Genesis 28 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 28:1-22

1Choncho Isake anayitanitsa Yakobo namudalitsa nʼkumuwuzitsa kuti, “Usakwatire mkazi wa kuno ku Kanaani. 2Panopo upite ku Padanaramu, ku nyumba kwa Betueli abambo a amayi akowa, kumeneko ukakwatire mmodzi mwa ana aakazi a Labani, mlongo wa amayi akowa. 3Mulungu Wamphamvuzonse akudalitse iwe nakupatse ana ambiri mpaka udzasanduke gulu lalikulu la mitundu ya anthu. 4Mulunguyo akudalitse iwe monga mmene anamudalitsira Abrahamu kuti zidzukulu zako zidzalandira dziko limene ukukhalamo ngati mlendo kuti lidzakhale lawo. Ili ndi dziko limene Mulungu anapereka kwa Abrahamu.” 5Ndipo Isake anamulola Yakobo kuti anyamuke kupita ku Padanaramu kwa Labani mwana wa Betueli Mwaramu. Labani anali mlongo wa Rebeka, mayi wa Yakobo ndi Esau.

6Tsopano Esau anadziwa kuti Isake anadalitsa Yakobo ndi kumutumiza ku Padanaramu kuti akakwatire kumeneko. Anawuzidwanso kuti, “Usakwatire mkazi wa ku Kanaani.” 7Yakobo anamvera abambo ake ndi amayi ake ndi kupita ku Padanaramu. 8Ndiye pamenepo Esau anazindikira kuti abambo ake Isake sankakondwera ndi akazi a ku Kanaani; 9anapita kwa Ismaeli mwana wa Abrahamu nakwatira Mahalati mwana wa Ismaeli, mlongo wake wa Nebayoti. Anatero kuwonjezera akazi amene anali nawo kale.

Maloto a Yakobo pa Beteli

10Yakobo ananyamuka pa ulendo kuchoka ku Beeriseba kupita ku Harani. 11Atafika pa malo pena, anayima kuti agonepo chifukwa dzuwa linali litalowa. Anatenga mwala wina pomwepo natsamiritsapo mutu wake, ndipo anagona. 12Mʼmaloto, anaona makwerero oyimikidwa pansi ndipo anakafika kumwamba. Angelo a Mulungu amakwera ndi kutsika pa makwereropo. 13Tsono Yehova anayimirira pambali pake, nati, “Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu kholo lake la Isake abambo ako. Ndidzakupatsa iwe ndi zidzukulu zako dziko limene ukugonamolo. 14Zidzukulu zako zidzachuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi ndipo zidzabalalikira kumadzulo ndi kummawa, kumpoto ndi kummwera. Anthu onse adzalandira madalitso kudzera mwa iwe ndi zidzukulu zako. 15Ine ndili nawe pamodzi ndipo ndidzakuyangʼanira kulikonse upiteko, ndipo ndidzakubwezera ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zimene ndakulonjezazi.”

16Yakobo atadzidzimuka, anati, “Zoonadi Yehova ali pa malo ano, ndipo ine sindinadziwe.” 17Tsono anachita mantha ndipo anati, “Malo ano ndi woopsa ndithu. Zoonadi pano ndi pa nyumba ya Mulungu ndi khomo la kumwamba.”

18Mmamawa mwake Yakobo anatenga mwala umene anatsamira mutu wake uja nawuyimika ngati chipilala ndi kuthira mafuta pamwamba pake 19Iye anawatcha malowo Beteli, ngakhale kuti poyamba mzindawo ankawutcha Luzi.

20Pamenepo Yakobo analumbira kwa Yehova nati, “Ngati inu Mulungu mukhala ndi ine, kundiyangʼanira pa ulendo wangawu ndi kundipatsa chakudya ndi chovala; 21ngati inu mudzandibweretsa kwathu mu mtendere, ndiye kuti mudzakhala Mulungu wanga, 22ndipo mwala uwu ndawuyimikawu udzakhala Nyumba ya Mulungu. Ine ndidzakupatsani chakhumi cha zinthu zonse zimene mudzandipatse.”