Ezekieli 9 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 9:1-11

Opembedza Mafano Aphedwa

1Pambuyo pake Yehova anandiyankhula mofuwula kuti, “Bwerani pafupi, inu odzalanga mzindawu, aliyense ali ndi chida chake mʼmanja.” 2Ndipo ndinaona anthu asanu ndi mmodzi akubwera kuchokera ku chipata chakumtunda chimene chimaloza kumpoto, aliyense ali ndi chida choopsa cha nkhondo mʼdzanja lake. Pagulu pawopa panali munthu wovala chovala chabafuta, atatenga zolembera pambali pake. Iwo analowa ndi kuyima pambali pa guwa lamkuwa.

3Tsono ulemerero wa Mulungu wa Israeli unakwera kuchokera pamwamba pa akerubi, pamene unali, ndipo unafika pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Pamenepo Yehova anayitana munthu amene anavala chovala chabafuta uja amene anatenga zolembera pambali pake 4ndipo anamuwuza kuti, “Pita mu mzinda wonse wa Yerusalemu ndi kuyika chizindikiro pamphumi pa anthu amene akumva chisoni ndi kulira chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene zikuchitika mu mzindamo.”

5Kenaka ndinamva Yehova akuwuza anthu ena aja kuti, “Mutsateni mu mzinda wonse ndipo mukakanthe aliyense mopanda kumvera chisoni kapena chifundo. 6Mukaphe kotheratu anthu okalamba, anyamata ndi atsikana, makanda ndi akazi koma musakakhudze wina aliyense amene ali ndi chizindikiro. Muyambire ku Nyumba yanga yopatulika.” Motero iwo anayamba ndi akuluakulu amene anali kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu.

7Ndipo Yehova anawawuza kuti, “Ipitsani Nyumba ya Mulungu ndipo mudzaze mabwalo ake ndi anthu akufa. Pitani.” Choncho iwo anapita nayamba kupha anthu mu mzinda monse. 8Pamene iwo ankapha anthu, ine ndinatsala ndekha. Tsono ndinadzigwetsa chafufumimba ndi kufuwula kuti, “Aa, Ambuye Yehova! Kodi mwawakwiyiratu anthu a ku Yerusalemu motero kuti mudzawononga kotheratu anthu onse otsala ku Israeli?”

9Iye anandiyankha kuti, “Tchimo la Aisraeli ndi Yuda ndi lalikulu kwambiri; dziko ladzaza ndi zophana ndipo mu mzinda mwadzaza ndi zosalungama. Iwo akunena kuti, ‘Yehova walisiya dziko lake; Yehova sakuona.’ 10Choncho sindidzawamvera chisoni kapena kuwaleka, koma Ine ndidzawalanga potsata zochita zawo.”

11Ndipo munthu wovala chovala chabafuta uja atatenga zolembera pambali pake anadzafotokozera Yehova kuti, “Ndachita monga munandilamulira.”