Genesis 49 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 49:1-33

Yakobo Adalitsa Ana ake Aamuna

1Pambuyo pake Yakobo anayitanitsa ana ake aamuna nati: Sonkhanani pamodzi kuti ndikuwuzeni zimene zidzakuchitikireni mʼmasiku a mʼtsogolo.

2“Bwerani ndipo imvani mawu anga, inu ana a Yakobo;

mverani abambo anu Israeli.

3“Rubeni, ndiwe woyamba kubadwa;

mphamvu yanga ndiponso chizindikiro choyamba cha mphamvu zanga,

wopambana pa ulemerero ndi mphamvu.

4Wokokoma ngati madzi a chigumula, koma sudzakhalanso wopambana,

iwe unagona pa bedi la abambo ako,

ndithu unayipitsa bedi la mdzakazi wake.

5“Simeoni ndi Levi ndi pachibale pawo,

anachitira nkhanza anthu amene anachita nawo pangano.

6Iwe moyo wanga, usakhale nawo pa misonkhano yawo ya mseri,

kapena kugwirizana nawo mʼmabwalo awo,

pakuti anapha anthu mu mkwiyo wawo

ndipo anapundula ngʼombe zamphongo monga kunawakomera.

7Matemberero awagwere chifukwa cha mkwiyo wawo woopsa chonchi

ndi ukali wawo wankhanza choterewu!

Ine ndidzawabalalitsa mʼdziko la Yakobo

ndi kuwamwaza iwo mʼdziko la Israeli.

8“Yuda, ndiwe amene abale ako adzatamanda;

dzanja lako lidzagwira pa khosi pa adani ako;

abale ako adzakugwadira iwe.

9Yuda ali ngati mwana wa mkango;

umabwerera ku malo ako ndi zofunkha, mwana wanga.

Monga mkango, amadziwongola ndi kugona pansi,

ndipo ngati mkango waukazi, ndani angalimbe mtima kumudzutsa?

10Ndodo yaufumu sidzachoka mwa Yuda,

udzawupanirira ulamuliro motero kuti palibe amene adzawuchotse,

mpaka mwini wake weniweni atabwera

ndipo mitundu yonse ya anthu idzamumvera.

11Ndiye amene amamangirira bulu wake wamkazi kumtengo wa mpesa,

ndi mwana wa bulu ku nthambi ya mpesa wabwino.

Ndi iye amene amachapa zovala zake mu vinyo;

ndi mkanjo wake mu vinyo wofiira ngati magazi.

12Maso ake adzakhala akuda chifukwa cha vinyo,

mano ake woyera chifukwa cha mkaka.

13“Zebuloni adzakhala mʼmphepete mwa nyanja;

adzakhala pa dooko la sitima zapamadzi;

malire ake adzafika ku Sidoni.

14“Isakara ali ngati bulu wamphamvu

wogona pansi pakati pa makola.

15Ataona ubwino wake wa pamalo pake popumira

ndi kukongola kwa dziko lake,

iye anaweramutsa msana kuti anyamule katundu wake

ndipo anasanduka wogwira ntchito ya ukapolo.

16“Dani adzaweruza mwachilungamo anthu ake

monga limodzi mwa mafuko a anthu a mu Israeli.

17Dani adzakhala ngati njoka ya mʼmphepete mwa msewu,

songo yokhala mʼnjira

imene imaluma chidendene cha kavalo

kuti wokwerapoyo agwe chagada.

18“Ndikuyembekeza chipulumutso chanu Yehova.

19“Gadi adzachitidwa chiwembu ndi gulu la amaliwongo,

koma iye adzawathamangitsa.

20“Dziko la Aseri lidzabereka chakudya chokoma,

ndipo iye adzapereka chakudya kwa mafumu.

21“Nafutali ali ngati mbawala yayikazi

yokhala ndi ana okongola kwambiri.

22“Yosefe ali ngati mtengo wobereka zipatso,

mtengo wobereka zipatso pafupi ndi kasupe,

nthambi zake zimayanga pa chipupa cha mwala.

23Alenje a uta anamuchita chiwembu mwankhanza;

anamuthamangitsa ndi mauta awo.

24Koma uta wake sunagwedezeke,

ndi manja ake amphamvu aja analimbika,

chifukwa cha mphamvu za Mulungu Wamphamvu wa Yakobo,

chifukwa ali Mʼbusa ndi Thanthwe la Israeli.

25Chifukwa cha Mulungu wa makolo ako amene amakuthandiza;

chifukwa cha Mulungu Wamphamvu, amene amakudalitsa

ndi mvula yochokera kumwamba,

ndi madzi otumphuka pansi pa nthaka,

ndipo amakudalitsa pokupatsa ana ambiri ndi ngʼombe zambiri.

26Madalitso a kholo lako ndi amphamvu kuposa

madalitso a mapiri akale

oposa zabwino za ku zitunda zamgonagona.

