Hoseya 14 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Hoseya 14:1-9

Kulapa Kubweretsa Madalitso

1Iwe Israeli bwerera kwa Yehova Mulungu wako.

Machimo anu ndi amene akugwetsani!

2Bweretsani zopempha zanu

ndipo bwererani kwa Yehova.

Munene kwa Iye kuti,

“Tikhululukireni machimo athu onse

ndi kutilandira mokoma mtima,

kuti tithe kukuyamikani ndi mawu a pakamwa pathu.

3Asiriya sangatipulumutse;

ife sitidzakwera pa akavalo ankhondo,

sitidzanenanso kuti, ‘Milungu yathu’

kwa zimene manja athu omwe anazipanga,

pakuti ndinu amene mumachitira chifundo ana amasiye.”

4Ine ndidzachiza kusakhulupirika kwawo

ndipo ndidzawakonda mwaufulu

pakuti ndaleka kuwakwiyira.

5Ndidzakhala ngati mame kwa Israeli

Ndipo iye adzachita maluwa ngati kakombo.

Adzazika mizu yake pansi

ngati mkungudza wa ku Lebanoni;

6mphukira zake zidzakula.

Kukongola kwake kudzakhala ngati mtengo wa olivi,

kununkhira kwake ngati mkungudza wa ku Lebanoni.

7Anthu adzakhalanso mu mthunzi wake.

Iye adzakula bwino ngati tirigu.

Adzachita maluwa ngati mphesa

ndipo kutchuka kwake kudzakhala ngati vinyo wochokera ku Lebanoni.

8Efereimu adzati, “Ndidzachita nawonso chiyani mafano?

Ine ndidzamuyankha ndi kumusamalira.

Ine ndili ngati mtengo wa payini wobiriwira;

zipatso zako zimachokera kwa Ine.”

9Ndani ali ndi nzeru? Adzazindikire zinthu izi.

Ndani amene amamvetsa zinthu? Adzamvetse izi.

Njira za Yehova ndi zolungama;

anthu olungama amayenda mʼmenemo,

koma anthu owukira amapunthwamo.