Genesis 48 – CCL & HTB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 48:1-22

Manase ndi Efereimu

1Patapita kanthawi Yosefe anawuzidwa kuti, “Abambo ako akudwala.” Choncho anatenga ana ake awiri aja Manase ndi Efereimu ndi kupita nawo kwa Yakobo. 2Yakobo atawuzidwa kuti, “Mwana wanu Yosefe wabwera,” Israeli anadzilimbitsa nadzuka kukhala tsonga pa bedi pake.

3Yakobo anati kwa Yosefe, “Mulungu Wamphamvuzonse anandionekera ku Luzi mʼdziko la Kanaani, ndipo anandidalitsa, 4nati kwa ine, ‘Ndidzakupatsa ana ambiri ndipo zidzukulu zako zidzasanduka mitundu yambiri ya anthu. Ndidzapereka dziko ili kwa zidzukulu zako zobwera pambuyo pako kuti likhale lawo mpaka muyaya.’

5“Tsopano ana ako aamuna awiri amene anabadwa ine ndisanabwere kuno adzakhala ana anga. Efereimu ndi Manase adzakhala anga monga mmene alili Rubeni ndi Simeoni. 6Koma amene ati adzabadwe pambuyo pa iwowa adzakhala ako ndipo cholowa chawo chidzadziwika ndi mayina a abale awo. 7Pamene ndimabwerera kuchoka ku Parani, mwachisoni Rakele, amayi ako anamwalira mʼdziko la Kanaani, tikanali mʼnjira, mtunda wokafika ku Efurata ukanalipo. Ndipo ndinawayika kumeneko mʼmphepete mwa msewu wa ku Efurata” (amene ndi Betelehemu).

8Israeli ataona ana a Yosefe anafunsa kuti, “Anyamatawa ndi a yani?”

9Yosefe anati kwa abambo ake, “Awa ndi ana anga amene Mulungu wandipatsa kuno.”

Ndipo Israeli anati, “Bwera nawo kuno kuti ndiwadalitse.”

10Koma maso a Israeli anali ofowoka chifukwa cha kukalamba moti sankaona nʼkomwe. Tsono Yosefe anabwera nawo ana ake aja pafupi ndi abambo ake ndipo abambo ake anawapsompsona nawakumbatira.

11Israeli anati kwa Yosefe, “Ine sindinali kuyembekeza kuti nʼkudzaonanso nkhope yako, ndipo tsopano Mulungu wandilola kuti ndionenso ngakhale ana ako.”

12Tsono Yosefe anawachotsa ana aja pa mawondo a Israeli ndipo anamuweramira nkhope pansi. 13Yosefe anawagwira ana onse awiri padzanja, Efereimu ku dzanja lake lamanja kulunjika dzanja lamanzere la Israeli ndipo Manase ku dzanja lamanzere kulunjikitsa dzanja lamanja la Israeli, ndipo anawayandikiza kwa Yakobo. 14Koma Israeli anapinganitsa mikono motero kuti anayika dzanja lake lamanja pamutu pa Efereimu ngakhale kuti iyeyo anali wamngʼono ndi dzanja lake lakumanzere analisanjika pamutu pa Manase ngakhale kuti iyeyu ndiye anali mwana woyamba.

15Kenaka anadalitsa Yosefe nati,

“Mulungu amene makolo anga

Abrahamu ndi Isake anamutumikira,

Mulungu amene wakhala ali mʼbusa wanga

moyo wanga wonse kufikira lero,

16mngelo amene wandipulumutsa ine ku zovuta zonse,

ameneyo adalitse anyamata awa.

Kudzera mwa iwowa

dzina langa ndi mayina a makolo anga, Abrahamu ndi Isake, adzamveka.

Iwowa adzakhala ndi ana ambiri nadzasanduka mtundu waukulu

pa dziko lapansi.”

17Yosefe ataona kuti abambo ake ayika dzanja lamanja pa Efereimu, sanakondwere. Choncho anagwira dzanja la abambo ake kuti alichotse pamutu pa Efereimu ndi kuliyika pamutu pa Manase, 18nati kwa abambo ake, “Ayi, abambo anga, uyu ndiye woyamba kubadwa, ikani dzanja lanu lamanja pamutu pake.”

19Koma abambo ake anakana nati, “Ndikudziwa, mwana wanga, ndikudziwa. Adzukulu a iyeyunso adzakhala mtundu waukulu. Komabe mʼbale wake wamngʼonoyu adzakhala wamkulu kuposa iye, ndipo zidzukulu zake zidzakhala mitundu yayikulu ya anthu.” 20Tsono iye anawadalitsa tsiku limenelo nati,

“Aisraeli adzagwiritsa ntchito dzina lanu podalitsa nadzati:

Mulungu akudalitseni monga Efereimu ndi Manase.”

