Genesis 34 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 34:1-31

Dina ndi Sekemu

1Tsopano Dina, mwana amene Leya anaberekera Yakobo, anapita kukacheza ndi akazi ena a mʼdzikolo. 2Pamene Sekemu mwana wa Hamori Mhivi, mfumu ya deralo, anamuona, anamugwirira. 3Koma Sekemu anamukondadi namwali uja, Dina, mwana wa Yakobo motero kuti anamuyankhula mawu womutonthoza. 4Choncho Sekemu anati kwa abambo ake Hamori, “Mundipezere mtsikana uyu kuti akhale mkazi wanga.”

5Yakobo anamva kuti mwana wake Dina wagwiriridwa, koma sanachitepo kanthu msanga kudikira mpaka ana ake amuna omwe anali ku busa atabwerako.

6Kenaka Hamori, abambo a Sekemu, anapita kukakambirana ndi Yakobo. 7Pa nthawi iyi nʼkuti ana a Yakobo atabwererako ku busa kuja. Iwo atangomva zimene zinachitika, anawawidwa mtima. Iwo anapsa mtima kwambiri kuti Sekemu nʼkuchita chonyansa choterechi mu dziko la Israeli, kumugwirira Dina, mwana wa Yakobo.

8Koma Hamori anawawuza kuti, “Mwana wanga Sekemu wamukonda kwambiri mwana wanu. Chonde muloleni kuti akhale mkazi wake. 9Tiyeni tichite mgwirizano wa ukwati kuti ife tidzikwatira ana anu ndi inu mudzikwatira ana athu. 10Khazikikani pakati pathu. Mukhoza kupeza malo wokhala kulikonse kumene mufuna. Mukhozanso kuchita malonda momasuka ndi kupeza chuma.”

11Pamenepo Sekemu anati kwa abambo ndi alongo ake a Dina, “Inu mundikomere mtima, ndipo ndidzakupatsani chilichonse munganene. 12Tchulani mtengo wamalowolo umene ndiyenera kupereka, ndipo ndipereka. Ndidzakupatsani chilichonse chimene mukufuna malingana inu mukandipatsa namwaliyu kuti ndimukwatire.”

13Ana a Yakobo anayankha Sekemu ndi abambo ake, Hamori mwachinyengo chifukwa mlongo wawo, Dina anali atayipitsidwa. 14Iwo anati, “Sitingachite zimenezo, kupereka mlongo wathu kwa munthu wosachita mdulidwe. Chimenecho ndi chinthu cha manyazi kwa ife. 15Tikuvomerani pokhapokha mutakhala ngati ife, mutachita mdulidwe ana anu onse aamuna. 16Kenaka tidzakulolani kuti mukwatire ana athu, ifenso tizikwatira ana anu. Choncho tidzakhala pakati panu ndipo tidzakhala anthu amodzi. 17Koma ngati simuvomereza kuchita mdulidwe titenga mlongo wathu ndi kupita.”

18Mawu amenewa anakondweretsa Hamori ndi mwana wake Sekemu. 19Mnyamata uja amene anali wolemekezeka kwambiri pa banja lake lonse, sanachedwe kuchita mdulidwe popeza anamukonda kwambiri mwana wa Yakobo. 20Choncho Hamori ndi mwana wake Sekemu anapita ku chipata cha mzinda wawo kukayankhula ndi anthu a mu mzindawo. 21Iwo anati, “Anthu awa ndi a mtendere. Aloleni kuti akhale mʼdziko mwathu muno nachitamo malonda. Dzikoli lili ndi malo ambiri woti iwo nʼkukhalamo. Tingathe kukwatira ana awo aakazi ndipo angathe kukwatira ana athu aakazi. 22Komatu anthuwa adzavomereza kukhala amodzi a ife pokhapokha ngati amuna onse pakati pathu atachita mdulidwe monga alili iwo. 23Tikatero, ndiye kuti ziweto zawo zonsezi, katundu wawo yenseyu ndi ziweto zawo zina zonsezi zidzakhala zathu. Choncho tiyeni tiwavomereze ndipo adzakhazikika pakati pathu.”

24Amuna onse amene anatuluka ku chipata cha mzinda anavomerezana ndi Hamori ndi mwana wake Sekemu, ndipo aliyense wamwamuna mu mzindamo anachita mdulidwe.

