Ezekieli 31 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 31:1-18

Mkungudza mu Lebanoni

1Pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu, chaka cha khumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti: 2“Iwe mwana wa munthu, unene kwa Farao mfumu ya Igupto ndi gulu lake lankhondo. Awawuze kuti,

“ ‘Kodi mu ukulu wanu ndani angafanane ndi inu?

3Taonani, ndidzakufanizirani ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni,

wa nthambi zokongola zochititsa mthunzi mʼnkhalango.

Unali wautali,

msonga zake zooneka pamwamba pa nkhalango.

4Madzi ndiwo ankawukulitsa mkungudzawo,

akasupe ozama ankawutalikitsa.

Mitsinje yake inkayenda

mozungulira malo amene unaliwo

ndipo ngalande zake zinkafika

ku mitengo yonse ya mʼmunda.

5Choncho unatalika kwambiri

kupambana mitengo yonse ya mʼmunda.

Nthambi zake zinachuluka

ndi kutalika kwambiri,

chifukwa inkalandira madzi ambiri.

6Mbalame zonse zamlengalenga

zinkamanga zisa zake mʼnthambi za mtengowo.

Nyama zakuthengo zonse

zinkaswanirana mʼmunsi mwa nthambi zake.

Mitundu yotchuka ya anthu

inkakhala mu mthunzi wake.

7Unali wokongola kwambiri,

wa nthambi zake zotambalala,

chifukwa mizu yake inazama pansi

kumene kunali madzi ochuluka.

8Mʼmunda wa Mulungu munalibe

mkungudza wofanana nawo,

kapena mitengo ya payini

ya nthambi zofanafana ndi nthambi zake.

Munalibenso mtengo wa mkuyu

nthambi zofanafana ndi zake.

Mʼmunda wa Mulungu munalibe mtengo wina uliwonse

wofanana ndi iwo kukongola kwake.

9Ine ndinawupanga wokongola

wa nthambi zochuluka.

Mitengo yonse ya mu Edeni, mʼmunda wa

Mulungu inawuchitira nsanje.

10“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Chifukwa kuti mtengowo unatalika kwambiri, unatulutsa songa zake mpaka ku thambo, ndipo unadzikweza chifukwa cha msinkhu wake, 11ndinawupereka mʼdzanja la mfumu ya mitundu ya anthu kuti awulange molingana ndi kuyipa kwake. 12Anthu ankhanza kwambiri amitundu ya anthu achilendo adzawudula ndi kuwusiya. Nthambi zake zidzagwera pa mapiri ndi mu zigwa zonse. Nthambi zake zidzathyokera mʼmitsinje ya mʼdzikomo. Motero mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi amene ankasangalala mu mthunzi wake idzawusiya. 13Mbalame zonse zamlengalenga zidzakhala pa mtengo wakugwawo, ndipo nyama zakuthengo zonse zidzakhala pa nthambi zake. 14Zidzakutero kuti pasakhalenso mitengo inanso ya mʼmbali mwa madzi yotalika kwambiri, imene idzatalike kwambiri ndi songa zake kufika mpaka ku mitambo. Komanso kuti pasadzakhalenso mitengo yolandira bwino madzi, imene idzatalika motero. Paja yonseyo kutha kwake ndi kufa, kupita ku dziko lapansi kukhala ndi anthu akufa amene analowa mʼmanda kale.

15“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene mkungudzawo unatsikira ku manda, ndinawuza nyanja kuti iwulire maliro pakuwuphimba. Ndinawumitsa mitsinje ndipo madzi ambiri anaphwa. Ndinabweretsa mdima pa Lebanoni chifukwa cha mtengowo ndipo mitengo yonse ya mʼdzikomo inawuma. 16Mitundu ya anthu inagwedezeka pakumva mkokomo wa kugwa kwake, pamene ndinawutsitsira ku manda pamodzi ndi iwo amene anafa. Pamenepo ku dziko la akufa mitengo yonse ya ku Edeni pamodzi ndi ya ku Lebanoni yosankhidwa bwino inasangalatsidwa chifukwa cha zimenezi. 17Amene ankakhala mu mthunzi wake, amene ankayanjana nawo, iwonso anapita nawo pamodzi ku manda, kukakhala pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu.

18“ ‘Ndi mitengo iti ya mu Edeni imene ingafanane ndi kukongola kwako ndi ulemerero wako? Komabe iwenso, udzatsikira ku dziko la anthu akufa pamodzi ndi mitengo ya mu Edeni. Udzagona pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, anthu amene anaphedwa pa nkhondo.

“ ‘Mtengowo ndi Farao ndi gulu lake lankhondo, akutero Ambuye Yehova.’ ”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以西结书 31:1-18

香柏树的比喻

1第十一年三月一日,耶和华对我说: 2“人子啊,你要对埃及王法老和他的百姓说,

“‘谁能比你强大呢?

3看啊,亚述曾是黎巴嫩的一棵香柏树,

枝繁叶茂,遮天蔽日,

高耸入云。

4它在河流和深泉的滋润下茁壮成长,

溪流四围环绕它,

浇灌着林间的树木。

5充足的水源使它高过田间所有的树木,

枝子长得又粗又长。

6空中的飞鸟都在它的枝头上搭窝,

田间的野兽都在它的树荫下生产,

所有的大国都住在它的荫下。

7它高大美丽,枝干修长,

因为树根深入水源,

8连上帝园中的香柏树也不能与它相比。

松树不能与它的枝干相比,

枫树不能与它的枝条相比,

主耶和华园中的树木没有一棵能与它媲美。

9我使它枝繁叶茂,美丽无比,

以致上帝伊甸园里的树木都羡慕它。’

10“因此,主耶和华说,‘因为它树干高大,树梢高耸入云,心高气傲, 11我要把它交在列国的首领手里,他必按照它的邪恶惩治它。我丢弃了它。 12外族人,就是列邦中最残暴的人要把它砍倒,丢弃在那里,它折断的枝干散落在山间和河谷中。世上各族都离开它的荫下, 13天上的飞禽要栖身在那折断的树干上,地上的走兽要躺卧在它的枝条中。 14故此,水边的树木都不再傲然矗立,高耸入云,水源充足的大树也不再如此高大,因为它们都注定要与下坟墓的人一同死亡,落到阴间的深处。’

15“主耶和华说,‘它下到阴间的那天,我要使哀声响起,使深渊闭塞,江河止息,洪水停滞。我要使黎巴嫩为它哀哭,田野的树木因它而枯萎。 16我将它与下坟墓的人一同抛到阴间时,列国听见它坠落的响声,都恐惧战抖。伊甸园中的树木和黎巴嫩水源充足、上好的树木都在阴间得到安慰。 17在它荫庇下做它爪牙的盟友都与它一同落到阴间,到被杀的人那里。

18“‘伊甸园的树木中,谁能与你的威荣相比呢?然而你却要与伊甸园的树木一同下到阴间,躺卧在未受割礼的人当中,与被杀的人在一起。

“‘这就是法老和他百姓的结局。这是主耶和华说的。’”