Genesis 25 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 25:1-34

Abrahamu Amwalira

1Abrahamu anakwatira mkazi wina dzina lake Ketura. 2Iyeyu anamubalira Zimurani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa. 3Yokisani anabereka Seba ndi Dedani ndipo zidzukulu za Dedani ndiwo Aasuri, Aletusi, ndi Aleumi. 4Ana aamuna a Midiyani anali, Efai, Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida. Onsewa anali zidzukulu za Ketura.

5Abrahamu anasiyira Isake chilichonse anali nacho. 6Koma pamene anali ndi moyo, Abrahamu anapereka mphatso kwa ana aakazi ake ena onse. Kenaka anawatumiza ku dziko la kummawa kuti akhale kutali ndi mwana wake Isake.

7Abrahamu anakhala ndi moyo zaka 175. 8Abrahamu anamwalira atakalamba kwambiri ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. 9Ana ake, Isake ndi Ismaeli anamuyika mʼphanga la Makipela pafupi ndi Mamre, mʼmunda umene kale unali wa Efroni mwana wa Zohari Mhiti, 10uwu ndi munda umene Abrahamu anagula kwa Ahiti. Kumeneko Abrahamu anakayikidwa pamodzi ndi mkazi wake Sara. 11Atamwalira Abrahamu, Mulungu anadalitsa mwana wake Isake, amene ankakhala pafupi ndi Beeri-lahai-roi (chitsime cha Wamoyo Wondipenya).

Ana Aamuna a Ismaeli

12Nazi zidzukulu za Ismaeli, mwana wa Abrahamu amene wantchito wa Sara, Hagara Mwigupto uja, anaberekera Abrahamu.

13Awa ndi mayina a ana a Ismaeli monga mwa mndandanda wa mabadwidwe awo: Nebayoti ndiye anali mwana woyamba wa Ismaeli; kenaka Kedara, Adibeeli, Mibisamu, 14Misima, Duma, Masa, 15Hadadi, Tema, Yeturi, Nafisi ndi Kedema; 16Amenewa ndi ana a Ismaeli ndi mayina awo monga mwa midzi ndi misasa yawo. Anali olamulira mafuko khumi ndi awiri. 17Ismaeli anakhala ndi moyo zaka 137. Iye anamwalira ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. 18Zidzukulu za Ismaeli zinkakhala mʼdera la pakati pa Havila ndi Suri, kummwera kwa Igupto, mukamapita cha ku Asuri. Choncho anakhala kummawa kwa abale awo.

Yakobo ndi Esau

19Iyi ndi mbiri ya Isake mwana wa Abrahamu.

Abrahamu anabereka Isake 20ndipo Isake anali ndi zaka makumi anayi pamene anakwatira Rebeka mwana wa Betueli Mwaramu wa ku Padanaramu mlongo wa Labani Mwaramu.

21Isake anapempherera mkazi wake kwa Yehova popeza iye anali wosabereka. Yehova anayankha pemphero lake ndipo mkazi wake Rebeka anatenga pathupi. 22Koma pamene anawo amalimbana mʼmimba mwake, iye anati, “Bwanji zikundichitikira zoterezi?” Choncho anapita kukafunsa kwa Yehova.

23Yehova anati kwa iye,

“Udzabala mafuko awiri a anthu olimbana,

ndipo magulu awiri a anthu ochokera mwa iwe adzasiyana;

fuko limodzi lidzakhala la mphamvu kuposa linzake,

ndipo wamkulu adzatumikira wamngʼono.”

24Pamene nthawi inakwana yakuti abeleke, Rebeka anaberekadi mapasa. 25Woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati chovala cha ubweya; choncho anamutcha Esau. 26Kenaka mʼbale wake anabadwa atagwira chidendene cha Esau; choncho anamutcha Yakobo. Isake anali ndi zaka 60 pamene Rebeka anabereka mapasawa.

27Anyamatawo anakula ndipo Esau anakhala katswiri wosaka, munthu wamʼthengo, pamene Yakobo anali munthu wofatsa, wokonda kukhala pa nyumba. 28Isake ankakonda Esau chifukwa cha nyama za kutchire zomwe ankakonda kudya, koma Rebeka ankakonda Yakobo.

29Tsiku lina pamene Yakobo ankaphika chakudya, Esau anabwera kuchokera kuthengo ali wolefuka ndi njala. 30Iye anati kwa Yakobo, “Tandipatsako phala lofiiralo, ndimwe! Ndalefuka ndi njala.” (Nʼchifukwa chake amatchedwanso Edomu).

31Yakobo anayankha, “Choyamba undigulitse ukulu wako.”

32Esau anati, “Chabwino, ine ndatsala pangʼono kufa, ukulu undithandiza chiyani?”

33Koma Yakobo anati, “Lumbira kwa ine choyamba.” Kotero Esau analumbiradi, ndipo anagulitsa ukulu wake kwa Yakobo.

34Choncho Yakobo anamupatsa Esau buledi ndi phala lofiira lija. Iye anadya ndi kumwa, nanyamuka kumapita.

Motero Esau anapeputsa ukulu wake wachisamba uja.