Levitiko 1 – CCL & NIRV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 1:1-17

Nsembe Zopsereza

126 Yehova anayitana Mose mu tenti ya msonkhano. Iye anati, 2“Aliyense wa inu ngati abwera ndi nsembe kwa Yehova kuchokera pa ziweto zake, choperekacho chikhale ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi.

3“ ‘Ngati munthu apereka nsembe yopsereza ya ngʼombe, ikhale yayimuna yopanda chilema. Aziyipereka pa khomo la tenti ya msonkhano, kuti Yehova alandire. 4Munthuyo asanjike dzanja lake pa mutu pa nsembe yopserezayo, ndipo idzalandiridwa kuti ikhale yopepesera machimo ake. 5Pambuyo pake aphe ngʼombeyo pamaso pa Yehova, ndipo ansembe, ana a Aaroni, atenge magazi ake ndi kuwawaza mbali zonse za guwa lansembe limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano. 6Munthuyo asende nsembe yopserezayo ndi kuyidula nthulinthuli. 7Ndipo ana a Aaroni, wansembe uja asonkhe moto pa guwa ndi kuyalapo nkhuni pa motopo. 8Kenaka ana a Aaroni, wansembe uja, ayike nthuli za nyamayo, mutu wake pamodzi ndi mafuta omwe pa nkhuni zimene zili paguwapo. 9Munthuyo atsuke zamʼkati mwa nyamayo pamodzi ndi miyendo yake yomwe, ndipo wansembe awotche nyama yonse paguwapo. Iyi ndi nsembe yopsereza, chopereka chowotcha pa moto, cha fungo lokomera Yehova.

10“ ‘Koma ngati chopereka cha nsembe yopserezayo ndi nkhosa kapena mbuzi kuchokera pa ziweto zake, munthuyo apereke yayimuna yopanda chilema. 11Ayiphere kumpoto kwa guwa, pamaso pa Yehova, ndipo ana a Aaroni amene ndi ansembe, awaze magazi ake mbali zonse za guwalo. 12Kenaka ayidule nyamayo nthulinthuli, ndipo wansembe ayike nthulizo pa guwa, atengenso mutu ndi mafuta omwe, ndipo ayike zonsezi pa nkhuni zimene zikuyaka pa guwa. 13Munthuyo atsuke zamʼkati mwa nyamayo pamodzi ndi miyendo yake yomwe, ndipo wansembe abwere nazo zonse ndi kuzitentha pa guwa. Iyi ndi nsembe yopsereza, chopereka chotentha pa moto, fungo lokomera Yehova.

14“ ‘Koma ngati chopereka kwa Yehova ndi nsembe yopsereza ya mbalame, ndiye ikhale njiwa kapena mawunda. 15Wansembe abwere nayo ku guwa, ayidule mutu moyipotola ndi kutentha mutuwo pa guwa. Magazi ake awathire pansi kuti ayenderere pambali pa guwa. 16Iye achotse chithokomiro pamodzi ndi nthenga zake zomwe ndi kuzitaya ku malo wotayirako phulusa, kummawa kwa guwalo. 17Kenaka ayingʼambe pakati, koma asachotse mapiko. Ndipo wansembe ayiwotche pa nkhuni zimene zikuyaka pa guwa. Imeneyi ndi nsembe yopsereza, yowotcha pa moto ndiponso ya fungo lokomera Yehova.

New International Reader’s Version

Leviticus 1:1-17

Rules for Burnt Offerings

1The Lord called out to Moses. He spoke to him from the tent of meeting. He said, 2“Speak to the Israelites. Tell them, ‘Suppose anyone among you brings an offering to the Lord. They must bring an animal from their herd or flock.

3“ ‘If someone brings a burnt offering from the herd, they must offer a male animal. It must not have any flaws. They must bring it to the entrance to the tent of meeting. Then the Lord will accept it. 4They must place their hand on the head of the burnt offering. Then the Lord will accept it in place of them. It will pay for their sin. 5The young bull must be killed there in the sight of the Lord. Then the priests in Aaron’s family line must bring its blood to the altar. They must splash it against the sides of the altar. The altar stands at the entrance to the tent of meeting. 6The skin must be removed from the animal brought for the burnt offering. Then the animal must be cut into pieces. 7The priests in Aaron’s family line must build a fire on the altar. They must place wood on the fire. 8Then they must place the pieces of the animal on the burning wood on the altar. The pieces include the head and the fat. 9The inside parts of the animal must be washed with water. The legs must also be washed. The priest must burn all of it on the altar. It is a burnt offering. It is a food offering. Its smell pleases the Lord.

10“ ‘If someone offers a burnt offering from the flock, it must be a male animal. It can be a sheep or a goat. It must not have any flaws. 11They must kill it at the north side of the altar in the sight of the Lord. The priests in Aaron’s family line must splash its blood against the sides of the altar. 12They must cut the animal into pieces. The priest must place the pieces on the burning wood on the altar. The pieces include the head and the fat. 13They must wash the inside parts with water. The legs must also be washed. The priest must bring all the parts to the altar. He must burn them there. It is a burnt offering. It is a food offering. Its smell pleases the Lord.

14“ ‘If someone offers to the Lord a burnt offering of birds, it must be a dove or a young pigeon. 15The priest must bring it to the altar. He must twist its head off. Then he must burn the rest of the bird on the altar. Its blood must be emptied out on the side of the altar. 16The priest must remove the small bag inside the bird’s throat. He must also remove the feathers. Then he must throw them to the east side of the altar. That is where the ashes are. 17He must take hold of the wings of the bird and tear it open. But he must not tear it in two. Then the priest will burn it on the wood burning on the altar. It is a burnt offering. It is a food offering. Its smell pleases the Lord.