Ezekieli 3 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 3:1-27

1Tsono Mulungu anandiwuza kuti, “Mwana wa munthu, idya chimene ndikukupatsachi. Idya kenaka upite ukayankhule ndi Aisraeli.” 2Choncho ndinayasama ndipo anandipatsa mpukutuwo kuti ndidye.

3Kenaka Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, idya mpukutu umene ndikukupatsa kuti ukhute.” Choncho ndinadya, ndipo unkatsekemera ngati uchi mʼkamwa mwanga.

4Pamenepo Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, pita tsopano kwa Aisraeli ndipo ukawawuze mawu anga. 5Sindikukutuma kwa anthu oyankhula chiyankhulo chachilendo ndi chovuta, koma kwa Aisraeli. 6Sindikukutuma kwa mitundu yambiri ya anthu oyankhula chiyankhulo chachilendo ndi chovuta, amene mawu ake sungawamvetse. Ndithu ndikanakutuma kwa iwowa, bwenzi iwo atakumvera. 7Koma Aisraeli sadzakumvera chifukwa iwo sakufuna kumvera Ine. Paja Aisraeli onse ndi okanika ndiponso a mtima wowuma. 8Tsono ine ndakhwimitsa nkhope yako mofanana ndi nkhope zawo. Ndalimbitsanso mutu wako mofanana ndi mitu yawo. 9Ine ndidzakusandutsa wolimba ngati mwala wa dayimondi umene uposa thanthwe lina lililonse kulimba kwake. Usachite nawo mantha kapena kuopsedwa nawo. Paja anthuwa ndi awupandu.”

10Anatinso, “Iwe mwana wa munthu, umvetsetse bwino zimene ndikukuwuzazi ndipo mawu angawa uwasunge bwino mu mtima mwako. 11Tsopano upite kwa Aisraeli anzako amene ali ku ukapolo ndipo ukayankhule nawo. ‘Kaya akamvera kaya sakamvera,’ koma uzikawawuza kuti, Ambuye Wamphamvuzonse akuti zakutizakuti.”

12Pamenepo Mzimu unandinyamula ndipo kumbuyo kwanga ndinamva liwu lamphamvu ngati chivomerezi chachikulu, lonena kuti, “Utamandike ulemerero wa Yehova kumene Iye amakhala!” 13Phokoso ndinkalimvalo linali la kugundana kwa mapiko a zamoyo ndiponso phokoso la mikombero ya pambali pake ija, limene linkamveka ngati chivomerezi chachikulu. 14Mzimu wa Yehova unandikweza ndi kundinyamula ndipo ndinachokapo ndili wowawidwa ndi wonyuka mu mtima. Ndipo dzanja la Yehova linali pa ine mwa mphamvu. 15Choncho ndinafika kwa amene anali mu ukapolo ku Telabibu pafupi ndi mtsinje wa Kebara. Ndinakhala pansi pakati pawo masiku asanu ndi awiri, ndili wothedwa nzeru kwambiri.

Chenjezo kwa Israeli

16Atatha masiku asanu ndi awiriwo, Yehova anandiwuza kuti, 17“Iwe mwana wa munthu, Ine ndakuyika kuti ukhale mlonda wa Aisraeli. Uziti ukamva mawu anga, ndiye uzikawachenjeza. 18Ndikawuza munthu woyipa kuti, ‘Iwe udzafa ndithu,’ koma iwe osamuchenjeza kapena kumuyankhula kuti aleke njira zake zoyipa ndi kuti akhale ndi moyo, munthu woyipayo adzafa mu uchimo wake, koma Ine ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake. 19Koma ukamuchenjeza munthu woyipa koma iye osatembenuka mtima kuleka zoyipa zake kapena kusiya njira zake zoyipa, munthuyo adzafa chifukwa cha uchimo wake koma iwe udzapulumutsa moyo wako.

20“Ngati munthu wolungama asiya chilungamo chake ndi kuchita uchimo ndipo Ine nʼkumuyika mʼzoopsa, munthuyo adzafa ndithu. Popeza iwe sunamuchenjeze, adzafadi chifukwa cha tchimo ndipo chilungamo chake sichidzakumbukiridwa, koma ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake. 21Koma ngati umuchenjeza munthu wolungama kuti asachimwe ndipo iye nʼkuleka kuchimwa adzakhala ndi moyo ndithu chifukwa anamvera chenjezo, ndipo iwe udzapulumutsa moyo wako.”

