Genesis 40 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 40:1-23

Yosefe Amasulira Maloto a Amʼndende Anzake

1Patapita nthawi, woperekera zakumwa ndi wopanga buledi a ku nyumba kwa mfumu ya ku Igupto analakwira mbuye wawoyo. 2Farao anapsa mtima ndi akuluakulu awiriwa, 3ndipo anakawatsekera mʼndende, nakawayika mʼmanja mwa mkulu wa asilikali olonda ku nyumba kwa mfumu kuja, mʼndende momwe Yosefe ankasungidwamo. 4Mkulu wa alonda aja anawapereka mʼmanja mwa Yosefe, ndipo iye anawasamalira.

Iwo anakhala mʼndendemo kwa kanthawi. 5Usiku wina, aliyense wa anthu awiriwa, wopereka zakumwa pamodzi ndi wopanga buledi wa ku nyumba ya mfumu ya ku Igupto aja, amene ankasungidwa mʼndende, analota maloto. Malotowo anali ndi tanthauzo lake.

6Mmawa wake, Yosefe atabwera, anaona kuti nkhope zawo zinali zakugwa. 7Choncho anafunsa akuluakulu a kwa Farao amene anali naye mʼndende muja kuti, “Bwanji nkhope zanu zili zachisoni lero?”

8Iwo anayankha, “Tonse awiri talota maloto, koma palibe wotitanthauzira malotowo.”

Pamenepo Yosefe anawawuza kuti, “Ndi Mulungu yekha amene amapereka matanthauzo a maloto. Uzeni ine maloto anu.”

9Choncho mkulu wa operekera zakumwa uja anamuwuza Yosefe maloto ake. Anati, “Mʼmaloto anga ndinaona mtengo wa mpesa, 10unali ndi nthambi zitatu. Mpesawo utangophukira, unachita maluwa ndipo maphava ake anabereka mphesa zakupsa. 11Chikho cha Farao chinali mʼmanja mwanga, ndipo ndinatenga mphesa, kupsinyira mu chikho cha Farao ndi kuchipereka mʼmanja mwake.”

12Yosefe anati kwa iye, “Tanthauzo lake ndi ili: Nthambi zitatuzo ndi masiku atatu. 13Pakangopita masiku atatu, Farao adzakutulutsa muno. Udzaperekera zakumwa kwa Farao monga momwe umachitira poyamba. 14Koma zako zikakuyendera bwino, udzandikumbukire ndi kundikomera mtima. Chonde ukandipepesere kwa Farao kuti anditulutse muno. 15Popezatu ine anangochita mondiba kubwera nane kuno kuchokera ku dziko la Ahebri, ndipo ngakhale kunoko, ine sindinalakwe kali konse kuti ndizipezeka mʼdzenje muno.”

16Mkulu wa opanga buledi ataona kuti Yosefe wapereka tanthauzo labwino, anati kwa Yosefe, “Inenso ndinalota nditasenza nsengwa zitatu za buledi. 17Mu nsengwa yapamwamba munali zakudya zamitundumitundu za Farao, koma mbalame zimadya zakudyazo.”

18Yosefe anati, “Tanthauzo lake ndi ili: nsengwa zitatuzo ndi masiku atatu. 19Pakangotha masiku atatu Farao adzakutulutsa muno koma adzakupachika. Ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.”

20Tsono tsiku lachitatulo linali lokumbukira kubadwa kwa Farao, ndipo anawakonzera phwando akuluakulu ake onse. Anatulutsa mʼndende mkulu wa operekera zakumwa ndi mkulu wa ophika buledi, ndipo anawayimiritsa pamaso pa nduna zake. 21Tsono Farao anamubwezera mkulu wa operekera zakumwa uja pa udindo wake, kotero kuti anayamba kuperekeranso zakumwa kwa Farao, 22koma mkulu wa ophika buledi anamupachika, mofanana ndi mmene Yosefe anatanthauzira maloto.

23Koma mkulu wa operekera zakumwa uja sanamukumbukire Yosefe ndipo anamuyiwaliratu.

King James Version

Genesis 40:1-23

1And it came to pass after these things, that the butler of the king of Egypt and his baker had offended their lord the king of Egypt. 2And Pharaoh was wroth against two of his officers, against the chief of the butlers, and against the chief of the bakers. 3And he put them in ward in the house of the captain of the guard, into the prison, the place where Joseph was bound. 4And the captain of the guard charged Joseph with them, and he served them: and they continued a season in ward.

5¶ And they dreamed a dream both of them, each man his dream in one night, each man according to the interpretation of his dream, the butler and the baker of the king of Egypt, which were bound in the prison. 6And Joseph came in unto them in the morning, and looked upon them, and, behold, they were sad. 7And he asked Pharaoh’s officers that were with him in the ward of his lord’s house, saying, Wherefore look ye so sadly to day?40.7 look…: Heb. are your faces evil? 8And they said unto him, We have dreamed a dream, and there is no interpreter of it. And Joseph said unto them, Do not interpretations belong to God? tell me them, I pray you. 9And the chief butler told his dream to Joseph, and said to him, In my dream, behold, a vine was before me; 10And in the vine were three branches: and it was as though it budded, and her blossoms shot forth; and the clusters thereof brought forth ripe grapes: 11And Pharaoh’s cup was in my hand: and I took the grapes, and pressed them into Pharaoh’s cup, and I gave the cup into Pharaoh’s hand. 12And Joseph said unto him, This is the interpretation of it: The three branches are three days: 13Yet within three days shall Pharaoh lift up thine head, and restore thee unto thy place: and thou shalt deliver Pharaoh’s cup into his hand, after the former manner when thou wast his butler.40.13 lift…: or, reckon 14But think on me when it shall be well with thee, and shew kindness, I pray thee, unto me, and make mention of me unto Pharaoh, and bring me out of this house:40.14 think…: Heb. remember me with thee 15For indeed I was stolen away out of the land of the Hebrews: and here also have I done nothing that they should put me into the dungeon. 16When the chief baker saw that the interpretation was good, he said unto Joseph, I also was in my dream, and, behold, I had three white baskets on my head:40.16 white: or, full of holes 17And in the uppermost basket there was of all manner of bakemeats for Pharaoh; and the birds did eat them out of the basket upon my head.40.17 bakemeats…: Heb. meat of Pharaoh, the work of a baker, or, cook 18And Joseph answered and said, This is the interpretation thereof: The three baskets are three days: 19Yet within three days shall Pharaoh lift up thy head from off thee, and shall hang thee on a tree; and the birds shall eat thy flesh from off thee.40.19 lift…: or, reckon thee, and take thy office from thee

20¶ And it came to pass the third day, which was Pharaoh’s birthday, that he made a feast unto all his servants: and he lifted up the head of the chief butler and of the chief baker among his servants.40.20 lifted…: or, reckoned 21And he restored the chief butler unto his butlership again; and he gave the cup into Pharaoh’s hand: 22But he hanged the chief baker: as Joseph had interpreted to them. 23Yet did not the chief butler remember Joseph, but forgat him.