Genesis 44 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 44:1-34

Chikho Chasiliva Mʼthumba la Benjamini

1Pambuyo pake Yosefe analamulira wantchito wa mʼnyumba mwake kuti, “Adzazire chakudya anthuwa mʼmatumba mwawo monga mmene anganyamulire, ndipo uwayikire ndalama zawo pakamwa pa matumba awowo. 2Tsono uyike chikho changa cha siliva chija, pakamwa pa thumba la wamngʼono kwambiriyu pamodzi ndi ndalama zake za chakudya” Ndipo iye anachita monga Yosefe ananenera.

3Mmawa kutacha anthu aja analoledwa kuti apite ndi abulu awo. 4Atangotuluka mu mzinda muja, koma asanapite patali, Yosefe anati kwa wantchito wake, “Nyamuka atsatire anthu aja msanga. Ndipo ukawapeza, uwafunse kuti, ‘Bwanji mwabwezera zoyipa ndi zabwino? 5Mwaberanji chikho chimene mbuye wanga amamweramo ndi kugwiritsa ntchito akafuna kuwombeza? Chimene mwachitachi ndi chinthu choyipa.’ ”

6Wantchito uja atawapeza ananena mawu anawuzidwa aja. 7Koma iwo anati kwa iye, “Kodi mbuye wanga mukuneneranji zimenezi? Sizingatheke ndi pangʼono pomwe kuti antchito anufe nʼkuchita zoterozo ayi! 8Paja ife pobwera kuchokera ku Kanaani tinatenga ndalama kubwezera zimene tinazipeza mʼmatumba mwathu. Ndiye pali chifukwa chanji kuti tikabe siliva kapena golide mʼnyumba mwa mbuye wanu? 9Ngati wantchito wanu wina pano atapezeka nacho chikhocho, ameneyo aphedwe ndipo ena tonsefe tidzakhala akapolo anu, mbuye wathu.”

10Iye anati, “Chabwino, tsono zikhale monga mwaneneramu. Komatu aliyense amene angapezeke nacho chikhocho adzakhala kapolo wanga, ndipo ena nonsenu muzipita mwaufulu.”

11Tsono onse anafulumira kutsitsa pansi aliyense thumba lake ndi kulitsekula. 12Kenaka anayamba kufufuza, kuyambira pa wamkulu mpaka pa wamngʼono. Ndipo chikhocho chinapezeka mʼthumba mwa Benjamini. 13Apo onse anangʼamba zovala zawo ndi chisoni. Ndipo anasenzetsa abulu katundu wawo nabwerera ku mzinda konkuja.

14Pamene Yuda ndi abale ake ankafika ku nyumba kwa Yosefe nʼkuti Yosefe akanali komweko. Ndipo anadzigwetsa pansi pamaso pake. 15Yosefe anafunsa kuti, “Nʼchiyani mwachitachi? Kodi simudziwa kuti munthu ngati ine ndikhoza kuona zinthu mwakuwombeza?”

16Yuda anayankha, “Kodi tinganenenji kwa mbuye wanga? Tinena chiyani? Tingadzilungamitse bwanji? Mulungu waulula kulakwa kwa antchito anu. Ndipo tsopano ndife akapolo a mbuye wanga, ife tonse pamodzi ndi amene wapezeka ndi chikhocho.”

17Koma Yosefe anati, “Sindingachite choncho ayi! Yekhayo amene wapezeka ndi chikhocho ndi amene akhale kapolo wanga. Ena nonsenu, bwererani kwa abambo anu mu mtendere.”

18Ndipo Yuda anamuyandikira iye nati, “Chonde mbuye wanga mulole kapolo wanune ndinene mawu pangʼono kwa mbuye wanga. Musandipsere mtima, kapolo wanune, popeza inu muli ngati Farao yemwe. 19Mbuye wanga munafunsa akapolo anufe kuti, ‘Kodi muli ndi abambo anu kapena mʼbale wanu?’ 20Ndipo ife tinayankha, ‘Inde mbuye wathu, ife tili ndi abambo athu wokalamba, ndipo pali mwana wamwamuna wamngʼono amene anabadwa abambo athu atakalamba kale. Mʼbale wake anafa ndipo ndi yekhayo mʼmimba mwa amayi ake amene watsala ndipo abambo ake amamukonda.’

21“Ndipo inu munatiwuza kuti, ‘Mubwere naye kwa ine kuti ndidzamuone ndekha.’ 22Ife tinati, ‘Mbuye wathu, mnyamatayo sangasiye abambo ake, akawasiya ndiye kuti abambo akewo adzafa.’ 23Koma inu munatichenjeza kuti, ‘Pokhapokha mutabwera naye mʼbale wanu wamngʼono kwambiri, simudzandionanso.’ 24Ndiye pamene tinafika kwa kapolo wanu, abambo athu tinawawuza zonse zimene munanena.

25“Abambo athu anatiwuza kuti, ‘Pitaninso mukagule kachakudya pangʼono.’ 26Koma tinati, ‘Sitingathe kupitanso. Sitingapite pokhapokha mngʼono wathuyu apite nafe chifukwa munthu uja anati sitingaonane naye ngati mngʼono wathuyu sakhala nafe.’

