Habakuku 3 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Habakuku 3:1-19

Pemphero la Habakuku

1Pemphero la mneneri Habakuku potsata mayimbidwe a Sigionoti.

2Inu Yehova, ndamva za kutchuka kwanu;

Inu Yehova, ntchito zanu zandiopsa.

Muzichitenso masiku athu ano,

masiku athu ano zidziwike;

mu ukali wanu mukumbukire kuchita chifundo.

3Mulungu anabwera kuchokera ku Temani,

Woyerayo kuchokera ku Phiri la Parani.

Sela

Ulemerero wake unaphimba mlengalenga

ndipo dziko lapansi linadzaza ndi matamando ake.

4Kuwala kwa ulemerero wake kunali ngati kutuluka kwa dzuwa;

kunyezimira kunkatuluka mʼdzanja lake,

mʼmene anabisamo mphamvu zake.

5Patsogolo pake pankagwa mliri;

nthenda yoopsa inkagwa kumbuyo kwake.

6Iye anayimirira ndi kugwedeza dziko lapansi;

anayangʼana ndipo mitundu ya anthu inanjenjemera.

Mapiri okhazikika anagumuka

ndipo zitunda zakalekale zinatitimira.

Njira zake ndi zachikhalire.

7Ndinaona matenti a ku Kusani ali pa mavuto,

mokhala a ku Midiyani muli ululu waukulu.

8Inu Yehova, kodi munakwiyira mitsinje?

Kodi munakalipira timitsinje?

Kodi munapsera mtima nyanja

pamene munakwera pa akavalo anu

ndiponso magaleta anu achipulumutso?

9Munasolola uta wanu mʼchimake,

munayitanitsa mivi yambiri.

Sela

Munagawa dziko lapansi ndi mitsinje;

10mapiri anakuonani ndipo anagwedezeka.

Madzi amphamvu anasefukira;

nyanja yozama inakokoma

ndipo mafunde ake anakwera kwambiri.

11Dzuwa ndi mwezi zinayima chilili mlengalenga,

pa kungʼanima kwa mivi yanu yowulukayo,

pa kunyezimira kwa mkondo wanu.

12Munayendayenda mʼdziko lapansi muli ndi ukali,

ndipo munapondereza mitundu ya anthu muli ndi mkwiyo.

13Munapita kukalanditsa anthu anu,

kukapulumutsa wodzozedwa wanu.

Munakantha mtsogoleri wa dziko la anthu oyipa,

munawononga anthu ake onse.

Sela

14Ndi mkondo wake womwe munalasa mtsogoleri wake

pamene ankhondo ake anabwera mwamphamvu kudzatibalalitsa,

ankasangalala ngati kuti akudzawononga

osauka amene akubisala.

15Munapondaponda pa nyanja ndi akavalo anu,

kuvundula madzi amphamvu.

16Ndinamva ndipo mtima wanga unagunda kwambiri,

milomo yanga inanjenjemera pakumva phokosolo;

mafupa anga anaguluka,

ndipo mawondo anga anawombana.

Komabe ndikuyembekezera mofatsa,

tsiku la masautso limene lidzafike pa mtundu wa anthu umene ukutithira nkhondo.

17Ngakhale mtengo wa mkuyu usachite maluwa,

ndipo mipesa ikhale yopanda mphesa.

Ngakhale mitengo ya olivi isabereke zipatso,

ndipo mʼminda musatuluke kanthu.

Ngakhale nkhosa

ndi ngʼombe zithe mʼkhola,

18komabe ine ndidzakondwera mwa Yehova,

ndidzasangalala mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.

19Ambuye Yehova ndiye mphamvu yanga;

amalimbitsa miyendo yanga ngati ya mbawala yayikazi,

amandithandiza kukafika pamwamba pa phiri.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za nsambo.