Ezekieli 4 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 4:1-17

Chionetsero cha Kuzingidwa kwa Yerusalemu

1Mulungu anati, “Iwe mwana wa munthu, tsopano tenga njerwa, uliyike pamaso pako ndipo ujambulepo chithunzi cha mzinda wa Yerusalemu. 2Ndipo uwuzinge mzindawo motere: uwumangire nsanja zowuzinga, uwumbire mitumbira ya nkhondo, uwumangire misasa ya nkhondo ndipo uyike zida zogumulira kuzungulira mzindawo. 3Kenaka utenge chiwaya chachitsulo uchiyike ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mzindawo. Uyangʼanitsitse mzindawo ndipo udzakhala wozingidwa ndi nsanja za nkhondo. Choncho umangire nsanja zankhondo. Chimenechi chidzakhala chizindikiro kwa Aisraeli.

4“Tsono iwe ugonere kumanzere kwako ndipo ndidzayika pa iwe tchimo la Aisraeli. Iwe udzasenza tchimolo masiku onse amene udzagonere mbali imeneyo. 5Ine ndakuyikira masiku okwana 390 malingana ndi zaka za machimo awo. Umu ndi mmene udzasenzere machimo a Aisraeli.

6“Utatha zimenezo udzagonerenso mbali ya kudzanja lamanja, ndipo udzasenza machimo a anthu a ku Yuda masiku makumi anayi, tsiku lililonse kuyimira chaka chimodzi. 7Tsono udzayangʼanitsitse nsanja za nkhondo zozinga. Dzanja la mkanjo wako utalikwinya ndi dzanja lako utakweza, udzalosere modzudzula Yerusalemu. 8Ine ndidzakumanga ndi zingwe kotero kuti sudzatha kutembenukira uku ndi uku mpaka utatsiriza masiku akuzingidwa ako.

9“Tsono tenga tirigu ndi barele, nyemba ndi mphodza, mapira ndi mchewere; ndipo uyike zonsezi mʼmbale imodzi ndipo upange buledi wako. Uzidya pa masiku 390 amene udzakhala ukugonera mbali imodzi. 10Uyeze theka la kilogalamu la chakudyacho kuti uzidya tsiku lililonse kamodzi kokha. 11Uyezenso zikho ziwiri zamadzi ndipo uzimwa tsiku ndi tsiku. 12Uzidya chakudya chako ngati momwe amadyera keke ya barele. Uzidzaphika chakudyacho anthu akuona pogwiritsa ntchito ndowe ya munthu ngati nkhuni.” 13Yehova anati, “Chimodzimodzi anthu a Israeli adzadya chakudya chodetsedwa ku mayiko achilendo kumene Ine ndidzawapirikitsira.”

14Koma ine ndinati, “Zisatero, Ambuye Yehova! Ine sindinadziyipitsepo pa zachipembedzo. Kuyambira ubwana wanga mpaka tsopano, sindinadyepo kanthu kalikonse kopezeka katafa kapena kophedwa ndi zirombo za kutchire. Palibe nyama yodetsedwa pa zachipembedzo imene inalowa pakamwa panga.”

15Iye anati, “Chabwino, ndidzakulola kuti uphike buledi wako ndi ndowe za ngʼombe mʼmalo mwa ndowe za munthu.”

16Pambuyo pake anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Yerusalemu ndidzawachepetsera chakudya. Anthuwo adzadya chakudya chochita kuyeza ndipo azidzadya mwa nkhawa. Azidzamwanso madzi ochita kuyeza ndiponso mwa mantha. 17Ndidzachita zimenezi kuti adzasowe chakudya ndi madzi. Choncho adzachita nkhawa akumapenyana ndipo adzatheratu ndi kuwonda chifukwa cha machimo awo.”