27“Koma kapolo wanu, abambo athu anatiwuza kuti, ‘Inu mukudziwa kuti mkazi wanga anandiberekera ana aamuna awiri. 28Mmodzi wa iwo anandisiya. Ine ndimati anadyedwa ndi chirombo popeza sindinamuonenso mpaka lero. 29Tsopano mukanditengeranso uyu, nakaphedwa mu njira ndiye kuti mudzandikankhira ku manda ndi chisoni.’

30“Tsono ngati tizibwerera kwa mtumiki wanu, abambo athu popanda mnyamatayu, amene moyo wa abambo ake uli pa iyeyu, 31ndipo akakaona kuti mnyamatayu palibe, basi akafa. Ife tidzakhala ngati takankhira abambo athu ku manda ndi chisoni. 32Ndiponsotu ine ndinadzipereka kwa abambo anga kukhala chikole chotsimikiza kuti mnyamatayu ndidzamuteteza, ndipo ndinati, ‘Ngati sindibwerera naye mnyamatayu kwa inu, ndiye kuti ndidzakhala wochimwira inu abambo anga moyo wanga wonse.’

33“Tsono, chonde mulole kuti ine kapolo wanu nditsalire kuno kukhala kapolo wa mbuye wathu mʼmalo mwa mnyamatayu. Koma iye apite pamodzi ndi abale akewa. 34Ndingabwerere bwanji kwa abambo anga ngati sindingapite ndi mnyamatayu? Ayi! Sindifuna kukaona tsoka limene lingakagwere abambo anga.”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

创世记 44:1-34

约瑟试验弟兄

1约瑟吩咐管家说:“给他们的口袋装满粮食,他们能带多少就装多少,把各人的钱放回他们的口袋中, 2再把我的银杯和买粮的钱一起放在最小的兄弟的口袋中。”管家一一办妥了。

3第二天清早,他们就牵着驴离开了。 4他们出城不久,约瑟对管家说:“你快去追他们,追上了就对他们说,‘你们为什么以恶报善? 5为什么偷我主人用来喝酒和占卜的银杯?你们这是作恶!’”

6于是,管家追上他们,按约瑟的话问他们。 7他们回答说:“我主为什么这样说?我们绝不会做这种事。 8你看,我们把上次在口袋里发现的钱都从迦南带回来还你了,又怎么会偷你主人家的金银呢? 9你若在仆人中任何人身上搜到银杯,他就要死!我们也要做我主的奴仆。”

10管家说:“好,就照你们的话做吧!银杯从谁那里搜出来,谁就做我的奴仆,其他人都没有罪。” 11于是,他们急忙把口袋卸到地上打开。 12管家就从最年长的开始搜查,最后在便雅悯的口袋里搜出了银杯。 13他们伤心地撕裂衣服,把东西放回驴背上,返回城里。

14犹大和他兄弟们回到约瑟家时,约瑟还在那里,他们就俯伏在他面前。 15约瑟对他们说:“你们做的是什么事?难道你们不知道像我这样的人是懂得占卜的吗?” 16犹大说:“我们能对我主说什么呢?我们还有什么话可说呢?我们如何洗脱罪名呢?上帝既然查出你仆人们的罪,我们跟那个被发现有银杯的弟弟一起做我主的奴仆吧!” 17约瑟回答说:“不!我决不会这样做。从谁那里搜出了银杯,谁就做我的奴仆,其他人平安地回去见你们的父亲吧。”

犹大求情

18犹大近前来对他说:“我主啊,你就像法老一样,求你容仆人说一句话,不要向仆人发怒。 19我主曾经问仆人们是否有父亲和弟兄, 20我们对我主说,‘我们有年迈的老父,他在晚年得了一个儿子,这孩子的哥哥已经死了,他母亲只剩下他这一个儿子,他父亲很疼爱他。’ 21你吩咐仆人们把弟弟带来给你亲眼看看, 22我们对我主说,‘这孩子不能离开他父亲,他若离开,他父亲一定会死。’ 23可是,你说如果仆人们不把弟弟带来,就不得再见你。 24我们回到你仆人——我们的父亲那里,把我主的话告诉了他。

25“后来,他又吩咐仆人们回来买粮, 26我们告诉他,我们不能来,只有我们的弟弟同来,我们才能来。否则,我们不能见你的面。 27我父亲就对我们说,‘你们应该知道,我妻子给我生了两个儿子。 28其中一个离开了我,我想他一定被野兽撕碎了,我再没有见过他。 29要是你们把他的弟弟也带走,遇上什么意外的话,你们会使我这白发苍苍的老人凄凄惨惨地进坟墓。’

30“我们父亲的命与这孩子的命紧密相连,倘若我没有把这孩子带回到你仆人——我父亲身边, 31他一看这孩子不在,一定会死。仆人们会使自己白发苍苍的父亲凄凄惨惨地进坟墓。 32仆人曾经向父亲保证这孩子的安全,说我若不把这孩子带回他身边,情愿一生担罪。 33现在求你准许仆人代替这孩子做你的奴仆,让他跟他哥哥们回去吧。 34这孩子不和我一同回去,我如何见我父亲呢?我不愿看到灾难临到我父亲。”