Genesis 30 – CCL & NIRV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 30:1-43

1Rakele ataona kuti sakumuberekera Yakobo ana, anayamba kumuchitira nsanje mʼbale wake. Choncho anati kwa Yakobo, “Undipatse ana kapena apo ayi ndingofa!”

2Yakobo anapsera mtima Rakele ndipo nati, “Kodi ine ndalowa mʼmalo mwa Mulungu amene wakulepheretsa iwe kukhala ndi ana?”

3Pamenepo Rakele anati kwa Yakobo, “Mdzakazi wanga Biliha nayu. Lowana naye kuti mwina nʼkundibalira mwana, ndipo kudzera mwa iyeyu nanenso nʼkukhala ndi ana.”

4Ndipo anamupatsa Yakobo wantchito wake Biliha kuti alowane naye. Choncho Yakobo analowana ndi Biliha, 5ndipo Bilihayo anatenga pathupi namubalira Yakobo mwana wamwamuna. 6Pamenepo Rakele anati, “Mulungu waweruza mondikomera mtima, wamva kupempha kwanga ndipo wandipatsa mwana wa mwamuna.” Choncho anamutcha Dani.

7Biliha, wantchito wa Rakele, anatenganso pathupi nabalira Yakobo mwana wa mwamuna wachiwiri. 8Pamenepo Rakele anati, “Ndakhala ndikulimbana kwambiri ndi mʼbale wanga ndipo ndapambana.” Choncho anamutcha Nafutali.

9Pamene Leya anaona kuti waleka kubereka ana, iye anatenga wantchito wake Zilipa namupereka kwa Yakobo kuti alowane naye. 10Zilipa, wantchito wa Leya, anaberekera Yakobo mwana wamwamuna. 11Pamenepo Leya anati, “Mwayi wangawo!” Choncho anamutcha Gadi.

12Zilipa, wantchito wa Leya anamubalira Yakobo mwana wa mwamuna wachiwiri. 13Pamenepo Leya anati, “Ndakondwa bwanji! Amayi adzanditcha ine wokondwa.” Choncho anamutcha Aseri.

14Pa nthawi yokolola tirigu, Rubeni anapita ku munda ndipo anapezako zipatso za mankhwala wobereketsa. Tsono anatengerako mayi wake Leya. Rakele anati kwa Leya, “Chonde patseko mankhwala wakupezera mwana wakowo.”

15Koma iye anati kwa Rakele, “Kodi sizinakukwanire kulanda mwamuna wanga? Ukuti utengenso mankhwala a mwana wangawa.”

Iye anati, “Chabwino, agone ndi iwe usiku uno kuti tisinthane ndi mankhwala a mwana wakowo.”

16Choncho pamene Yakobo ankabwera kuchokera ku munda madzulo, Leya anapita kukakumana naye nati, “Lero mukagona ku nyumba chifukwa ndakubwerekani ndi mankhwala wobereketsa a mwana wanga.” Choncho usiku umenewo Yakobo anakalowa kwa Leya.

17Mulungu anamva pemphero la Leya ndipo anatenga pathupi nabalira Yakobo mwana wa mwamuna wachisanu. 18Pamenepo Leya anati, “Mulungu wandipatsa mphotho chifukwa chopereka wantchito wanga kwa mwamuna wanga.” Choncho anamutcha Isakara.

19Leya anatenganso pathupi nabalira Yakobo mwana wa mwamuna wachisanu ndi chimodzi. 20Pamenepo Leya anati, “Mulungu wandipatsa mphatso yapamwamba. Tsopano mwamuna wanga adzandilemekeza chifukwa ndamubalira ana aamuna asanu ndi mmodzi.” Choncho anamutcha Zebuloni.

21Patapita nthawi Leya anabereka mwana wamkazi ndipo anamutcha Dina.

22Kenaka, Mulungu anakumbukira Rakele namva pemphero lake ndi kulola kuti akhale ndi mwana. 23Rakele anatenga pathupi nabala mwana wamwamuna ndipo anati, “Mulungu wandichotsera manyazi anga.” 24Iye anamutcha mwanayo Yosefe, ndipo anati, “Mulungu andipatsenso mwana wina.”

Nkhosa za Yakobo Zichuluka

25Rakele atabereka Yosefe, Yakobo anati kwa Labani, “Ndimasuleni kuti ndizipita ku dziko la kwathu. 26Patseni akazi anga ndi ana anga, amene ndinakugwirirani ntchito, ndipo ndidzanyamuka ulendo. Inu mukudziwa ntchito imene ndakugwirirani.”