Choncho anayika Efereimu patsogolo pa Manase.

21Kenaka Israeli anati kwa Yosefe, “Ine ndatsala pangʼono kufa, koma Mulungu adzakhala ndipo adzakutenganinso kubwerera nanu ku dziko la makolo anu. 22Ndiponso iwe wekha ndikupatsa moposera abale ako, malo woonjezera, Sekemu, malo amene ndinalanda kwa Aamori ndi lupanga ndi uta wanga.”

Het Boek

Genesis 48:1-22

Jakob zegent de zonen van Jozef

1Op een dag, niet lang hierna, hoorde Jozef dat zijn vader snel achteruit ging. Samen met zijn twee zonen, Manasse en Efraïm, ging hij hem bezoeken.

2Toen Jakob hoorde dat Jozef er was, verzamelde hij al zijn krachten en ging rechtop in bed zitten om hem te begroeten. 3-4 Hij zei tegen Jozef: ‘God, de Almachtige, verscheen aan mij bij Luz in het land Kanaän. Hij zegende mij en zei: “Ik zal u tot een groot volk maken en het land Kanaän aan de kinderen van uw kinderen geven, als een eeuwig bezit.” 5Wat je twee zonen betreft, Efraïm en Manasse, die hier in Egypte zijn geboren voordat ik aankwam, ik neem ze aan als mijn eigen kinderen en zij zullen van mij erven net als Ruben en Simeon. 6Maar alle andere kinderen die je nog zult krijgen, zullen van jou zijn en in Efraïms en Manasses erfenis van jou delen. 7Dit doe ik omdat je moeder Rachel stierf, toen ik uit Paddan-Aram kwam. We waren vlakbij Efrat en ik heb haar langs de weg naar Bethlehem begraven.’

8Toen keek Israël naar Manasse en Efraïm. ‘Zijn dat je zonen?’ vroeg hij. 9‘Ja,’ antwoordde Jozef, ‘dit zijn de zonen die God mij hier in Egypte heeft gegeven.’ 10Israël zei: ‘Breng ze hier bij mij, dan zal ik ze zegenen.’ Israël was op zijn hoge leeftijd half blind en kon nauwelijks zien. Jozef bracht zijn zonen vlakbij hem en hij kuste en omhelsde hen. 11Israël zei tegen Jozef: ‘Ik had niet gedacht, dat ik jou ooit zou terugzien, maar nu heeft God mij zelfs jouw kinderen laten zien.’ 12-13 Jozef nam zijn zonen bij de hand, boog diep voor zijn vader en leidde hen naar hun grootvaders knieën. Efraïm aan Israëls linkerhand en Manasse aan zijn rechterhand. 14Maar Israël kruiste zijn armen en legde zijn handen op de hoofden van de jonge mannen. Zo kwam zijn rechterhand te liggen op het hoofd van Efraïm, de jongste van de twee, en zijn linkerhand op het hoofd van Manasse, de oudste. Hij deed dit met opzet.

15Toen zegende hij Jozef met de woorden: ‘Moge God, de God van mijn voorouders Abraham en Isaak, de God die mij mijn hele leven als een herder heeft geleid, deze mannen zegenen. 16Hij is de Engel die mij in moeilijke tijden altijd heeft geholpen. Mogen Jozefs zonen de namen van mij en van mijn voorouders Abraham en Isaak eer aandoen en mogen zij tot een groot volk uitgroeien.’

17Maar Jozef vond het onjuist dat zijn vader zijn rechterhand op Efraïms hoofd had gelegd. Hij tilde de hand op om hem op Manasses hoofd te leggen. 18‘Vader,’ zei hij, ‘u hebt uw rechterhand op het verkeerde hoofd! Deze hier is de oudste. Leg uw rechterhand toch op zijn hoofd.’ 19Maar zijn vader weigerde. ‘Ik weet wat ik doe, mijn zoon,’ zei hij. ‘Manasse zal ook uitgroeien tot een groot volk, maar zijn jongere broer zal nog groter worden.’ 20Zo zegende Jakob de jongens die dag met de woorden: ‘Moge het volk van Israël elkaar zegenen door te zeggen: “God make u als Efraïm en Manasse”.’ (Let erop dat hij Efraïm vóór Manasse noemt). 21Toen zei Israël tegen Jozef: ‘Ik ga spoedig sterven, maar God zal met je zijn en je terugbrengen in Kanaän, het land van je voorouders. 22En ik heb jou het land van Sichem toegedacht, in plaats van je broers, als deel van het land dat ik met het zwaard en de boog op de Amorieten heb veroverd.’