Genesis 21 – CCL & CARSA

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 21:1-34

Kubadwa kwa Isake

1Yehova anakomera mtima Sara monga ananenera, ndipo Yehovayo anachita monga momwe analonjezera. 2Sara anakhala ndi pathupi ndipo anamuberekera Abrahamu mwana wamwamuna mu ukalamba wake, pa nyengo imene Mulungu anamulonjeza. 3Abrahamu anapereka dzina loti Isake kwa mwana wamwamuna amene Sara anamuberekera. 4Isake atakwanitsa masiku asanu ndi atatu, Abrahamu anamuchita mdulidwe monga Mulungu anamulamulira. 5Abrahamu anali ndi 100 pamene mwana wake Isake anabadwa.

6Sara anati, “Mulungu wandibweretsera mseko, ndipo aliyense amene adzamva zimenezi adzaseka nane pamodzi.” 7Ndipo anawonjezera kuti, “Ndani akanamuwuza Abrahamu kuti Sara nʼkudzayamwitsako ana? Chonsecho ndamubalira mwana wamwamuna kuwukalamba wake.”

Kuchotsedwa kwa Hagara ndi Ismaeli

8Mwana uja anakula mpaka kumuletsa kuyamwa. Tsiku lomuletsa Isake kuyamwa, Abrahamu anakonza phwando lalikulu. 9Koma Sara anaona kuti mwana wamwamuna amene Hagara Mwigupto anamuberekera Abrahamu amamuseka, 10ndipo anati kwa Abrahamu, “Muchotse mdzakazi ndi mwana wake wamwamunayu, pakuti mwana wa kapolo sadzagawana chuma ndi mwana wanga Isake.”

11Nkhaniyi inamumvetsa chisoni kwambiri Abrahamu chifukwa imakhudza mwana wake. 12Koma Mulungu anamuwuza Abrahamu kuti, “Usamve chisoni motero ndi mnyamatayu ndi mdzakazi wakoyu. Mvetsera chilichonse chomwe Sara akukuwuza, chifukwa zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake. 13Mwana wa mdzakazi wakoyu ndidzamusandutsa mtundu wa anthu chifukwa ndi mwana wako.”

14Mmamawa wake, Abrahamu anatenga chakudya ndi botolo la madzi nazipereka kwa Hagara. Anasenzetsa Hagara nawaperekeza pangʼono ndi mnyamatayo. Hagara ananyamuka nayendayenda mʼchipululu cha Beeriseba.

15Madzi atatha mʼbotolo muja, anamuyika mnyamatayo pansi pa zitsamba. 16Kenaka Hagara anachoka nakakhala pansi cha pakatalipo, pafupifupi mamita makumi asanu ndi anayi, popeza mʼmaganizo mwake amati, “Sindingaonerere mwanayu akufa.” Ndipo anakhala pansi cha poteropo nʼkumalira.

17Mulungu anamva mnyamatayo akulira ndipo mngelo wa Mulungu anayankhula kwa Hagara kuchokera kumwamba nati, “Chavuta nʼchiyani Hagara? Usachite mantha; Mulungu wamva kulira kwa mnyamatayo pamene wagonapo. 18Munyamule mnyamatayo ndipo umugwire dzanja pakuti ndidzamupanga kukhala mtundu waukulu.”

19Kenaka Mulungu anatsekula maso a Hagara ndipo anaona chitsime cha madzi. Choncho anapita nadzaza botolo lija ndi madzi ndi kumupatsa mnyamatayo kuti amwe.

20Mulungu anali ndi mnyamatayo pamene ankakula. Anakhala ku chipululu nakhala katswiri wolasa uta. 21Akukhala ku chipululu cha Parani, mayi ake anamupezera mkazi wochokera ku Igupto.

Pangano la ku Beeriseba

22Pa nthawiyo, Abimeleki ndi Fikolo wamkulu wankhondo wake anati kwa Abrahamu, “Mulungu ali nawe pa chilichonse umachita. 23Tsopano undilumbirire ine pano pamaso pa Mulungu kuti sudzachita mwa chinyengo ndi ine kapena ana anga kapena zidzukulu zanga. Undionetse ine pamodzi ndi dziko limene ukukhalamo ngati mlendo, kukoma mtima kokhala ngati kumene ndinakuonetsa ine.”

24Abrahamu anati, “Ine ndikulumbira.”

25Kenaka Abrahamu anadandaula kwa Abimeleki pa za chitsime chimene antchito a Abimeleki analanda. 26Koma Abimeleki anati, “Ine sindikudziwa amene anachita zimenezi. Iwe sunandiwuze, ndipo ndazimva lero zimenezi.”

27Choncho Abrahamu anabweretsa nkhosa ndi ngʼombe nazipereka kwa Abimeleki, ndipo anthu awiriwo anachita pangano. 28Abrahamu anapatulako ana ankhosa aakazi asanu ndi awiri kuchoka pagulu la nkhosa zina, 29ndipo Abimeleki anafunsa Abrahamu, “Kodi tanthauzo lake la ana ankhosa aakazi asanu ndi awiri amene wawapatula pawokhawa nʼchiyani?”

30Iye anayankha kuti, “Landirani ana ankhosa aakazi kuchokera mʼdzanja langa ngati umboni kuti ndinakumba chitsime ichi.”

