Hoseya 1 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Hoseya 1:1-11

1Awa ndi mawu amene Yehova anayankhula kwa Hoseya mwana wa Beeri pa nthawi ya ulamuliro wa Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda ndiponso pa nthawi ya ulamuliro wa Yeroboamu mwana wa Yowasi mfumu ya ku Israeli.

Mkazi wa Hoseya ndi Ana Ake

2Yehova atayamba kuyankhula kudzera mwa Hoseya, Yehova anati kwa Hoseyayo, “Pita kakwatire mkazi wachiwerewere ndipo ubereke naye ana mʼchiwerewere chake pakuti anthu a mʼdziko muno achimwa pochita chigololo choyipitsitsa, posiya Yehova.” 3Motero Hoseya anakwatira Gomeri mwana wamkazi wa Dibulaimu, ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna.

4Tsono Yehova anati kwa Hoseya, “Umutche dzina loti Yezireeli, pakuti ndili pafupi kulanga banja la Yehu chifukwa cha anthu amene anawapha ku Yezireeli ndipo ndidzathetsa ufumu wa Israeli. 5Tsiku limenelo ndidzathyola uta wa Israeli mʼchigwa cha Yezireeli.”

6Gomeri anakhala woyembekezeranso ndipo anabereka mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, “Umutche dzina loti ‘Sakondedwa’ pakuti sindidzaonetsanso chikondi changa pa nyumba ya Israeli, kuti ndingawakhululukire konse. 7Komatu ndidzaonetsa chikondi pa nyumba ya Yuda; ndipo ndidzawapulumutsa, osati ndi uta, lupanga kapena nkhondo, kapena akavalo ndi okwerapo ake, koma ine Yehova Mulungu wawo ndidzawapulumutsa.”

8Sakondedwa ataleka kuyamwa, Gomeri anabereka mwana wina wamwamuna. 9Pamenepo Yehova anati, “Umutche dzina loti Sianthuanga,” pakuti inu si ndinu anthu anga ndipo Ine si ndine Mulungu wanu.

10“Komabe Aisraeli adzachuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja umene sangathe kuwuyeza kapena kuwuwerenga. Pamalo omwe ananena kuti, ‘Sindinu anthu anga,’ pomweponso adzawatchula kuti ‘Ana a Mulungu wamoyo.’ 11Anthu a ku Yuda ndi anthu a ku Israeli adzasonkhananso pamodzi ndipo adzasankha mtsogoleri mmodzi ndi kutuluka mʼdzikomo, pakuti tsiku la Yezireeli lidzakhala lalikulu kwambiri.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

何西阿書 1:1-11

1烏西雅約坦亞哈斯希西迦猶大王,約阿施的兒子耶羅波安以色列王期間,耶和華將祂的話傳給備利的兒子何西阿

何西阿娶妓女為妻

2耶和華首次向何西阿說話時,對他說:「你去娶一個妓女為妻,和她生養兒女,因為這片土地上的人極其淫亂,背棄了耶和華。」 3於是,何西阿娶了滴拉音的女兒歌蜜為妻,她懷孕為他生了一個兒子。 4耶和華對何西阿說:「給他取名叫耶斯列1·4 耶斯列」意思是「上帝撒種」。此處指上帝要像撒種一樣驅散以色列人,但在1·11指上帝要賜福他們,就像撒種後獲得了大豐收。,因為再過不久,我就要因耶戶家在耶斯列的屠殺而懲罰他們,消滅以色列國。 5那時,我要在耶斯列平原折斷以色列的弓。」 6後來,歌蜜又懷孕生了一個女兒。耶和華對何西阿說:「給她取名叫羅·路哈瑪1·6 羅·路哈瑪」意思是「不蒙憐憫」。,因為我將不再憐憫以色列家,也不再赦免他們的罪。 7但我要憐憫猶大家,使他們依靠他們的上帝耶和華得到拯救,而不是依靠戰弓、刀劍、馬匹、騎兵和戰爭。」 8羅·路哈瑪斷奶後,歌蜜又懷孕生了一個兒子。 9耶和華說:「給他取名叫羅·阿米1·9 羅·阿米」意思是「不是我的子民」。,因為以色列人不再是我的子民,我也不再是他們的上帝。

以色列的復興

10「然而,以色列的人數必像海沙一樣量不盡、數不完。從前我在什麼地方對他們說『你們不是我的子民』,將來也要在那裡對他們說『你們是永活上帝的兒女』。 11那時,猶大人和以色列人將被聚集起來,為自己選立一位首領,從流亡之地返回故鄉,安居樂業。耶斯列的日子將是偉大的日子。