anayitana Misaeli ndi Elizafani, ana a Uzieli, abambo angʼono a Aaroni, ndipo anawawuza kuti, “Bwerani kuno mudzachotse abale anuwa pa malo wopatulika ndi kuwatulutsira kunja kwa msasa.” 5Choncho anabwera atavala minjiro yawo ndipo anawatenga ndi kuwatulutsa kunja kwa msasawo monga momwe Mose analamulira.

6Ndipo Mose anawuza Aaroni ndi ana ake Eliezara ndi Itamara kuti, “Musalileke tsitsi lanu nyankhalala ndipo musangʼambe zovala zanu kuti mungafe, ndi mkwiyo wa Yehova ungagwere anthu onsewa. Koma abale anu okha, kutanthauza fuko lonse la Israeli ndiwo ayenera kulira omwalira aja amene Yehova wawapsereza ndi moto. 7Musatuluke kunja kwa tenti ya msonkhano, mungafe, chifukwa munadzozedwa ndi mafuta a Yehova kukhala ansembe.” Choncho iwo anachita monga Mose ananenera.

8Pambuyo pake Yehova anayankhula ndi Aaroni nati, 9“Iwe ndi ana ako musamamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa pamene mukulowa mu tenti ya msonkhano kuti mungafe. Ili ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse. 10Muzisiyanitsa pakati pa zinthu zopatulika ndi zinthu wamba, pakati pa zinthu zodetsedwa ndi zinthu zoyeretsedwa, 11ndipo muyenera kuphunzitsa Aisraeli onse malamulo amene Yehova wakupatsani kudzera mwa Mose.”

12Mose anawuza Aaroni ndi ana ake otsalawo, Eliezara ndi Itamara kuti, “Tengani zopereka zachakudya zopanda yisiti zimene zatsala pa nsembe zopsereza za kwa Yehova ndipo muzidye pafupi ndi guwa pakuti ndi zopatulika kwambiri. 13Muzidye pa malo wopatulika chifukwa zimenezi ndi gawo lako ndi la ana ako pa zopereka zopsereza kwa Yehova. Izitu ndi zimene Yehova anandilamulira. 14Koma iwe pamodzi ndi ana ako aamuna ndi aakazi muzidya chidale chimene chinaweyulidwa ndi ntchafu zimene zinaperekedwa nsembe. Muzidye pamalo woyeretsedwa. Zimenezi zaperekedwa kwa iwe ndi ana ako monga gawo lanu pa zopereka zachiyanjano zimene apereka Aisraeli. 15Ntchafu imene inaperekedwayo ndi chidale chomwe chinaweyulidwacho abwere nazo pamodzi ndi nsembe ya mafuta ya Yehova yotentha pa moto, ndipo uziweyule kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Yehova. Zimenezi zizikhala zako ndi ana ako nthawi zonse monga walamulira Yehova.”

16Pambuyo pake Mose anafunafuna mbuzi ya nsembe yopepesera machimo koma anapeza kuti anayitentha kale. Apa Mose anakalipira Eliezara ndi Itamara, ana a Aaroni otsala aja nati, 17“Chifukwa chiyani simunadyere pamalo wopatulika nsembe yopepesera machimo ija? Kodi imene ija siyopatulika? Kodi Yehova sanapereke nyamayo kwa inu kuti muchotse machimo a mpingo wonse powachitira mwambo wa nsembe yopepesera machimo pamaso pa Yehova? 18Pakuti magazi ake sanalowe nawo ku Malo Wopatulika, mukanadya nyama ya mbuziyo pa malo wopatulikawo monga Yehova analamulira.”

19Aaroni anamuyankha Mose kuti, “Lero anthu apereka nsembe yawo yopepesera machimo ndiponso nsembe yawo yopsereza pamaso pa Yehova komabe zinthu zoterezi zandichitikira. Kodi Yehova akanakondwa ndikanadya nsembe yopepesera machimo lero?” 20Pamene Mose anamva zimenezi, anakhutira.

Священное Писание (Восточный перевод), версия для Таджикистана

Левит 10:1-20

Смерть Надава и Авиуда, нарушивших правила жертвоприношения

1Сыновья Хоруна Надав и Авиуд взяли сосуды, положили в них тлеющие угли, добавили благовоний и принесли Вечному чуждый огонь10:1 Священнослужители должны были использовать уголь от жертвенника для жертвы всесожжения, чтобы жечь благовония (см. 16:12), но, вероятно, сыновья Хоруна использовали «чуждый» огонь из другого источника. Также возможно, что сыновья Хоруна были пьяны, потому что, согласно 9 стиху, Вечный тут же предупреждает священнослужителей не пить вина и пива., чего Он им не велел. 2Тогда Вечный послал огонь, который сжёг их, и они погибли перед Вечным. 3Тогда Мусо сказал Хоруну:

– Это то, о чём Вечный говорил:

«Среди приближающихся ко Мне Я явлю Свою святость;

на глазах у всего народа Я прославлюсь».

Хорун промолчал.

4Мусо позвал Мисаила и Элцафана, сыновей Узиила, дяди Хоруна, и сказал им:

– Подойдите и вынесите ваших родственников за лагерь, подальше от святилища.

5Они подошли и, взяв их за рубашки, вынесли за лагерь, как приказал Мусо.

6Мусо сказал Хоруну и его сыновьям Элеазару и Итамару:

– Не оплакивайте их, распуская волосы10:6 Или: «обнажая голову». и разрывая на себе одежду, иначе вы умрёте, а Вечный разгневается на весь народ. Но ваши сородичи, весь народ Исроила, могут оплакивать тех, кого Вечный испепелил. 7Не уходите от входа в шатёр встречи, иначе вы умрёте, ведь на вас помазание Вечного.

Они исполнили то, что сказал Мусо.

Обязанности священнослужителей

8Вечный сказал Хоруну:

9– Ты и твои сыновья не должны пить вино или другие алкогольные напитки, когда входите в шатёр встречи, иначе вы умрёте. Это вечное установление для грядущих поколений. 10Различайте между священным и несвященным, между чистым и нечистым 11и учите исроильтян установлениям, которые Вечный дал через Мусо.

12Мусо сказал Хоруну и его оставшимся сыновьям Элеазару и Итамару:

– Возьмите хлебное приношение, которое осталось из огненных жертв Вечному, и ешьте его, приготовленное без закваски, возле жертвенника, потому что это великая святыня. 13Ешьте его на святом месте, потому что оно – ваша доля и доля ваших сыновей в огненных жертвах Вечному; мне было так велено. 14Ты, твои сыновья и дочери можете есть грудину потрясания и бедро возношения. Ешьте их на чистом месте; они даны тебе и твоим детям как доля в жертвах примирения, приносимых исроильтянами. 15Бедро возношения и грудину потрясания следует приносить с жиром огненных жертв, чтобы их потрясали перед Вечным как приношение потрясания. Это будет постоянной долей тебе и твоим детям, как повелел Вечный.

16Когда Мусо спросил о козле жертвы за грех и узнал, что его уже сожгли, он разгневался на Элеазара и Итамара, оставшихся сыновей Хоруна. Он спросил:

17– Почему вы не ели жертву за грех на святом месте? Это великая святыня; она была дана вам, чтобы вы сняли вину народа, очистив его перед Вечным. 18Раз её кровь не внесли в святилище, вы должны были съесть жертву на святом месте, как я велел.

19Хорун ответил Мусо:

– Сегодня они принесли жертву за грех и всесожжение Вечному, и всё же со мной случилось такое! Неужели Вечному было бы угодно, если бы я сегодня съел приношение за грех?

20Услышав это, Мусо согласился.