27Koma Labani anati kwa iye, “Chonde, ngati mungandikomere mtima musapite chifukwa ndadziwa kudzera mwa kuwombeza kwanga kuti Yehova wandidalitsa chifukwa cha inu.” 28Anapitiriza kunena kuti, “Tchula malipiro ako ndipo ndidzakupatsa.”

29Koma Yakobo anati kwa iye, “Inu mukudziwa mmene ine ndakugwirirani ntchito ndi mmene ziweto zanu zaswanira pamene ine ndimazisamalira. 30Poyamba munali nazo zochepa ine ndisanabwere, koma tsopano zachuluka. Yehova wakudalitsani chifukwa cha ine. Ndi nthawi tsopano kuti nane ndisamalire banja langa.”

31Labani anafunsa, “Ndikupatse chiyani?”

Yakobo anayankha, “Musandipatse kanthu. Koma mungondichitira izi ndipo ndidzapitiriza kusamalira nkhosa zanu ndi kuziyangʼanira: 32Mundilole ndiyendeyende pakati pa ziweto zanu lero ndi kuchotsamo mwana wankhosa wamkazi aliyense wakuda, mbuzi iliyonse yamathothomathotho ndi yamawangamawanga. Zimenezi ndiye zikhale malipiro anga. 33Ndipo chilungamo changa chidzaoneka mʼtsogolo, pamene inu mudzabwere kudzaona malipiro angawo. Ngati mudzapeza mbuzi mʼgulu langa imene si yamawangamawanga, kapena mwana wankhosa wamkazi amene si wakuda ndiye kuti zimenezo zidzakhala kuti ndinakuberani.”

34Labani anati, “Ndavomera, zikhale monga mmene wayankhuliramu.” 35Tsiku lomwelo Labani anachotsa atonde onse ndi mbuzi zazikazi zonse zimene zinali ndi mawangamawanga kapena zamathothomathotho, ndiponso zonse zabanga loyera. Anachotsa ana onse ankhosa aakazi akuda, napereka ziweto zonsezi kwa ana ake aamuna kuti aziweta. 36Kenaka Labani anayenda mtunda wa masiku atatu kutalikirana ndi Yakobo koma Yakobo anapitiriza kuweta nkhosa zina zonse za Labani.

37Tsono Yakobo anatenga nthambi zaziwisi za mitengo ya mkundi, alimoni ndi puleni nazisenda kuchotsa makungwa ake mpaka mtengo woyera wamʼkati kuonekera. 38Atatero anayika nthambi zija mʼmagome omwera madzi molunjika ziweto zija kuti pakumwa madziwo ziweto zazikazi ziziyangʼana nthambi zija popeza kuti pakumwa madzi ziweto zija zinkakwerana. 39Ndiye kuti nkhosa zija zinkatenga mawere pakumwa madzi molunjika nthambi zija, ndipo zinkaswa ana a mawangamawanga kapena a mathothomathotho. 40Yakobo anayika padera ana a ziweto zija. Koma ziweto zina anaziyika kuti ziyangʼanane ndi za Labani, zimene zinali za mawangamawanga ndi zakuda. Motero anapeza ziweto zakezake, ndipo sanazisakanize ndi za Labani. 41Yakobo ankayika nthambi zija momwera madzi pamene ziweto zamphamvu zazikazi zinkakweredwa pofuna kuti zitenge mawere pakumwa madzi moyangʼanana ndi nthambi zija. 42Koma sankayika nthambizo pamene ziweto zofowoka zazikazi zinkakweredwa pakumwa madzi. Choncho ziweto zofowoka zonse zinakhala za Labani, ndi ziweto zamphamvu zinakhala za Yakobo. 43Mwa njira imeneyi, Yakobo analemera kwambiri ndipo anali ndi ziweto zochuluka kwambiri, antchito aakazi ndi aamuna, ngamira ndi abulu.

New International Reader’s Version

Genesis 30:1-43

1Rachel saw that she wasn’t having any children by Jacob. So she became jealous of her sister. She said to Jacob, “Give me children, or I’ll die!”

2Jacob became angry with her. He said, “Do you think I’m God? He’s the one who has kept you from having children.”

3Then she said, “Here’s my servant Bilhah. Sleep with her so that she can have children for me. Then I too can have a family through her.”

4So Rachel gave Jacob her servant Bilhah as a wife. Jacob slept with her. 5And Bilhah became pregnant. She had a son by him. 6Then Rachel said, “God has stood up for my rights. He has listened to my prayer and given me a son.” So she named him Dan.

