Ezekieli 34 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 34:1-31

Abusa a Israeli

1Yehova anandiyankhula kuti: 2“Iwe mwana wa munthu, yankhula mawu oyimba mlandu abusa a Israeli. Lengeza ndipo uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Tsoka kwa abusa a Israeli amene mumangodzisamala nokha! Kodi abusa sayenera kusamalira nkhosa? 3Mumadya chambiko, mumadziveka zovala zaubweya, ndi kupha nyama zonenepa, koma simusamalira nkhosazo. 4Simunalimbitse nkhosa zofowoka, kapena kuchiritsa zodwala, kapena kumanga mabala a nkhosa zopweteka. Simunabweze zosochera kapena kufunafuna zotayika. Munaziweta mozunza ndi mwankhanza. 5Kotero zinabalalika chifukwa zinalibe mʼbusa, ndipo pamene zinabalalika zinakhala chakudya cha zirombo zonse zakuthengo. 6Nkhosa zanga zinayendayenda mʼmapiri onse ndi mʼzitunda zonse zazitali. Zinabalalika pa dziko lonse lapansi, ndipo palibe amene anazilondola kapena kuzifunafuna.

7“ ‘Choncho Inu abusa, tamvani zimene Ine Yehova ndikukuwuzani. 8Pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Wamphamvuzonse, ndithu, nkhosa zanga zinajiwa ndi zirombo zakuthengo, zinasanduka chakudya cha zirombo chifukwa panalibe abusa. Abusa anga sanafunefune nkhosa zanga. Iwo ankangosamala za iwo okha mʼmalo mosamala nkhosa zanga. 9Chifukwa chake, inu abusa, tamvani zimene Ine Yehova ndikukuwuzani. 10Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndayipidwa nanu, inu abusa. Ndidzakulandani nkhosa zanga ndipo simudzazidyetsanso. Ndidzakuchotsani pa ntchito ya ubusa kuti musamangodzidyetsa nokha. Ndidzalanditsa nkhosa zanga kukamwa kwanu ndipo simudzazidyanso.

11“ ‘Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti, mwini wakene ndidzazifunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira. 12Monga mʼbusa amanka nafunafuna nkhosa zake pamene zina zabalalikira kutali, moteronso Ine ndidzafunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa kuchoka kumalo onse kumene zinabalalikira pa nthawi yankhungu ndi mdima. 13Ndidzazitulutsa pakati pa mitundu ya anthu ndi kuzisonkhanitsa kuchokera ku mayiko ena, ndipo ndidzazibwezera ku dziko lawo. Ndidzaziwetera ku mapiri a Israeli, mʼmbali mwa mitsinje ndi kumalo kumene kumakhala anthu. 14Ndidzaziwetera kumalo a msipu wabwino. Mapiri okwera a Israeli adzakhala malo azidyetserako. Kumeneko zidzapumula ku abusa abwino a msipu ndipo zizidzadyadi msipu wonenepetsa pa mapiri a Israeli. 15Ine mwini wake ndidzaziweta nkhosa zanga ndi kuzilola kuti zipumule. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 16Ndidzafunafuna zotayika ndi kubweza zosochera. Ndidzamanga mabala a zopweteka ndi kulimbikitsa zofowoka. Koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaweta nkhosazo mwachilungamo.

17“ ‘Kunena za inu, nkhosa zanga, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ndi nkhosa, pakati pa nkhosa zazimuna ndi mbuzi zazimuna. 18Kodi sikukukwanirani kudya msipu wabwino kuti muzichita kuponderezanso msipu umene simunadyewo? Kodi simukhutira ndi kumwa madzi abwino kuti muzinka mudetsanso madzi otsalawo ndi mapazi anu? 19Kodi nkhosa zanga zidye zimene mwazipondaponda ndi kumwa madzi amene mwawadetsa ndi mapazi anu?

20“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Taonani, Ine mwini wake ndidzaweruza pakati pa nkhosa zonenepa ndi nkhosa zowonda. 21Popeza zofowoka mumaziwomba ndi kuzikankhira kumbali, ndipo mumazigunda ndi nyanga zanu nʼkuzimwazira kutali, 22tsono Ine ndidzapulumutsa nkhosa zanga, ndipo sindidzalolanso kuti zijiwe. Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ina ndi nkhosa inanso. 23Ndidzaziyikira mʼbusa mmodzi, mtumiki wanga Davide. Iyeyo ndiye azidzazisamala. Adzakhala mʼbusa wawo. 24Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wake ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu pakati pa nkhosazo. Ine Yehova ndayankhula.

25“ ‘Ndidzapangana nazo pangano la mtendere. Ndidzachotsa mʼdzikomo zirombo zolusa. Choncho nkhosa zanga zidzakhala mu mtendere mu chipululu ngakhalenso mʼthengo. 26Ndidzakhazika anthu anga pafupi ndi phiri langa loyera ndipo ndidzawadalitsa. Ndidzawagwetsera mvula pa nthawi yake ndipo idzakhala mvula ya madalitso. 27Mitengo ya mʼminda idzabereka zipatso zake, ndipo nthaka idzakhala ndi zokolola zake. Anthu adzakhala mwamtendere mʼdziko lawo. Iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene ndidzathyola magoli awo ndi kuwapulumutsa kuchoka mʼmanja mwa amene anawagwira ukapolo. 28Anthu amitundu ina sadzawafunkhanso ndipo sadzadyedwa ndi zirombo zakuthengo. Adzakhala mwamtendere ndipo palibe amene adzawaopseze. 29Ndidzawapatsa zokolola zochuluka motero kuti sadzavutikanso ndi njala. Anthu a mitundu ina sadzawanyozanso. 30Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wawo ndili nawo pamodzi, ndipo kuti iwo, Aisraeli, ndi anthu anga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 31Inu ndinu nkhosa zanga, nkhosa zimene ndimazidyetsa. Ine ndine Mulungu wanu. Ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse.’ ”