Mkungudza mu Lebanoni
1Pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu, chaka cha khumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti: 2“Iwe mwana wa munthu, unene kwa Farao mfumu ya Igupto ndi gulu lake lankhondo. Awawuze kuti,
“ ‘Kodi mu ukulu wanu ndani angafanane ndi inu?
3Taonani, ndidzakufanizirani ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni,
wa nthambi zokongola zochititsa mthunzi mʼnkhalango.
Unali wautali,
msonga zake zooneka pamwamba pa nkhalango.
4Madzi ndiwo ankawukulitsa mkungudzawo,
akasupe ozama ankawutalikitsa.
Mitsinje yake inkayenda
mozungulira malo amene unaliwo
ndipo ngalande zake zinkafika
ku mitengo yonse ya mʼmunda.
5Choncho unatalika kwambiri
kupambana mitengo yonse ya mʼmunda.
Nthambi zake zinachuluka
ndi kutalika kwambiri,
chifukwa inkalandira madzi ambiri.
6Mbalame zonse zamlengalenga
zinkamanga zisa zake mʼnthambi za mtengowo.
Nyama zakuthengo zonse
zinkaswanirana mʼmunsi mwa nthambi zake.
Mitundu yotchuka ya anthu
inkakhala mu mthunzi wake.
7Unali wokongola kwambiri,
wa nthambi zake zotambalala,
chifukwa mizu yake inazama pansi
kumene kunali madzi ochuluka.
8Mʼmunda wa Mulungu munalibe
mkungudza wofanana nawo,
kapena mitengo ya payini
ya nthambi zofanafana ndi nthambi zake.
Munalibenso mtengo wa mkuyu
nthambi zofanafana ndi zake.
Mʼmunda wa Mulungu munalibe mtengo wina uliwonse
wofanana ndi iwo kukongola kwake.
9Ine ndinawupanga wokongola
wa nthambi zochuluka.
Mitengo yonse ya mu Edeni, mʼmunda wa
Mulungu inawuchitira nsanje.
10“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Chifukwa kuti mtengowo unatalika kwambiri, unatulutsa songa zake mpaka ku thambo, ndipo unadzikweza chifukwa cha msinkhu wake, 11ndinawupereka mʼdzanja la mfumu ya mitundu ya anthu kuti awulange molingana ndi kuyipa kwake. 12Anthu ankhanza kwambiri amitundu ya anthu achilendo adzawudula ndi kuwusiya. Nthambi zake zidzagwera pa mapiri ndi mu zigwa zonse. Nthambi zake zidzathyokera mʼmitsinje ya mʼdzikomo. Motero mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi amene ankasangalala mu mthunzi wake idzawusiya. 13Mbalame zonse zamlengalenga zidzakhala pa mtengo wakugwawo, ndipo nyama zakuthengo zonse zidzakhala pa nthambi zake. 14Zidzakutero kuti pasakhalenso mitengo inanso ya mʼmbali mwa madzi yotalika kwambiri, imene idzatalike kwambiri ndi songa zake kufika mpaka ku mitambo. Komanso kuti pasadzakhalenso mitengo yolandira bwino madzi, imene idzatalika motero. Paja yonseyo kutha kwake ndi kufa, kupita ku dziko lapansi kukhala ndi anthu akufa amene analowa mʼmanda kale.
15“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene mkungudzawo unatsikira ku manda, ndinawuza nyanja kuti iwulire maliro pakuwuphimba. Ndinawumitsa mitsinje ndipo madzi ambiri anaphwa. Ndinabweretsa mdima pa Lebanoni chifukwa cha mtengowo ndipo mitengo yonse ya mʼdzikomo inawuma. 16Mitundu ya anthu inagwedezeka pakumva mkokomo wa kugwa kwake, pamene ndinawutsitsira ku manda pamodzi ndi iwo amene anafa. Pamenepo ku dziko la akufa mitengo yonse ya ku Edeni pamodzi ndi ya ku Lebanoni yosankhidwa bwino inasangalatsidwa chifukwa cha zimenezi. 17Amene ankakhala mu mthunzi wake, amene ankayanjana nawo, iwonso anapita nawo pamodzi ku manda, kukakhala pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu.
