Hoseya 2 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Hoseya 2:1-23

1“Nena kwa abale ako kuti, ‘Ndinu anthu anga,’ kwa alongo ako kuti ‘Ndinu okondedwa anga.’ ”

Kulangidwa ndi Kubwezeretsedwa kwa Israeli

2“Dzudzulani amayi anu, adzudzuleni iwo,

pakuti si mkazi wanga,

ndipo ine sindine mwamuna wake.

Iyeyo achotse maonekedwe adama pa nkhope yake,

ndi kusakhulupirika pa mawere ake.

3Akapanda kutero ndidzamuvula,

ndipo adzakhala wamaliseche monga tsiku limene anabadwa;

ndidzamuwumitsa ngati chipululu,

adzakhala ngati dziko lopanda madzi,

ndi kumupha ndi ludzu.

4Sindidzaonetsa chikondi changa pa ana ake,

chifukwa ndi ana a mʼchiwerewere.

5Amayi awo akhala akuchita zachiwerewere

ndipo anawabereka anawo akuchita zinthu zochititsa manyazi.

Iwo anati, ‘Ine ndidzatsatira zibwenzi zanga,

zimene zimandipatsa chakudya ndi madzi,

ubweya ndi thonje, mafuta ndi chakumwa.’

6Choncho njira yake ndidzayitseka ndi minga;

ndidzamuzinga ndi khoma kotero kuti sadzapezanso njira yotulukira.

7Adzathamangira zibwenzi zake koma sadzazipeza;

adzazifunafuna koma sadzazipeza.

Pamenepo iye adzati,

‘Ndibwerera kwa mwamuna wanga woyamba uja,

pakuti ndinali pabwino ndi iyeyo kusiyanitsa ndi pano.’

8Iye sanazindikire kuti ndine amene

ndinkamupatsa tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta.

Ndine amene ndinkamukhuthulira siliva ndi golide,

zimene ankapangira mafano a Baala.

9“Choncho Ine ndidzamulanda tirigu wanga pa nthawi yokolola,

ndi vinyo wanga watsopano pa nthawi yopsinya mphesa.

Ndidzamulanda ubweya ndi thonje langa,

zomwe akanaphimba nazo umaliseche wake.

10Motero tsopano ndidzaonetsa maliseche ake

pamaso pa zibwenzi zake;

palibe ndi mmodzi yemwe adzamupulumutse mʼmanja mwanga.

11Ndidzathetsa zikondwerero zake zonse:

zikondwerero zake za chaka ndi chaka, za mwezi watsopano,

za pa masiku a Sabata ndi maphwando ake onse a pa masiku okhazikitsidwa.

12Ndidzawononga mitengo yake ya mpesa ndi mitengo yake yamkuyu,

imene iye ankanena kuti inali malipiro ake ochokera kwa zibwenzi zake.

Ndidzayisandutsa chithukuluzi,

ndipo zirombo zakuthengo zidzadya zipatsozo.

13Ndidzamulanga chifukwa cha masiku

amene anafukiza lubani kwa Abaala;

anadzikongoletsa povala mphete ndi mikanda yamtengowapatali

ndipo anathamangira zibwenzi zake,

koma Ine anandiyiwala,”

akutero Yehova.

14“Koma tsopano ndidzamukopa mkaziyo;

ndidzapita naye ku chipululu

ndipo ndidzamuyankhula mwachikondi.

15Kumeneko ndidzamubwezera minda yake ya mpesa,

ndipo ndidzasandutsa Chigwa cha Akori kukhala khomo la chiyembekezo.

Kumeneko iye adzayimba nyimbo monga mʼmasiku a ubwana wake,

monga tsiku limene anatuluka ku Igupto.

16“Tsiku limeneli,” Yehova akuti,

“udzandiyitana kuti, ‘Amuna anga;’

sudzandiyitananso kuti, ‘Mbuye wanga.’

17Ndidzachotsa mayina a Abaala pakamwa pake;

sadzatchulanso mayina awo popemphera.

18Tsiku limenelo ndidzachita pangano

ndi zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga

ndiponso zolengedwa zokwawa pansi kuti ziyanjane ndi anthu anga.

Ndidzachotsa mʼdzikomo uta,

lupanga ndi zida zonse zankhondo,

kuti onse apumule mwamtendere.

19Ndidzakutomera kuti ukhale mkazi wanga mpaka muyaya;

ndidzakutomera mwachilungamo, mwaungwiro,

mwachikondi ndi mwachifundo.

20Ndidzakutomera mokhulupirika

ndipo udzadziwa Yehova.

21“Tsiku limenelo Ine ndidzayankha,”

akutero Yehova.

“Ndidzayankha mlengalenga pempho lake lofuna mitambo

ndipo mvula idzagwa pa dziko lapansi;

22ndipo nthaka idzamvera kupempha kwa tirigu,

vinyo ndi mafuta,

ndipo zidzamvera Yezireeli.

23Ndidzadzala Israeli mʼdziko kuti akhale wanga:

ndidzaonetsa chikondi changa kwa anthu amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Sakondedwa.’

Ndidzawawuza amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Si anthu anga,’ kuti, ‘Ndinu anthu wanga;’

ndipo adzanena kuti, ‘ndinu Mulungu wathu,’ ”