25Patapita masiku atatu, amuna onse akumvabe ululu wa kuchita mdulidwe uja, ana awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, alongo ake a Dina, anatenga malupanga ndi kulowa mu mzindawo mwakachetechete napha amuna onse. 26Anapha Hamori ndi Sekemu. Anakatenga Dina ku nyumba kwa Sekemu nanyamuka. 27Ana a Yakobo anafika kwa anthu ophedwawo ndi kututa katundu mu mzindawo chifukwa anagwiririra mlongo wawo. 28Analanda nkhosa zawo, ngʼombe zawo, abulu awo ndi china chilichonse chawo mu mzindamo pamodzi ndi za ku minda. 29Anawatengera chuma chawo chonse, akazi ndi ana awo, pamodzi ndi zonse zimene zinapezeka mʼnyumba zawo. Zonsezi zinayesedwa ngati zolandidwa ku nkhondo.

30Pamenepo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, “Mwandiputira mavuto, ndi kundiyipitsira dzina pakati pa anthu a mʼdziko lino, Akanaani ndi Aperezi. Ife ndife owerengeka, ndipo atati aphatikizane kudzandithira nkhondo, ndiye kuti ine ndi banja langa tidzawonongeka.”

31Koma iwo anayankha kuti, “Pepani, nanga achite kumusandutsa mlongo wathu ngati mkazi wachiwerewere?”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

創世記 34:1-31

底娜受辱

1一天,利亞雅各所生的女兒底娜到外面去見當地的女子。 2當地首領希未哈抹的兒子示劍看到她,就抓住她,強行玷污了她。 3他戀慕雅各的女兒底娜,就用甜言蜜語討她歡心。 4他求父親哈抹為他說親,把底娜娶過來。 5消息傳到雅各耳中時,他的兒子們正在田野放牧。他只好忍氣吞聲,等兒子們回來再作打算。 6示劍的父親哈抹來和雅各商議。 7雅各的兒子們一聽說這事,就從田野趕回來。大家都非常憤怒,因為示劍不該對以色列家做這醜事——玷污雅各的女兒。

8哈抹跟他們商議說:「我兒子示劍愛慕你們家的女兒,請你們把女兒嫁給他吧! 9我們可以互相通婚,你們可以把女兒嫁給我們的兒子,也可以娶我們的女兒為妻。 10你們可以在我們這裡安頓下來,這片土地就在你們面前,住在這裡做買賣、置產業吧。」 11示劍底娜的父親和她的弟兄們說:「請你們恩待我,你們要什麼,我都給你們。 12只要你們答應把女兒嫁給我,無論你們要多少聘金和禮物,我必如數奉上。」

雅各之子計殺示劍人

13雅各的兒子們因為示劍玷污了他們的妹妹底娜,就假意對示劍和他的父親哈抹說: 14「我們不能把妹妹嫁給沒有受過割禮的人,這對我們是一種羞辱。 15除非你們所有的男子都跟我們一樣受割禮, 16我們才能答應和你們通婚,共同生活,結成一個民族。 17如果你們不肯這樣做,我們就把妹妹帶走。」

18哈抹父子欣然答應。 19示劍毫不遲延地照辦,因為他熱戀底娜。在哈抹家族中,他最受人尊重。 20哈抹父子來到城門口,對那城的居民說: 21「這些人跟我們相處和睦,就讓他們在這裡定居、做買賣吧。我們這裡有足夠的地方可以容納他們,我們可以和他們通婚。 22可是,他們有一個條件,就是要我們所有的男子和他們一樣接受割禮,他們才答應和我們一起生活,結成一個民族。 23到時候,他們的財產和牛羊等所有牲畜不全歸我們了嗎?我們同意他們吧,這樣他們就會在我們這裡定居。」 24在城門進出的人聽了哈抹父子的話,都表示贊同。於是,城裡的男子都接受了割禮。

25到了第三天,他們傷口正疼痛的時候,雅各的兩個兒子——底娜的哥哥西緬利未拿著利劍,乘眾人沒有防備,潛入城中,殺掉了所有的男子, 26包括哈抹示劍,從示劍家裡帶走了底娜27雅各的兒子又到城裡擄掠,因為他們的妹妹在那裡被人玷污。 28他們搶走牛群、羊群、驢群和城裡城外所有的東西, 29並帶走所有財物、婦孺以及房屋裡的一切。 30雅各責備西緬利未說:「你們為什麼要給我惹麻煩,使我在當地的迦南人和比利洗人中留下臭名呢?我們人數很少,要是他們聯手來攻擊我們,我們全家必遭滅門之禍。」 31他們說:「他怎麼能把我們的妹妹當妓女對待?」