Hoseya 10 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Hoseya 10:1-15

1Israeli anali mpesa wotambalala;

anabereka zipatso zambiri.

Pamene zipatso zawo zinanka zichuluka,

anawonjezera kumanga maguwa ansembe.

Pamene dziko lake linkatukuka,

anakongoletsa miyala yake yopatulika.

2Mtima wawo ndi wonyenga

ndipo tsopano ayenera kulangidwa chifukwa cha kulakwa kwawo.

Yehova adzagumula maguwa awo ansembe

ndi kuwononga miyala yawo yopatulika.

3Pamenepo anthuwo adzanena kuti, “Ife tilibe mfumu

chifukwa sitinaope Yehova.

Koma ngakhale tikanakhala ndi mfumu,

kodi mfumuyo ikanatichitira chiyani?”

4Mafumu amalonjeza zambiri,

amalumbira zabodza

pochita mapangano.

Kotero maweruzo amaphuka

ngati zitsamba zakupha mʼmunda umene walimidwa.

5Anthu amene amakhala mu Samariya akuchita mantha

chifukwa cha fano la mwana wangʼombe ku Beti-Aveni.

Anthu ake adzalirira fanolo,

chimodzimodzinso ansembe ake adamawo,

amene anakondwera ndi kukongola kwake,

chifukwa lachotsedwa pakati pawo ndi kupita ku ukapolo.

6Fanolo lidzatengedwa kupita ku Asiriya

ngati mphatso kwa mfumu yayikulu.

Efereimu adzachititsidwa manyazi

chifukwa cha mafano ake amitengo.

7Samariya ndi mfumu yake adzatengedwa kupita kutali

ngati kanthambi koyenda pa madzi.

8Malo opembedzerako mafano a ku Aveni adzawonongedwa.

Ili ndiye tchimo la Israeli.

Minga ndi mitungwi zidzamera

ndi kuphimba maguwa awo ansembe.

Kenaka anthu adzawuza mapiri kuti, “Tiphimbeni!”

ndipo adzawuza zitunda kuti, “Tigwereni!”

9“Iwe Israeli, wachimwa kuyambira mʼmasiku a Gibeya,

ndipo wakhala uli pomwepo.

Kodi nkhondo sinagonjetse anthu

ochita zoyipa ku Gibeya?

10Pamene ndifunire, ndidzalanga anthuwo;

mitundu ya anthu idzasonkhanitsidwa kudzalimbana nawo,

kuwayika mʼndende chifukwa cha uchimo wawo waukulu.

11Efereimu ndi mwana wangʼombe wamkazi wophunzitsidwa

amene amakonda kupuntha tirigu,

choncho Ine ndidzayika goli

mʼkhosi lake lokongolalo.

Ndidzasenzetsa Efereimu goli,

Yuda ayenera kulima,

ndipo Yakobo ayenera kutipula.

12Mufese nokha chilungamo

ndipo mudzakolola chipatso cha chikondi changa chosasinthika.

Ndipo tipulani munda wanu wosalimidwawo;

pakuti ino ndi nthawi yofunafuna Yehova,

mpaka Iye atabwera

kudzakugwetserani mivumbi ya chilungamo.

13Koma inu munadzala zolakwa,

mwakolola zoyipa;

mwadya chipatso cha chinyengo.

Chifukwa mumadalira mphamvu zanu

ndiponso ankhondo anu ochulukawo,

14phokoso lankhondo lidzamveka pakati pa anthu anga

kotero kuti malinga anu onse adzawonongeka,

monga momwe Salimani anawonongera Beti-Aribeli pa nthawi ya nkhondo;

pamene anapha amayi pamodzi ndi ana awo omwe.

15Momwemonso zidzakuchitikira, iwe Beteli

chifukwa kuyipa kwako ndi kwakukulu.

Tsiku limeneli likadzafika,

mfumu ya Israeli idzawonongedwa kwathunthu.