18“ ‘Ndi mitengo iti ya mu Edeni imene ingafanane ndi kukongola kwako ndi ulemerero wako? Komabe iwenso, udzatsikira ku dziko la anthu akufa pamodzi ndi mitengo ya mu Edeni. Udzagona pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, anthu amene anaphedwa pa nkhondo.
“ ‘Mtengowo ndi Farao ndi gulu lake lankhondo, akutero Ambuye Yehova.’ ”
El cedro del Líbano
1El día primero del mes tercero del año undécimo, el Señor me dirigió la palabra: 2«Hijo de hombre, dile al faraón, rey de Egipto, y a toda su gente:
»“¿Quién se puede comparar con tu grandeza?
3Fíjate en Asiria,
que alguna vez fue cedro del Líbano,
con bello y frondoso ramaje;
su copa sobresalía del espeso follaje.
4Las aguas lo hicieron crecer;
las corrientes profundas lo nutrieron.
Sus ríos corrían
en torno a sus raíces;
sus acequias regaban
todos los árboles del campo.
5Así el cedro creció
más alto que todos los árboles del campo.
Gracias a las abundantes aguas,
se extendió su frondoso ramaje.
6Todas las aves del cielo
anidaban en sus ramas.
Todas las bestias del campo
tenían sus crías bajo su follaje.
Todas las naciones
vivían bajo su sombra.
7Era un árbol imponente y majestuoso,
de ramas extendidas;
sus raíces se hundían
hasta las aguas caudalosas.
8Ningún cedro en el jardín de Dios
se le podía comparar;
ningún ciprés ostentaba un follaje parecido
ni tenían su ramaje los castaños.
Ningún árbol del jardín de Dios
se le comparaba en hermosura.
9Yo lo hice bello
y con un ramaje majestuoso.
En el Edén, jardín de Dios,
era la envidia de todos los árboles.
10»”Por eso, así dice el Señor y Dios: Por cuanto el árbol creció tan alto y ufano de su altura, y se elevaba sobre el espeso follaje, 11yo lo he desechado; lo entregué en manos de un líder de naciones, para que lo trate según su maldad. 12Los extranjeros más crueles lo han talado y abandonado. Sus ramas han caído en los montes y en los valles; yacen rotas por todos los canales de los ríos del país. Huyeron y lo abandonaron todas las naciones que buscaban protección bajo su sombra. 13Ahora las aves del cielo se posan sobre su tronco caído y las bestias del campo se meten entre sus ramas. 14Y esto es para que ningún árbol que esté junto a las aguas vuelva a crecer tanto; para que ningún árbol, por bien regado que esté, vuelva a elevar su copa hasta las nubes. Todos están destinados a la muerte, a bajar a las regiones profundas de la tierra y quedarse entre los mortales que descienden a la fosa.
15»”Así dice el Señor y Dios: El día en que el cedro bajó a los dominios de la muerte,31:15 a los dominios de la muerte. Lit. al Seol. cubrí de luto las profundidades de las aguas. Detuve sus corrientes y contuve sus ríos; por él vestí de luto al Líbano y todos los árboles del campo se marchitaron. 16Cuando lo hice descender a los dominios de la muerte, junto con los que bajan a la fosa, con el estruendo de su caída hice temblar a las naciones. Todos los árboles del Edén, los más selectos y hermosos del Líbano, los que estaban mejor regados, se consolaron en las regiones subterráneas. 17Sus aliados entre las naciones que buscaban protección bajo su sombra también descendieron a los dominios de la muerte, junto con los que habían muerto a filo de espada.
18»”¿A cuál de los árboles del Edén se puede comparar contigo en esplendor y majestad? No obstante, también él descendió con los árboles del Edén a las regiones subterráneas. Allí quedó tendido en medio de los incircuncisos, junto con los que murieron a filo de espada.
»”¡Y así será la muerte del faraón y de todos sus súbditos!, afirma el Señor y Dios”».