Genesis 46 – CCL & JCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 46:1-34

Yakobo Apita ku Igupto

1Israeli anasonkhanitsa zonse anali nazo napita ku Beeriseba kukapereka nsembe kwa Mulungu wa abambo ake Isake.

2Ndipo Mulungu anayankhula ndi Israeli mʼmasomphenya usiku nati, “Yakobo! Yakobo!”

Iye anayankha, “Ee, Ambuye.”

3Mulungu anati, “Ine ndine Mulungu. Mulungu wa abambo ako. Usachite mantha kupita ku Igupto, pakuti ndidzachulukitsa zidzukulu zako kumeneko moti zidzakhala mtundu waukulu. 4Ine ndidzapita ku Igupto pamodzi ndi iwe ndipo mosakayika konse zidzukulu zako ndidzazibweretsa konkuno. Yosefe adzakhalapo pa nthawi yako yomwalira.”

5Yakobo anachoka ku Beeriseba, ndipo ana ake anakweza abambo awo, ana awo, pamodzi ndi akazi awo pa ngolo zimene Farao anatumiza kuti adzakwerepo. 6Iwo anatenganso ziweto zawo ndi katundu wawo amene anali naye ku Kanaani, ndipo Yakobo pamodzi ndi ana ndi zidzukulu zake anapita ku Igupto. 7Ndiye kuti popita ku Igupto Yakobo anatenga ana aamuna, zidzukulu zazimuna, ana aakazi ndi zidzukulu zazikazi.

8Nawa ana a Israeli (ndiye kuti Yakobo ndi ana ake) amene anapita ku Igupto:

Rubeni mwana woyamba wa Yakobo.

9Ana aamuna a Rubeni ndi awa:

Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi.

10Ana aamuna a Simeoni ndi awa:

Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shaulo amene mayi wake anali wa ku Kanaani.

11Ana aamuna a Levi ndi awa:

Geresoni, Kohati ndi Merari.

12Ana aamuna a Yuda ndi awa:

Eri, Onani, Sela, Perezi ndi Zera. Koma Eri ndi Onani anamwalira mʼdziko la Kanaani.

Ana a Perezi anali

Hezironi ndi Hamuli.

13Ana aamuna a Isakara ndi awa:

Tola, Puwa, Yobi ndi Simironi.

14Ana aamuna a Zebuloni ndi awa:

Seredi, Eloni ndi Yahaleeli.

15Amenewa ndi ana aamuna a Leya amene anamubalira Yakobo ku Padanaramu. Panali mwana wamkazi dzina lake Dina. Ana onse analipo 33.

16Ana aamuna a Gadi ndi awa:

Zifioni, Hagi, Suni, Eziboni, Eri, Arodi ndi Areli.

17Ana aamuna a Aseri ndi awa:

Imuna, Isiva, Isivi, Beriya

ndi Sera mlongo wawo.

Ana aamuna a Beriya ndi awa:

Heberi ndi Malikieli.

18Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa Zilipa amene Labani anapereka kwa mwana wake, Leya. Onse pamodzi analipo 16.

19Ana aamuna a Rakele mkazi wa Yakobo anali:

Yosefe ndi Benjamini. 20Ku Igupto, Asenati mwana wa Potifara wansembe wa Oni, anamuberekera Yosefe ana awa: Manase ndi Efereimu.

21Ana aamuna a Benjamini ndi awa:

Bela, Bekeri, Asibeli, Gera, Naamani, Ehi, Rosi, Mupimu, Hupimu ndi Aridi.

22Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa mkazi wake Rakele. Onse analipo khumi ndi anayi.

23Mwana wa mwamuna wa Dani anali:

Husimu.

24Ana aamuna a Nafutali ndi awa:

Yahazeeli, Guni, Yezeri ndi Silemu.

25Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa Biliha amene Labani anapereka kwa mwana wake Rakele. Onse pamodzi analipo asanu ndi awiri.

26Onse amene anapita ndi Yakobo (iwo amene anali akeake, osawerengera akazi a ana ake), analipo 66. 27Pophatikiza ana awiri a Yosefe obadwira ku Igupto, anthu a pa banja la Yakobo amene anapita ku Igupto, onse pamodzi analipo 70.

28Tsopano Yakobo anatumiza Yuda kwa Yosefe kukamupempha kuti akakumane naye ku Goseni. Iwo atafika ku chigawo cha Goseni, 29Yosefe anakonza galeta nakwerapo ndi kupita ku Goseni kukakumana ndi abambo ake, Israeli. Yosefe atangofika pamaso pa abambo ake, anawakumbatira nalira kwa nthawi yayitali.

30Israeli anati kwa Yosefe, “Tsopano ndikhoza kumwalira poti ndaona nkhope yako kuti ukanali ndi moyo.”

