Ezekieli 41 – CCL & CARS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 41:1-26

1Ndipo munthuyo anapita nane mʼchipinda chopatulika cha Nyumba ya Mulungu ndipo anayeza khonde lake; mulifupi mwa khondelo munali mamita atatu mbali iliyonse kutalika kwake. 2Mulifupi mwa khomo munali motalika mamita asanu. Makoma a mbali zonse anali a mamita awiri ndi theka mulifupi mwake. Anayezanso kutalika kwa chipinda chopatulika chija ndipo mulitali mwake munali motalika mamita makumi awiri ndi mulifupi mwake munali mamita khumi.

3Kenaka munthuyo anakalowa mʼkati ndipo anayeza khonde la pa khomo; khondelo linali mita imodzi mulifupi mwake. Mulifupi mwa khondelo munali mamita atatu. 4Ndiponso anayeza kutalika kwa chipinda chopatulika chenichenicho. Mulitali mwake munali mamita khumi, ndipo mulifupi mwake munali mamita khumi. Munthuyo anandiwuza kuti, “Ichi ndicho chipinda chopatulika kwambiri.”

5Tsono munthuyo anayeza khoma la Nyumba ya Mulungu; kuchindikira kwake kunali mamita atatu. Panalinso zipinda zina kuzungulira Nyumba ya Mulungu ndipo chilichonse chinali cha mamita awiri mulifupi wake. 6Zipindazo zinali zitatu zosanjikizana. Chigawo chilichonse chinali ndi zipinda makumi atatu. Pa makoma a Nyumba ya Mulungu panali zochirikiza zipindazo kuti zisatsamire khoma la Nyumba ya Mulungu. 7Zipinda za mʼmbalizo zinkapita zikulirakulira pomakwera chipinda ndi chipinda potsata kukulirakulira kwa zochirikiza za zipinda zija. Pambali pa Nyumba ya Mulungu panali makwerero okwerera pamwamba, kuchokera chigawo chapansi kudzera chapakati, mpaka kukafika pamwamba.

8Ndinaona chiwundo kuzungulira Nyumba ya Mulungu. Chinapanga maziko a zipindazo ndipo chinali cha mamita atatu. 9Khoma lakunja la zipindazo linali la mamita awiri ndi theka kuchindikira kwake. Pakati pa chiwundocho 10ndi zipinda za Nyumba ya Mulungu panali bwalo limeneli la mamita khumi kupingasa kwake kuzungulira Nyumba yonse ya Mulungu. 11Zitseko za zipinda zamʼmbalizo zinali zotsekulira ku chiwundo. Chitseko chimodzi chinkayangʼana kumpoto ndipo china chinkayangʼana kummwera. Chiwundo chosamangapo kanthu chinali mamita awiri ndi theka kukula kwake kuzungulira ponseponse.

12Nyumba imene inali chakummwera moyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu inali mamita 35 mulifupi mwake. Khoma la nyumbayo linali mamita awiri ndi theka kuchindikira kwake kuzungulira ponseponse, ndipo mulitali mwake linali mamita 45.

13Ndipo munthuyo anayeza Nyumba ya Mulungu ndipo mulitali mwake inali mamita makumi asanu. Nyumbayo ndi makoma ake, zonse zinali za mamita makumi asanu. 14Kumaso kwa Nyumba ya Mulungu chakummawa kwa bwalolo mulifupi mwake munali mamita makumi asanu.

15Kenaka anayeza kutalika kwa nyumba yoyangʼanana ndi bwalo chakumadzulo kwa Nyumba ya Mulungu, kuphatikizapo njira zamʼkati ku mbali iliyonse. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.

Chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu, chimene chili chamʼkati, khonde lamʼkati loyangʼanana ndi bwalo, 16mazenera ndi maferemu ake, zonsezi zinali zokutidwa ndi matabwa. Pamwamba moyangʼanana ndi chiwundo, Nyumba ya Mulungu inakutidwa ndi matabwa kuyambira pansi mpaka ku mazenera, (mazenerawo anali okutidwa), 17pamwamba pa khomo lolowera ku malo opatulika amʼkati komanso kuzungulira makoma onse kunja ndi mʼkati, 18anajambulapo zithunzi za kerubi mmodzi atakhala pakati pa kanjedza muwiri. Kerubi aliyense anali ndi nkhope ziwiri: 19imodzi inali nkhope ya munthu yoyangʼana kanjedza mbali imodzi, ndi ina inali nkhope ya mkango yoyangʼana kanjedza mbali ina. Zinajambulidwa kuzungulira Nyumba ya Mulungu yonse. 20Motero kuyambira pansi mpaka pamwamba pa khomo komanso pa makoma onse a chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu, anajambula zithunzi za akerubi ndi kanjedza pa makoma onse a malo opatulika.

