Hoseya 6 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Hoseya 6:1-11

Kusalapa kwa Israeli

1“Bwerani, tiyeni tibwerere kwa Yehova.

Iye watikhadzula,

koma adzatichiritsa.

Iye wativulaza,

koma adzamanga mabala athu.

2Pakapita masiku awiri adzatitsitsimutsa;

pa tsiku lachitatu Iye adzatiukitsa

kuti tikhale ndi moyo pamaso pake.

3Tiyeni timudziwe Yehova,

tiyeni tilimbike kumudziwa Iye.

Adzabwera kwa ife mosakayikira konse

ngati kutuluka kwa dzuwa;

adzabwera kwa ife ngati mvula ya mʼchilimwe,

ngati mvula ya nthawi yamphukira imene imakhathamiritsa nthaka.”

4Iwe Efereimu, kodi ndichite nawe chiyani?

Kodi ndichite nawe chiyani, iwe Yuda?

Chikondi chanu chili ngati nkhungu yammawa,

ngati mame a mmamawa amene amakamuka msanga.

5Choncho ndakuwazani ngati nkhuni kudzera mwa aneneri anga,

ndakuphani ndi mawu a pakamwa panga;

chigamulo changa chinangʼanima ngati mphenzi pa inu.

6Pakuti Ine ndimafuna chifundo osati nsembe,

ndi kudziwa Mulungu kulekana ndi nsembe zopsereza.

7Monga Adamu, anthuwa aphwanya pangano langa,

iwo sanakhulupirike kwa Ine.

8Giliyadi ndi mzinda wa anthu ochita zoyipa,

okhala ndi zizindikiro za kuphana.

9Monga momwe mbala zimadikirira anthu,

magulu a ansembe amachitanso motero;

iwo amapha anthu pa njira yopita ku Sekemu,

kupalamula milandu yochititsa manyazi.

10Ndaona chinthu choopsa kwambiri

mʼnyumba ya Israeli.

Kumeneko Efereimu akuchita zachiwerewere,

ndipo Israeli wadzidetsa.

11“Kunenanso za iwe Yuda,

udzakolola chilango.

“Pamene ndiwabwezere anthu anga zinthu zabwino.”