Zonse izi zikhale pamutu pa Yosefe,

pa mphumi pa wopatulika uja amene anapatulidwa pakati pa abale ake.

27“Benjamini ali ngati mʼmbulu wolusa;

umene mmawa umapha ndi kudya zofunkha,

ndipo madzulo umagawa zofunkhazo,”

28Onse awa ndi mafuko khumi ndi awiri a Israeli, ndipo zimenezi ndi zomwe abambo awo ananena pamene anawadalitsa, kuwapatsa aliyense madalitso ake womuyenera iye.

Kumwalira kwa Yakobo

29Kenaka Yakobo analamula ana ake nati: “Ine ndatsala pangʼono kufa. Tsono mukandiyike pamodzi ndi makolo anga mʼphanga la mʼmunda wa Efroni Mhiti. 30Ili ndi phanga la mʼmunda wa Makipela, pafupi ndi Mamre mʼdziko la Kanaani. Abrahamu anagula phangalo pamodzi ndi munda womwe kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda. 31Kumeneko kunayikidwa Abrahamu ndi mkazi wake Sara, Isake ndi mkazi wake Rebeka ndipo ndinayikakonso Leya. 32Munda ndi manda amene ali mʼmenemo zinagulidwa kwa Ahiti.”

33Yakobo atamaliza kupereka malangizo kwa ana ake, anabwezera miyendo yake pa bedi, namwalira ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

创世记 49:1-33

雅各的预言

1雅各把他的儿子们都叫来,对他们说:“你们到我身边来,我要把你们将来的遭遇告诉你们。

2雅各的儿子们啊,

你们都来听,

听你们父亲以色列的话。

3吕便啊,你是我的长子,

是我年轻力壮时生的,

比众弟兄更有尊荣和力量。

4可是,你必不再居首位,

因为你放纵情欲,

如沸腾不止的水,

你上了你父亲的床,

玷污了我的榻。

5西缅利未串通一气,

依仗刀剑,残暴不仁。

6我的灵啊,不要与他们同谋。

我的心啊,不要与他们联合。

他们泄愤杀人,

随意砍断牛腿的筋。

7他们狂暴凶残,该受咒诅!

我要使他们分散在雅各的子孙中,

散居在以色列各地。

8犹大啊,你的兄弟们必赞美你,

你必制服你的仇敌,

你父亲的儿子必向你下拜。

9我儿犹大是头小狮子,

他猎食回来,躺卧如雄狮,

蹲伏如母狮,谁敢惊扰他?

10王权必不离犹大

御杖必伴他左右,

直到那位执掌王权的来到,

万民都必归顺他。

11“他把小驴拴在葡萄树旁,

把驴驹拴在上好的葡萄树旁;

他在葡萄酒中洗衣服,

在葡萄汁中洗外袍。

12他的眼睛比酒乌润,

牙齿比奶洁白。

13西布伦必安居在海滨,

成为泊船的港口,

他的疆界必伸展到西顿

14以萨迦是头壮驴,

卧在羊圈中。

15他见那地方好作安身之处,

地土肥美,就垂下肩头,

做了奴隶。

16必治理他的人民,

以色列的一个支派。

17他必成为路边的蛇,

道旁的毒蛇,

咬伤马蹄,使骑马的人坠落。

18“耶和华啊,

我切切等候你的拯救。

19迦得必被强盗劫掠,

他却要反败为胜追赶他们。

20亚设必有丰美的出产和供君王享用的美味。

21拿弗他利是头自由的母鹿,

养育美丽的小鹿49:21 养育美丽的小鹿”或译“口出佳美之言”。

22约瑟是多结果子的枝条,

长在水泉旁,

他的枝条探出墙外。

23弓箭手凶猛地攻击他,

恶狠狠地射他。

24但他手持强弓,

双臂稳健有力,

因为雅各的大能者——以色列的牧者和磐石帮助他。

25你父亲的上帝必帮助你,

全能者必赐你天上的恩泽、

地上的百福,

使你子孙兴旺、牛羊满圈。

26你父亲的祝福高过亘古永存的峰峦,

多如绵延无尽的群山,

愿这一切的祝福都临到约瑟头上,

临到这超越众弟兄的人身上。

27便雅悯是匹贪婪的狼,

早晨吞吃猎物,

晚上瓜分战利品。”

28以上是以色列的十二支派,他们的父亲按着他们不同的福分给他们祝福。 29雅各又嘱咐他们说:“我要离世了,你们要把我葬在以弗仑田间的洞里,让我与祖先在一起。 30那洞穴在迦南幔利附近的麦比拉田间,是亚伯拉罕以弗仑买来作坟地的。 31亚伯拉罕和他的妻子撒拉以撒和他的妻子利百加都葬在那里,我把利亚也葬在了那里。 32那块田和田间的洞穴是向人买的。” 33雅各嘱咐完众子,在床上躺下,咽了气,去他祖先那里了。