22Nthawi ina dzanja la Yehova linali pa ine ndipo anandiwuza kuti, “Nyamuka upite ku chigwa, kumeneko ndikayankhula nawe.” 23Choncho ndinanyamuka kupita ku chigwa. Ndipo ndinaona ulemerero wa Yehova kumeneko, ngati ulemerero umene ndinaona mʼmbali mwa mtsinje wa Kebara ndipo ndinagwa pansi chafufumimba.

24Koma Mzimu wa Mulungu unalowa mwa ine ndipo unandiyimiritsa. Tsono Yehova anandiyankhula nati: “Pita, kadzitsekere mʼnyumba mwako. 25Ndipo iwe mwana wa munthu, adzakumanga ndi zingwe motero kuti sudzatha kuyendanso pakati pa anthu. 26Ndidzamatirira lilime lako kukhosi, kotero kuti udzakhala chete wosatha kuwadzudzula, chifukwa iwo ndi anthu aupandu. 27Koma pamene ndidzayankhula kwa iwe, ndidzatsekula pakamwa pako ndipo udzawawuza kuti, ‘Ambuye Yehova akuti zakutizakuti.’ Aliyense wofuna kumva amve ndipo wokana kumva, muleke akane; pakuti iwo ndi anthu opanduka.”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以西结书 3:1-27

1祂对我说:“人子啊,你要把得到的吃下去,要吃下这书卷,然后去向以色列人传讲。” 2我张开口,祂就给我吃那书卷, 3对我说:“吃下我赐你的这书卷,让它充满你的肚腹。”我便吃了,书卷在我嘴里甘甜如蜜。

4祂又对我说:“人子啊,现在你要到以色列人那里,把我的话传给他们。 5你不是奉命去语言不通的民族那里,而是到以色列人当中。 6我不是派你到那些语言陌生、难懂、你听不明白的民族中。我若果真派你到他们那里,他们一定会听你的话。 7然而以色列人却不肯听从你,因为他们顽固不化,不肯听从我。 8不过,我要使你的脸像他们的脸一样硬,使你的额像他们的额一样硬。 9我要使你的额比火石更硬,如同金刚石。他们虽然是一群叛逆的人,你不要害怕,也不要因为他们的脸色而惊慌。” 10祂又说:“人子啊,你要留心听我说的一切话,牢记在心。 11你要到你那些被掳的同胞那里,不论他们听不听,你都要向他们宣告,‘主耶和华这样说。’”

12那时,灵把我举起,我听见后面有隆隆的声音说:“耶和华的荣耀在祂的居所当受称颂!” 13我听见活物的翅膀相碰的声音,以及他们旁边的轮子发出的隆隆声。 14灵把我举起带走了。我心里苦闷,充满愤怒,耶和华大能的手在我身上。 15我来到住在提勒·亚毕的被掳的人中,在迦巴鲁河边。我感到无比震惊,在他们中间坐了七天。

告诫以色列人

16过了七天,耶和华对我说: 17“人子啊,我立你做以色列人的守望者,你要把我告诫他们的话告诉他们。 18当我说某个恶人必灭亡时,如果你不告诫他,劝告他痛改前非,挽救他的性命,他必死在自己的罪中,而我要追究你的责任。 19如果你已经告诫他,他还是不肯离开自己的邪恶和罪行,他必死在罪恶之中,而你必免于罪责。 20如果一个义人偏离正道、犯罪作恶,我会使他跌倒,他必死亡。如果你不告诫他,他必死在罪恶之中,他以前的义行也不会被记念,而我要追究你的责任。 21如果你告诫他不要犯罪,他听了你的告诫不再犯罪,他必保住性命,你也必免于罪责。”

22在那里,耶和华的手按在我身上,对我说:“你起来前往平原,我要在那里对你说话。” 23我到了平原,看见耶和华的荣耀停在那里,那荣耀和我在迦巴鲁河边所见的一样,我就俯伏在地。 24这时灵进入我里面,使我站立起来。耶和华对我说:“你要把自己关在房子里。 25人子啊,他们必把你捆绑起来,使你不能到百姓当中。 26同时,我要使你的舌头紧贴上膛,使你不能开口责备他们,因为他们是一群叛逆的人。 27但当我对你说话的时候,我必开启你的口,你要向他们宣告,‘主耶和华这样说。’肯听的就让他听,不肯听的就由他不听,因为他们是一群叛逆的人。”