Hoseya 8 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Hoseya 8:1-14

Israeli Akolola Kamvuluvulu

1“Ika lipenga pakamwa pako.

Ngati chiwombankhanga, kutsutsana ndi nyumba ya Yehova

chifukwa anthu aphwanya pangano langa

ndiponso agalukira lamulo langa.

2Israeli akulirira kwa Ine kuti,

‘Inu Mulungu wathu, ife timakudziwani!’

3Koma Israeli wakana zabwino;

mdani adzamuthamangitsa.

4Amalonga mafumu mosatsata kufuna kwanga.

Amasankha akalonga popanda chilolezo changa.

Amadzipangira mafano

asiliva ndi agolide

koma adzawonongeka nawo.

5Iwe Samariya, taya fano lako la mwana wangʼombe!

Mkwiyo wanga wayakira anthuwo.

Padzapita nthawi yayitali chotani asanasinthike kukhala oyera mtima?

6Mafanowa ndi ochokera ku Israeli!

Mwana wa ngʼombe uyu anapangidwa ndi munthu waluso;

si Mulungu amene anamupanga.

Adzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswa,

mwana wangʼombe wa ku Samariya.

7“Aisraeli amadzala mphepo

ndipo amakolola kamvuluvulu.

Tirigu alibe ngala;

sadzabala chakudya.

Akanabala chakudya

alendo akanadya chakudyacho.

8Israeli wamezedwa,

tsopano ali pakati pa anthu a mitundu ina

ngati chinthu cha chabechabe.

9Pakuti iwo anapita ku Asiriya

ngati mbidzi yongodziyendera pa yokha.

Efereimu wadzigulitsa kwa zibwenzi zake.

10Ngakhale wadzigulitsa pakati pa mitundu ya anthu,

Ine ndidzawasonkhanitsa pamodzi.

Iwo adzayamba kuzunzika pansi pa

ulamuliro wankhanza wa mfumu yamphamvu.

11“Ngakhale Efereimu anamanga maguwa ambiri a nsembe zoperekedwa chifukwa cha tchimo,

maguwa amenewa akhala malo ochimwirapo.

12Ndinawalembera zinthu zambiri za malamulo anga,

koma iwo anaziyesa ngati zinthu zachilendo.

13Amapereka nsembe za nyama kwa Ine

ndipo iwo amadya nyamayo,

koma Yehova sakondwera nazo.

Tsopano Iye adzakumbukira zoyipa zawo

ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo:

iwowo adzabwerera ku Igupto.

14Israeli wayiwala Mlengi wake

ndipo wamanga nyumba zaufumu;

Yuda wachulukitsa mizinda ya malinga.

Koma Ine ndidzaponya moto pa mizinda yawoyo,

moto umene udzatenthe malinga awo.”