Ezekieli 47 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 47:1-23

Mtsinje Wotuluka Mʼnyumba ya Mulungu

1Munthuyo anabwerera nane ku chipata cha Nyumba ya Mulungu. Ndinaona madzi akutuluka kunsi kwa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu chakummawa; poti Nyumba ya Mulungu inayangʼana kummawa. Madziwo ankachokera kunsi kwa mbali yakummwera ya Nyumba ya Mulungu; kummwera kwa guwa lansembe. 2Ananditulutsira pa chipata chakumpoto ndipo anazungulira nane panja mpaka ku chipata chakunja choyangʼana kummawa. Ndipo ndinaona madzi akutuluka chakummwera kwa chipatacho.

3Munthuyo anapita chakummawa ali ndi chingwe choyezera mʼdzanja lake. Iye anayeza mamita 500, ndipo pambuyo pake analowa nane mʼmadziwo amene ankalekeza mʼkakolo. 4Anayezanso mamita 500 ndipo analowa nane mʼmadzi amene amalekeza mʼmawondo. Iye anayezanso mamita 500 ndipo analowa nane mʼmadzi amene amalekeza mʼchiwuno. 5Munthuyo anayezanso mamita 500, ndipo madziwo anasanduka mtsinje woti sindikanatha kuwoloka, pakuti madziwo anakwera, ndipo anali ozama ofunika kusambira pofuna kuwoloka. 6Munthuyo anandifunsa kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziona zimenezi?”

Kenaka anabwerera nane ku gombe la mtsinjewo. 7Nditafika pa gombepo, ndinaona mitengo yambiri ku mbali iliyonse ya mtsinjewo. 8Tsono munthuyo anandiwuza kuti, “Madziwa akupita ku chigawo chakummawa ndi kutsikira ku chigwa cha Araba. Kenaka akathira mʼNyanja Yakufa, ndipo akakalowa mʼnyanjayo, madzi a nyanjayo adzasanduka okoma. 9Kulikonse kumene mtsinjewo ukuyenda cholengedwa chilichonse chidzakhala ndi moyo. Nsombanso zidzakhala zambiri. Paja madzi amenewa amapita kumeneko kuti akakometse madzi ena. Choncho kulikonse kumene madziwa akuyenda chilichonse chidzakhala ndi moyo. 10Asodzi adzayima mʼmbali mwa Nyanja Yakufa. Pakuti kuchokera ku Eni-Gedi mpaka ku Eni Egilaimu kudzakhala malo oponyako makoka. Kudzakhala nsomba zamitundumitundu, monga nsomba za ku Nyanja Yayikulu. 11Koma mathawale ake ndi maiwe ake sadzakhala ndi madzi abwino; adzakhala ndi madzi a mchere. 12Mʼmbali zonse za mtsinje mudzamera mitengo ya zipatso zakudya za mtundu uliwonse. Masamba ake sadzafota kapena kulephera kubereka zipatso. Izidzabereka mwezi uliwonse, chifukwa madzi ake adzakhala ochokera ku Nyumba ya Mulungu. Zipatso zake anthu azidzadya ndipo masamba ake azidzachitira mankhwala.”

Malire a Dziko

13Ambuye Yehova akuti, “Nawa malire amene mudzatsate powagawira dziko mafuko khumi ndi awiri a Israeli aja. Yosefe adzalandire zigawo ziwiri. 14Mudzawagawire dzikolo mofanana. Paja ndinalumbira kwa makolo anu kuti dzikoli lidzakhala lanulanu.

15“Malire a dzikolo adzakhala motere:

Mbali ya kumpoto adzachokera ku Nyanja Yayikulu kutsata msewu wa ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamoti ndi kupitirira ku Zedadi, 16Berota ndi Sibraimu (mizinda imene ili pakati pa malire a Damasiko ndi Hamati mpaka kukafika ku Hazeri Hatikoni mzinda umene uli mʼmalire mwa Haurani. 17Motero malire akumpoto adzachokera ku nyanja mpaka ku mzinda wa Hazari-Enoni, mʼmalire akumpoto a Damasiko ndi chakumpoto kwa malire a Hamati. Awa adzakhala malire a kumpoto.

18Mbali ya kummawa malire adzayenda pakati pa Haurani ndi Damasiko, mbali ya ku Yorodani pakati pa Giliyadi ndi dziko la Israeli, ku nyanja ya kummawa mpaka ku mzinda wa Tamara. Awa adzakhala malire akummawa.

19Mbali yakummwera malire adzayenda kuchokera ku dziwe la mzinda wa Tamara mpaka ku madzi a ku Meriba Kadesi. Kenaka ndi kutsata chigwa cha ku Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu. Awa adzakhala malire akummwera.

20Mbali ya kumadzulo, malire adzakhala Nyanja Yayikulu mpaka pa malo oyangʼanana ndi Lebo Hamati. Awa adzakhala malire akumadzulo.”

21“Mugawane dziko limeneli pakati panu potsata mafuko a Israeli. 22Muligawe kuti likhale cholowa chanu ndiponso cholowa cha alendo amene akukhala pakati panu, nakhala ndi ana pakati panu. Inu muwatenge monga mbadwa za mu Israeli. Adzapatsidwe cholowa chawo pamodzi ndi inu pakati pa mafuko a Israeli. 23Mu fuko lililonse kumene mlendoyo akukhala mumupatse cholowa chake.” Ndikutero Ine Ambuye Yehova.