31Kotero malo amenewo anatchedwa Beeriseba, chifukwa anthu awiriwo analumbirirapo malumbiro.

32Atatha kuchita pangano pa Beeriseba, Abimeleki ndi Fikolo mkulu wankhondo wake anabwerera ku dziko la Afilisti. 33Abrahamu anadzala mtengo wa bwemba ku Beeriseba, ndipo anapemphera pamenepo mʼdzina la Yehova, Mulungu Wamuyaya. 34Ndipo Abrahamu anakhala mʼdziko la Afilisti kwa nthawi yayitali.

Священное Писание (Восточный перевод), версия с «Аллахом»

Начало 21:1-34

Рождение Исхака

1Вечный, как Он и сказал, был милостив к Сарре и выполнил Своё обещание: 2Сарра забеременела и родила Ибрахиму сына, когда тот уже состарился, в то самое время, как обещал ему Аллах. 3Ибрахим дал своему новорождённому сыну, которого родила ему Сарра, имя Исхак. 4Когда его сыну Исхаку исполнилось восемь дней, Ибрахим обрезал его, как велел ему Аллах. 5Ибрахиму было сто лет, когда у него родился сын Исхак.

6Сарра сказала:

– Аллах заставил меня смеяться; каждый, кто услышит об этом, рассмеётся вместе со мной21:6 Или: «будет смеяться надо мной». Здесь присутствует игра слов, связанная с именем Исхак («он смеётся»)., – 7и добавила: – Кто бы сказал Ибрахиму, что Сарра будет кормить грудью? Но я родила ему сына в его старости.

8Ребёнок вырос и был отнят от груди. В тот день, когда Исхак был отнят от груди, Ибрахим устроил большой пир.

Изгнание Хаджар и Исмаила, сына Ибрахима

9Сарра увидела, что сын, которого египтянка Хаджар родила Ибрахиму, насмехается над Исхаком, 10и сказала Ибрахиму:

– Прогони эту рабыню и её сына, потому что сын этой рабыни не разделит наследства с моим сыном Исхаком.

11Ибрахим был сильно огорчён, потому что это был его сын. 12Но Аллах сказал ему:

– Не огорчайся из-за мальчика и рабыни. Послушайся Сарры и сделай всё, как она говорит, потому что через Исхака ты будешь иметь обещанное потомство21:12 Букв.: «семя».. 13Но Я произведу народ и от сына рабыни, потому что и он – твой потомок.

14На другой день рано утром Ибрахим взял еды и бурдюк с водой и дал Хаджар: положил их ей на плечи и отослал её прочь вместе с ребёнком. Она отправилась в путь и блуждала в пустыне Беэр-Шева. 15Когда вода в бурдюке кончилась, она оставила мальчика под кустом 16и, отойдя, села неподалёку, на расстоянии выстрела из лука, потому что думала: «Не стану смотреть, как мальчик умирает». И сидя там поблизости, она разрыдалась.

17Аллах услышал плач мальчика, и Ангел Аллаха обратился к Хаджар с небес и сказал ей:

– Что с тобой, Хаджар? Не бойся: Аллах услышал, как плачет мальчик там, где он лежит. 18Вставай, подними мальчика и возьми его за руку, потому что Я произведу от него великий народ.

19Тут Аллах открыл ей глаза, и она увидела колодец с водой. Она пошла, наполнила бурдюк водой и напоила мальчика.

20Аллах был с мальчиком. Исмаил вырос, поселился в пустыне и стал стрелком из лука. 21Он жил в пустыне Паран, и мать взяла для него жену из Египта.

Договор между Ибрахимом и Ави-Маликом

22В то время Ави-Малик, пришедший в сопровождении Фихола, начальника его войска, сказал Ибрахиму:

– Аллах с тобой во всём, что ты делаешь. 23Поклянись же мне здесь перед Аллахом, что ты не поступишь вероломно ни со мной, ни с моими детьми, ни с моим потомством. Окажи мне и стране, в которой ты живёшь как пришелец, ту же милость, какую я оказал тебе.

24Ибрахим сказал:

– Клянусь.

25Потом Ибрахим упрекнул Ави-Малика за колодец с водой, который захватили слуги Ави-Малика. 26Но Ави-Малик сказал:

– Я не знаю, кто это сделал. Ты не говорил мне, и до сего дня я не слышал об этом.

27Ибрахим привёл мелкий и крупный скот и дал Ави-Малику, и они заключили союз. 28Ибрахим отделил из стада семь молодых овец, 29и Ави-Малик спросил Ибрахима:

– Что означают эти семь молодых овец, которых ты отделил особо?

30Он ответил:

– Прими от меня семь этих молодых овец как свидетельство того, что я выкопал этот колодец, и он мой.

31Вот почему то место было названо Беэр-Шева («колодец семи, колодец клятвы»): ведь они оба дали там клятву.

32Заключив договор в Беэр-Шеве, Ави-Малик и Фихол, начальник его войска, вернулись на землю филистимлян. 33Ибрахим посадил в Беэр-Шеве тамариск и призвал там имя Вечного, Кто есть Бог навеки. 34Ибрахим жил на земле филистимлян долгое время.