21Mphuthu za chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu kutalika kwake mbali zonse kunali kofanana. Ndipo kumaso kwa malo opatulika kunali chinthu china chooneka ngati 22guwa lansembe la matabwa. Msinkhu wake unali mita imodzi ndi theka, mulitali mwake munali mita imodzi, mulifupi mwake munalinso mita imodzi. Mphuthu zake, tsinde lake ndi mbali zonse zinali za matabwa. Munthuyo anandiwuza kuti, “Tebulo limeneli ndilo limakhala pamaso pa Yehova.” 23Chipinda chachikulu chija chinali ndi zitseko ziwiri. Malo opatulika aja analinso ndi zitseko ziwiri. 24Chitseko chilichonse chinali ndi zigawo ziwiri zopatukana. 25Ndipo pa zitsekopo anajambulipo zithunzi za akerubi ndi kanjedza monga zomwe anajambulapo pa makoma. Kunja kwake kunali ngati denga lamatabwa pamwamba pa khonde lamʼkati. 26Pa mbali zonse za khonde lamʼkatilo panali mazenera, ndipo pa makoma ake onse anajambulapo zithunzi za kanjedza.

Священное Писание

Езекиил 41:1-26

1Он привёл меня в святилище и измерил опоры входа; они были по три метра41:1 Букв.: «шесть локтей». толщиной 2и по два с половиной метра шириной. Ширина входа равнялась пяти метрам. Он измерил святилище: оно было двадцать метров в длину и десять41:2 Букв.: «пять… десять… сорок… двадцать локтей». в ширину.

3Он прошёл святилище и измерил опоры входа у дальней комнаты; они были по одному метру толщиной и по три с половиной метра шириной. Ширина входа равнялась трём метрам41:3 Букв.: «два… семь… шесть локтей».. 4Он измерил дальнюю комнату: она была десять метров41:4 Букв.: «двадцать локтей»; также в ст. 10. в длину и десять в ширину.

Он сказал мне:

– Это Святая Святых.

5Он измерил стену храма. Она была три метра в толщину, и все боковые комнаты вокруг храма были по два метра41:5 Букв.: «шесть… четыре локтя». в ширину. 6Они располагались на трёх этажах, одна над другой, по тридцать на каждом этаже. По всей стене храма были сделаны выступы, которые служили опорами боковым комнатам, чтобы они не опирались на стены храма. 7Боковые комнаты вокруг храма расширялись с каждым последующим этажом. Сооружение, которое окружало храм, было построено восходящими ярусами, и комнаты, поднимаясь, расширялись. С нижнего этажа через средний на верхний вела лестница.

8Я видел, что храм стоит на приподнятой платформе, которая также служила основанием для боковых комнат. Она была высотой три метра41:8 Букв.: «в одну трость, шесть долгих локтей».. 9Наружная стена боковых комнат была толщиной в два с половиной метра41:9 Букв.: «пять локтей»; также в ст. 11.. Открытое пространство между боковыми комнатами храма 10и комнатами священнослужителей равнялось десяти метрам в ширину вокруг всего храма. 11В боковые комнаты можно было попасть с открытого пространства через входы, располагавшиеся на северной и южной сторонах. Вокруг комнат платформа выступала на два с половиной метра.

12Во дворе храма с западной стороны стояло здание, имевшее тридцать пять метров в ширину и сорок пять метров в длину. Толщина стены здания везде равнялась двум с половиной метрам41:12 Букв.: «семьдесят… девяносто… пять локтей»..

13Затем он измерил храм. Он был пятьдесят метров41:13 Букв.: «сто локтей»; также в ст. 14 и 15. в длину. Задний двор храма, включая западное здание со стенами, тоже имел пятьдесят метров в длину. 14И ширина храмового двора на востоке, включая сам храм и пространства по бокам, равнялась пятидесяти метрам.

15Он измерил длину здания, обращённого во двор позади храма, с его галереями по обеим сторонам; она составляла пятьдесят метров.

Святилище, дальняя комната и притвор, выходивший во двор, 16а также пороги, узкие окна и три этажа боковых комнат – всё позади и порог были отделаны деревом. Пол, стена до окон и окна были отделаны деревом. 17Изнутри стены храма вплоть до простенка над дверными косяками были сплошь покрыты резьбой: 18херувимами и пальмами. Пальмы чередовались с херувимами. У каждого херувима было по два лица: 19человеческое лицо, обращённое к пальме, с одной стороны, и львиное лицо, обращённое к пальме, – с другой. Так было сделано по всему храму. 20Херувимы и пальмы были вырезаны на стене святилища от пола до простенка над входом.

21Дверные косяки у входа в храм имели прямоугольную форму, и те, что были перед входом в Святая Святых, имели ту же форму. 22И был деревянный жертвенник длиной и шириной в один метр, а высотой в полтора метра41:22 Букв.: «два… три локтя».; его рога, основание41:22 Или: «длина». и бока были из дерева.

И он сказал мне:

– Это и есть стол, что стоит перед Вечным.

23И у святилища, и у Святая Святых двери были двойные. 24У каждой двери было по две створки, по две створки на петлях у каждой двери. 25А на внешних дверях храма были вырезаны херувимы и пальмы, как и на стенах, и перед притвором был деревянный навес. 26В боковых стенах притвора были узкие окна, и на обеих стенах были вырезаны пальмы. Над боковыми комнатами храма тоже были деревянные навесы.