Genesis 35 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 35:1-29

Yakobo Abwerera ku Beteli

1Tsono Mulungu anati kwa Yakobo, “Nyamuka uchoke kuno kupita ku Beteli. Kumeneko ukamange guwa lansembe la Mulungu amene anadza kwa iwe pamene umathawa Esau, mʼbale wako.”

2Choncho Yakobo anawuza a pa banja pake ndi onse amene anali naye kuti, “Chotsani milungu yachilendo imene muli nayo, ndipo mudziyeretse nokha ndi kusintha zovala zanu. 3Tiyeni tinyamuke kuchoka kuno kupita ku Beteli. Kumeneko ndikamumangira guwa lansembe Mulungu amene anandithandiza pa nthawi za masautso anga, komanso amene wakhala nane mʼmayendedwe anga onse.” 4Choncho anamupatsa Yakobo milungu yachilendo yonse imene anali nayo pamodzi ndi ndolo. Iye anazikwirira pansi pa mtengo wa thundu ku Sekemu. 5Pamenepo ananyamuka, ndipo mtima woopa Mulungu unagwera anthu onse a mʼmizinda yozungulira, kotero kuti palibe aliyense amene anatsatira banja la Yakobo.

6Yakobo ndi anthu onse anali naye aja anafika ku Luzi (ku Beteli) mu dziko la Kanaani. 7Kumeneko anamanga guwa lansembe nalitcha Eli Beteli, chifukwa kunali kumeneko kumene Mulungu anadziwulula yekha kwa Yakobo pamene ankathawa mʼbale wake.

8Debora mlezi wa Rakele anamwalira komweko nayikidwa mʼmanda pansi pa mtengo wa thundu cha kumunsi kwa Beteli. Choncho panatchedwa Aloni-Bakuti (mtengo wamaliro).

9Yakobo atabwera kuchokera ku Padanaramu, Mulungu anabweranso kwa iye namudalitsa. 10Mulungu anati kwa iye, “Dzina lako ndiwe Yakobo, koma sudzatchedwanso Yakobo; koma udzatchedwa Israeli.” Choncho anamutcha iye Israeli.

11Ndipo Mulungu anati kwa iye, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse; berekanani ndi kuchulukana. Mtundu wa anthu, inde, mitundu yambiri ya anthu idzatuluka mwa iwe, ndipo ena mwa zidzukulu zako adzakhala mafumu. 12Dziko limene ndinapereka kwa Abrahamu ndi Isake ndiliperekanso kwa iwe. Lidzakhala lako ndi la zidzukulu zako.” 13Kenaka Mulungu anamusiya Yakobo.

14Yakobo anayika mwala wachikumbutso pa malo pamene Mulungu anayankhula naye paja. Iye anathirapo nsembe yachakumwa ndi yamafuta. 15Yakobo anawatcha malo amene Mulungu anayankhula naye aja kuti Beteli.

Imfa ya Isake ndi Rakele

16Kenaka anachoka ku Beteli. Koma ali pafupi kufika ku Efurata nthawi yakuti Rakele aone mwana inakwana. Iye anavutika pobereka. 17Akanali chivutikire choncho, mzamba anamulimbikitsa nati, “Usaope pakuti ubala mwana wina wamwamuna.” 18Tsono pamene Rakele ankapuma wefuwefu (popeza ankamwalira) iye anatcha mwana uja kuti Beni-Oni. Koma abambo ake anamutcha kuti Benjamini.

19Choncho Rakele anamwalira ndipo anayikidwa pa njira yopita ku Efurata (Kumeneko ndiye ku Betelehemu). 20Pa manda ake, Yakobo anayimika mwala wachikumbutso wa pa manda ndipo ulipobe mpaka lero.

21Israeli (Yakobo) anasunthanso nakamanga tenti yake kupitirira nsanja ya Ederi. 22Israeli akanali mʼderali, Rubeni anapita nakagonana ndi Biliha, mdzakazi wa abambo ake. Yakobo uja anazimva zimenezi.

Yakobo anali ndi ana aamuna khumi ndi awiri:

23Ana a Leya ndi awa:

Rubeni anali mwana woyamba wa Yakobo,

Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, ndi Zebuloni.

24Ana a Rakele ndi awa:

Yosefe ndi Benjamini.

25Ana a Biliha, wantchito wa Rakele ndi awa:

Dani ndi Nafutali.

26Ana a Zilipa wantchito wa Leya ndi awa:

Gadi ndi Aseri.

Awa ndiwo ana a Yakobo amene anabadwira ku Padanaramu.

27Yakobo anafika ku mudzi kwa abambo ake Isake ku Mamre, (kumene kunkatchedwa ku Kiriyati-Ariba kapenanso Hebroni) kumene Abrahamu ndi Isake anakhalako kale. 28Isake anakhala ndi moyo zaka 180. 29Anamwalira ali wokalamba kwambiri ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. Ndipo ana ake Esau ndi Yakobo anamuyika mʼmanda.