7Rachel’s servant Bilhah became pregnant again. She had a second son by Jacob. 8Then Rachel said, “I’ve had a great struggle with my sister. Now I’ve won.” So she named him Naphtali.

9Leah saw that she had stopped having children. So she gave her servant Zilpah to Jacob as a wife. 10Leah’s servant Zilpah had a son by Jacob. 11Then Leah said, “What good fortune!” So she named him Gad.

12Leah’s servant Zilpah had a second son by Jacob. 13Then Leah said, “I’m so happy! The women will call me happy.” So she named him Asher.

14While the wheat harvest was being gathered, Reuben went out into the fields. He found some mandrake plants. He brought them to his mother Leah. Rachel said to Leah, “Please give me some of your son’s mandrakes.”

15But Leah said to her, “Isn’t it enough that you took my husband away? Are you going to take my son’s mandrakes too?”

Rachel said, “All right. Jacob can sleep with you tonight if you give me your son’s mandrakes.”

16Jacob came in from the fields that evening. Leah went out to meet him. “You have to sleep with me tonight,” she said. “I’ve traded my son’s mandrakes for that time with you.” So he slept with her that night.

17God listened to Leah. She became pregnant and had a fifth son by Jacob. 18Then Leah said, “God has rewarded me because I gave my female servant to my husband.” So she named the boy Issachar.

19Leah became pregnant again. She had a sixth son by Jacob. 20Then Leah said, “God has given me a priceless gift. This time my husband will treat me with honor. I’ve had six sons by him.” So she named the boy Zebulun.

21Some time later she had a daughter. She named her Dinah.

22Then God listened to Rachel. He showed concern for her. He made it possible for her to have children. 23She became pregnant and had a son. Then she said, “God has taken away my shame.” 24She said, “May the Lord give me another son.” So she named him Joseph.

Jacob Becomes the Owner of Large Flocks

25After Rachel had Joseph, Jacob spoke to Laban. He said, “Send me on my way. I want to go back to my own home and country. 26Give me my wives and children. I worked for you to get them. So I’ll be on my way. You know how much work I’ve done for you.”

27But Laban said to him, “If you are pleased with me, stay here. I’ve discovered that the Lord has blessed me because of you.” 28He continued, “Name your pay. I’ll give it to you.”

29Jacob said to him, “You know how hard I’ve worked for you. You know that your livestock has done better under my care. 30You had only a little before I came. But that little has become a lot. The Lord has blessed you everywhere I’ve been. But when can I do something for my own family?”

31“What should I give you?” Laban asked.

“Don’t give me anything,” Jacob replied. “Just do one thing for me. Then I’ll go on taking care of your flocks and watching over them. 32Let me go through all your flocks today. Let me remove every speckled or spotted sheep. Let me remove every dark-colored lamb. Let me remove every speckled or spotted goat. They will be my pay. 33My honesty will be a witness about me in days to come. It will be a witness every time you check on what you have paid me. Suppose I have a goat that doesn’t have speckles or spots. Or suppose I have a lamb that isn’t dark colored. Then it will be considered stolen.”

34“I agree,” said Laban. “Let’s do what you have said.” 35That same day Laban removed all the male goats that had stripes or spots. He removed all the female goats that had speckles or spots. They were the ones that had white on them. He also removed all the dark-colored lambs. He had his sons take care of them. 36Then he put a journey of three days between himself and Jacob. But Jacob continued to take care of the rest of Laban’s flocks.

37Jacob took freshly cut branches from poplar, almond and plane trees. He made white stripes on the branches by peeling off their bark. 38Then he placed the peeled branches in all the stone tubs where the animals drank water. He placed them there so they would be right in front of the flocks when they came to drink. The flocks were ready to mate when they came to drink. 39So they mated in front of the branches. And the flocks gave birth to striped, speckled or spotted little ones. 40Jacob put the little ones of the flock to one side by themselves. But he made the older ones face the striped and dark-colored animals that belonged to Laban. In that way, he made separate flocks for himself. He didn’t put them with Laban’s animals. 41Every time the stronger females were ready to mate, Jacob would place the branches in the stone tubs. He would place them in front of the animals so they would mate near the branches. 42But if the animals were weak, he wouldn’t place the branches there. So the weak animals went to Laban. And the strong ones went to Jacob. 43That’s how Jacob became very rich. He became the owner of large flocks. He also had many male and female servants. And he had many camels and donkeys.