31Ndipo Yosefe anati kwa abale ake pamodzi ndi a pa banja la abambo ake, “Ndipita kwa Farao ndipo ndikamuwuza kuti, ‘Abale anga pamodzi ndi onse a mʼnyumba ya abambo anga amene amakhala mʼdziko la Kanaani abwera kuno kwa ine. 32Anthuwa ndi abusa; amaweta ziweto zawo ndipo abwera ndi nkhosa ndi ngʼombe zawo, pamodzi ndi antchito awo.’ 33Tsono Farao akakuyitanani nakufunsani kuti, ‘Kodi mumagwira ntchito yanji?’ 34Muyankhe kuti, ‘Ife, bwana ndife oweta ziweto kuyambira ubwana wathu mpaka tsopano. Takhala tikuweta ziweto monga mmene ankachitira makolo athu.’ Mukadzayankha choncho, ndiye kuti mudzakhala mʼdziko la Goseni chifukwa anthu a ku Igupto amanyansidwa nawo anthu oweta ziweto.”

Japanese Contemporary Bible

創世記 46:1-34

46

ヤコブ、エジプトへ

1イスラエル(ヤコブ)は彼に属するすべてのものとともに出発し、ベエル・シェバまで来ると、そこで父イサクの神にいけにえをささげました。 2やがて夜になり、幻の中で神の語りかける声がありました。

「ヤコブ、ヤコブ。」

「はい。」

3-4「わたしは神、あなたの父の神だ。エジプトへ行くのを恐れてはならない。大きな国になるよう、あなたを守ろう。わたしもいっしょにエジプトへ下り、時がきたら、あなたの子孫を再びここに連れ帰る。あなたはエジプトで、ヨセフに看取られながら死ぬだろう。」

5それからヤコブはベエル・シェバを発ちました。息子たちはヤコブを、エジプトの王からもらった荷馬車に乗せました。女性や子どもたちもいっしょです。 6また、家畜と、カナンの地で手に入れた全財産も持って行きました。ヤコブをはじめ、 7息子、娘、孫と、一族こぞってエジプトへ移住したのです。

8-14ヤコブといっしょにエジプトに行った息子と孫は、次のとおりです。

長男ルベンとその息子エノク、パル、ヘツロン、カルミ。シメオンとその息子エムエル、ヤミン、オハデ、ヤキン、ツォハル、それから、カナン人の母親を持つサウル。レビとその息子ゲルション、ケハテ、メラリ。ユダとその息子エル、オナン、シェラ、ペレツ、ゼラフ〔エルとオナンはエジプトへ行く前にカナンで死んだ〕。ペレツの息子ヘツロンとハムル。イッサカルとその息子トラ、プワ、ヨブ、シムロン。ゼブルンとその息子セレデ、エロン、ヤフレエル。 15以上は、パダン・アラムでヤコブとレアの間に生まれた息子とその孫で、娘ディナを除いて総勢三十三人でした。

16-17このほかに、ガドとその息子ツィフヨン、ハギ、シュニ、エツボン、エリ、アロディ、アルエリ。アシェルとその息子イムナ、イシュワ、イシュビ、ベリア、妹セラフ。ベリアの息子ヘベル、マルキエル。 18以上十六人は、ラバンが上の娘レアに与えた奴隷ジルパとヤコブの間に生まれた息子と孫です。

19-22この一族には、ヤコブとラケルに生まれた息子と孫、合わせて十四名も含まれます。ヨセフとベニヤミン。エジプトで生まれたヨセフの息子はマナセとエフライム〔母親はヘリオポリスの祭司ポティ・フェラの娘アセナテ〕。ベニヤミンの息子はベラ、ベケル、アシュベル、ゲラ、ナアマン、エヒ、ロシュ、ムピム、フピム、アルデ。

23-25さらに、ラバンが下の娘ラケルに与えた奴隷ビルハとヤコブの間に生まれた息子と孫、合わせて七人も含まれます。ダンとその息子フシム。ナフタリとその息子ヤフツェエル、グニ、エツェル、シレム。

26エジプトへ下ったヤコブの子孫は、ヤコブの息子たちの妻を除いて総勢六十六名でした。 27ヨセフとその二人の息子、それにヤコブ自身を加えると、エジプトでのヤコブの一族は七十名になります。

28ヤコブはユダを先に送り、まもなくゴシェンに到着すると、ヨセフに伝えました。やがて、一行はゴシェンに着きました。 29ヨセフは馬車で駆けつけ、父親を出迎えました。二人はしっかり抱き合ってただ泣くばかりです。 30「こうしておまえの顔を見られるとは、夢にも思わなかった。無事でほんとうによかった。もう思い残すことはない。これで安心して死ねる。」イスラエルは涙ながらに言いました。

31ヨセフは彼らに言いました。「これから王のところへ上がります。一族の者がカナンから到着したと報告しなければなりませんから。 32その時、『一族の者はみな、羊飼いで、羊や牛の群れを連れ、全財産を携えて来ました』と申し上げておきます。 33あとで王のお召しがあり、職業は何かと聞かれたら、 34『先祖代々の羊飼いで、私どもも若い時からずっと羊を飼っております』と答えてください。そう申し上げれば、このゴシェンの地に住まわせてもらえるでしょう。エジプト人は羊飼いを軽蔑し、嫌っていますから、いっしょには住まないのです。」