Genesis 29 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 29:1-35

Yakobo Afika ku Padanaramu

1Yakobo anapitiriza ulendo wake kupita ku dziko la anthu a kummawa. 2Atafika kumeneko anaona chitsime ku busa ndipo panali magulu atatu a nkhosa zitagona pafupi ndi chitsimecho chifukwa nkhosazo zimamwetsedwa madzi ochokera mʼchitsimecho. Pamwamba pa chitsimecho panali mwala waukulu. 3Amati nkhosa zonse zikasonkhana, abusawo ankagudubuza mwalawo, kuwuchotsa ndi kumwetsa madzi nkhosazo. Kenaka ankawubwezera mwalawo pamalo pake, pakamwa pa chitsimepo.

4Yakobo anafunsa abusawo kuti, “Abale anga, mwachokera kuti?”

Iwo anayankha, “Tachokera ku Harani.”

5Iye anawafunsanso kuti, “Kodi Labani, mdzukulu wa Nahori mukumudziwa?”

Iwo anayankha, “Inde tikumudziwa?”

6Ndipo Yakobo anawafunsanso, “Kodi ali bwino?”

Iwo anati, “Inde ali bwino. Nayu Rakele mwana wake akubwera apoyu ndi nkhosa.”

7Iye anati, “Taonani, dzuwa likanalipo ndipo nthawi yosonkhanitsa nkhosa sinakwane. Bwanji osazimwetsa madzi nkhosazi.”

8Iwo anayankha, “Ayi sitingatero. Tidikira mpaka nkhosa zonse zisonkhane. Zikatero, tigubuduza mwalawu kuwuchotsa pamwamba pa chitsimepo, kenaka nʼkuzimwetsa madzi nkhosazo.”

9Ali chiyankhulire nawo, Rakele anafika ndi nkhosa za abambo ake popeza ndiye amene ankaweta nkhosazo. 10Yakobo ataona Rakele mwana wa Labani, mlongo wa amayi ake, ali ndi nkhosa za Labani, anapita nawugudubuza mwala uja nazimwetsa madzi nkhosa za amalume akezo. 11Kenaka Yakobo anapsompsona Rakele nayamba kulira mokweza. 12Kenaka Yakobo anawuza Rakele kuti iye ndi mwana wa Rebeka, mlongo wa abambo a Rakele uja. Choncho Rakele anathamanga nakawuza abambo ake.

13Labani atamva za Yakobo, mwana wa mlongo wake, anafulumira kukakumana naye. Anamukupatira napsompsona, napita naye ku nyumba kwake. Yakobo anafotokozera Labani zonse zinachitika. 14Ndipo, Labani anati kwa iye, “Iwe ndiwe ndithu fupa ndi mnofu wanga.”

Yakobo Akwatira Leya ndi Rakele

Yakobo anakhala ndi Labani mwezi umodzi. 15Tsono Labani anawuza Yakobo kuti, “Zoona iwe ndi ife ndi abale. Koma suyenera kundigwirira ntchito popanda malipiro. Ndiwuze kuti malipiro ako azikhala wotani?”

16Tsono Labani anali ndi ana aakazi awiri; dzina la wamkulu linali Leya, ndipo dzina la wamngʼono linali Rakele. 17Leya anali ndi maonekedwe wofowoka koma Rakele anali wa maonekedwe wokongola kwambiri. 18Yakobo anakonda Rakele ndipo anati, “Ndidzakugwirirani ntchito kwa zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha mwana wanu wamngʼono, Rakele.”

19Labani anati, “Kuli bwino kuti ndimupereke kwa iwe ameneyu kusiyana ndi munthu wina. Khala ndi ine kuno.” 20Choncho Yakobo anagwira ntchito zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele. Koma kwa iye zaka zonsezi zinakhala ngati masiku wochepa chifukwa anamukonda Rakele.

21Kenaka Yakobo anati kwa Labani, “Nthawi yanga ndakwanitsa, ndipatseni mwana wanu kuti ndimukwatire.”

22Pamenepo Labani anakonza phwando la ukwati, nayitana anthu onse a pamalopo. 23Koma pokwana usiku, Labani anatenga mwana wake wamkazi Leya namupatsa Yakobo, ndipo Yakobo anagona naye. 24Ndipo Labani anapereka wantchito wake wamkazi Zilipa kwa Leya kuti akhale wantchito wake.

25Pakucha mmawa, Yakobo anaona kuti anagona ndi Leya. Choncho Yakobo anafunsa Labani, “Nʼchiyani mwandichitirachi? Kodi ine sindinakugwirireni ntchito chifukwa cha Rakele? Bwanji mwandinyenga?”

26Labani anayankha, “Si mwambo wathu kuno kupereka wamngʼono ku banja, wamkulu asanakwatiwe. 27Yamba watsiriza sabata ya chikondwerero cha ukwati wa Leya; kenaka ndidzakupatsanso Rakele. Koma udzayenera kundigwirira ntchito zaka zisanu ndi ziwiri.”

28Yakobo anachitadi momwemo. Anamaliza sabata ya chikondwerero cha Leya, ndipo Labani anamupatsa Rakele kuti akhale mkazi wake. 29Labani anapereka wantchito wake wamkazi Biliha kwa Rakele kuti akhale wantchito wake. 30Yakobo analowana ndi mkazi wake Rakele, ndipo Yakobo anakonda Rakele kuposa Leya. Ndipo anamugwirira ntchito Labani zaka zina zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele.

Ana a Yakobo

31Pamene Mulungu anaona kuti Yakobo sankamukonda Leya kwambiri, Iye analola kuti Leya uja akhale ndi ana, ndi kuti Rakele akhale wosabala. 32Leya anakhala ndi pathupi ndipo anabereka mwana wamwamuna. Anamutcha Rubeni pakuti anati, “Yehova waona kusauka kwanga. Zoonadi, mwamuna wanga adzandikonda tsopano.”

33Anakhalanso ndi pathupi ndipo pamene anabereka mwana wamwamuna anati, “Yehova anamva kuti mwamuna wanga sakundikonda, choncho wandipatsanso mwana winayu.” Ndipo anamutcha dzina lake Simeoni.

34Anatenganso pathupi kachitatu, ndipo pamene anabereka mwana wamwamuna anati, “Pano pokha tidzaphatikana kwambiri ndi mwamuna wanga, chifukwa ndamubalira ana aamuna atatu.” Kotero anamutcha dzina lake Levi.

35Anatenganso pathupi pena, ndipo pamene anabereka mwana wamwamuna, iye anati, “Nthawi ino ndidzalemekeza Yehova.” Choncho anamutcha Yuda. Kenaka analeka kubereka.