Hoseya 4 – CCL & NIRV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Hoseya 4:1-19

Yehova Ayimba Mlandu Israeli

1Inu Aisraeli, imvani mawu a Yehova,

chifukwa Yehova ali ndi mlandu ndi inu

amene mumakhala mʼdzikoli:

“Mʼdziko mwanu mulibe kukhulupirika, mulibe chikondi

mulibe kulabadira za Mulungu.

2Muli kutemberera kokha, kunama ndi kupha.

Kuba ndi kuchita chigololo;

machimo achita kunyanya

ndipo akungokhalira kuphana.

3Chifukwa chake dziko likulira

ndipo onse amene amakhalamo akuvutika;

zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga

ndiponso nsomba zamʼnyanja zikufa.

4“Koma wina asapeze mnzake chifukwa,

wina aliyense asayimbe mlandu mnzake,

pakuti anthu ako ali ngati anthu

amene amayimba mlandu wansembe.

5Mumapunthwa usana ndi usiku

ndipo aneneri amapunthwa nanu pamodzi.

Choncho ndidzawononga amayi anu.

6Anthu anga akuwonongeka chifukwa chosadziwa.

“Pakuti mwakana kudziwa,

Inenso ndidzakukanani monga ansembe anga;

chifukwa mwayiwala lamulo la Mulungu wanu,

Inenso ndidzayiwala ana anu.

7Ansembe ankati akachuluka

iwo ankandichimwiranso kwambiri;

iwo anasinthanitsa ulemerero wawo ndi chinthu china chonyansa.

8Amalemererapo pa machimo a anthu anga

ndipo amafunitsitsa kuti anthuwo azipitiriza kuchimwa.

9Ndipo zidzakhala motere: zochitikira anthu ena, zidzachitikiranso ansembe.

Ndidzawalanga onsewo chifukwa cha njira zawo,

ndidzawabwezera chifukwa cha machitidwe awo.

10“Iwo azidzadya koma sadzakhuta;

azidzachita zachiwerewere koma sadzachulukana,

chifukwa anasiya Yehova

kuti adzipereke 11ku zachiwerewere,

ku vinyo wakale ndi watsopano,

zimene zimachotsa nzeru zomvetsa zinthu

12za anthu anga.

Anthu anga amapempha nzeru ku fano lamtengo

ndipo ndodo yawo yamtengo imawayankha.

Mzimu wachiwerewere umawasocheretsa;

iwo sakukhulupirika kwa Mulungu wawo.

13Amapereka nsembe pamwamba pa mapiri

ndi kufukiza lubani pa zitunda,

pa tsinde pa mtengo wa thundu, mnjale ndi mkundi,

pamene pali mthunzi wabwino.

Nʼchifukwa chake ana anu aakazi akuchita zachiwerewere

ndipo akazi a ana anu akuchita zigololo.

14“Ine sindidzalanga ana anu aakazi

pamene iwo adzachita zachiwerewere,

kapena akazi a ana anu

pamene adzachita zigololo.

Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere,

ndipo mumapereka nsembe pamodzi ndi akazi achiwerewere a ku malo opembedzerako.

Anthu amene alibe nzeru adzawonongeka ndithu!

15“Ngakhale umachita chigololo, iwe Israeli,

Yuda asapezeke ndi mlandu wotere.

“Usapite ku Giligala.

Usapite ku Beti-Aveni.

Ndipo usalumbire kuti, ‘Pali Yehova wamoyo!’

16Aisraeli ndi nkhutukumve,

ngosamva ngati ana angʼombe.

Kodi Yehova angathe kuwaweta bwanji

ngati ana ankhosa pa msipu wabwino?

17Efereimu waphathana ndi mafano;

mulekeni!

18Ngakhale pamene zakumwa zawo zatha,

amapitiriza kuchita zachiwerewere;

atsogoleri awo amakonda kwambiri njira zawo zochititsa manyazi.

19Adzachotsedwa ndi kamvuluvulu

ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zawo.

New International Reader’s Version

Hosea 4:1-19

The Lord Brings Charges Against Israel

1People of Israel, listen to the Lord’s message.

He is bringing charges

against you who live in Israel.

He says, “There is no faithfulness

or love in the land.

No one recognizes me as God.

2People curse one another.

They tell lies and commit murder.

They steal and commit adultery.

They break all my laws.

They keep spilling the blood of other people.

3That is why the land is drying up.

All those who live in it

are getting weaker and weaker.

The wild animals and the birds in the sky are dying.

So are the fish in the ocean.

4“But you priests should not blame the people.

You should not find fault with one another.

After all, your people

could also bring charges against you.

5You trip and fall day and night.

And the prophets fall down along with you.

So I will destroy your nation.

She is the one who gave birth to you.

6My people are destroyed

because they do not know me.

“You priests have refused to obey me.

So I will refuse to accept you as my priests.

You have not paid any attention to my law.

So I will not let your children be my priests.

7The more priests there were,

the more they sinned against me.

They have traded their glorious God for that shameful god named Baal.

8They live off the sins of my people.

And they want them to keep on sinning.

9So here is what I will do.

I will punish people and priests alike.

I will judge them because of their sinful lives.

I will pay them back

for the evil things they have done.

10“My people will eat.

But they will not have enough.

They will have sex with prostitutes.

But they will not have any children.

That’s because they have deserted me.

They have sex 11with prostitutes.

They drink old wine and fresh wine.

Their drinking has destroyed their ability to understand.

12My people ask a wooden statue of a god for advice.

They get answers from a stick of wood.

They are as unfaithful as prostitutes.

They are not faithful to their God.

13They offer sacrifices on the mountaintops.

They burn offerings on the hills.

They worship under oak, poplar and terebinth trees.

The trees provide plenty of shade.

So your daughters become prostitutes.

And your daughters-in-law commit adultery.

14“I will not punish your daughters

when they become prostitutes.

I will not judge your daughters-in-law

when they commit adultery.

After all, the men themselves have sex with sinful women.

They offer sacrifices where temple prostitutes earn their living.

People who can’t understand will be destroyed!

15“Israel, you are not faithful to me.

But I do not want Judah to become guilty too.

“My people, do not go to Gilgal to offer sacrifices.

Do not go up to Bethel to worship other gods.

When you make a promise, do not say,

‘You can be sure that the Lord is alive.’

16The people of Israel are stubborn.

They are as stubborn as a young cow.

So how can I take care of them

like lambs in a meadow?

17The people of Ephraim have joined themselves to other gods.

And nothing can be done to help them.

18They continue to be unfaithful to me

even when their drinks are gone.

And their rulers love to do shameful things.

19A windstorm will blow all of them away.

And their sacrifices will bring shame on them.