Ezekieli 29 – CCL & NIV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 29:1-21

Za Chilango cha Igupto

1Pa tsiku lakhumi ndi chiwiri la mwezi wakhumi, chaka chakhumi, Yehova anandiyankhula kuti: 2“Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa Farao, mfumu ya Igupto, ndipo unenere modzudzula mfumuyo pamodzi ndi dziko lake. 3Uyiwuze mfumuyo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Ndine mdani wako, iwe Farao mfumu ya Igupto,

iwe ngʼona yayikulu yogona pakati pa mitsinje yako.

Umanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga;

ndinadzipangira ndekha.’

4Koma ndidzakukola ndi mbedza mʼkamwa mwako

ndipo nsomba za mʼmitsinje yako zidzakangamira ku mamba ako.

Tsono ndidzakutulutsa mu mtsinje mwakomo

pamodzi ndi nsomba zimene zakangamira ku mamba ako.

5Ndidzakutaya ku chipululu,

iwe pamodzi ndi nsomba zonse za mʼmitsinje yako.

Udzagwera pamtetete kuthengo

popanda munthu woti akutole kuti akayike maliro ako.

Ndidzakusandutsa chakudya

cha zirombo za pa dziko lapansi ndi mbalame za mlengalenga.

6Motero aliyense amene amakhala mu Igupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

“ ‘Iwe unakhala ngati ndodo yabango ku Aisraeli. 7Pamene anakugwira unathethekera mʼmanja mwawo ndi kucheka mapewa awo. Pamene anakutsamira, unathyoka ndipo misana yawo inagwedezeka.

8“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, ndikubweretsera lupanga kuti lidzaphe anthu pamodzi ndi nyama zomwe. 9Dziko la Igupto lidzasanduka lopanda anthu. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

“ ‘Popeza iwe unati, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga; ndinawupanga ndine,’ 10nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawe pamodzi ndi mitsinje yakoyo, ndipo ndidzasandutsa dziko la Igupto bwinja kuyambira chipululu cha Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani, kukafika ku malire a Kusi. 11Palibe phazi la munthu kapena la nyama limene lidzapondepo. Kudzakhala kopanda anthu kwa zaka makumi anayi. 12Ndidzasandutsa dziko la Igupto kukhala chipululu ngati zipululu za mayiko ena. Kwa zaka makumi anayi mizinda yakenso idzakhala yopasuka pakati pa mizinda yopasuka. Ndipo ndidzathamangitsira Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndi kuwabalalitsira mʼmayiko.

13“ ‘Komabe Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pakutha pa zaka makumi anayi ndidzasonkhanitsa Aigupto onse kuchokera ku mayiko amene ndinawabalalitsirako. 14Ndidzachotsa Aiguptowo ku ukapolo ndipo ndidzawabwezera ku Patirosi kumene anachokera. Kumeneko iwo adzakhala ufumu wotsika. 15Udzakhala ufumu wotsika kwambiri kupambana maufumu ena onse ndipo sudzadzitukumula pakati pa mitundu ina. Ndidzawufowoketsa kwambiri kotero kuti sudzathanso kulamulira mitundu ya anthu. 16Aisraeli sadzadaliranso Aigupto. Koma kuti chilango chawo chidzawakumbutsa tchimo lawo lija lofunafuna thandizo kuchokera ku Igupto. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.’ ”

Mphotho ya Nebukadinezara

17Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, chaka cha 27, Yehova anandiyankhula kuti: 18“Iwe mwana wa munthu, kale Nebukadinezara mfumu ya Babuloni inagwiritsa ntchito ankhondo ake kukathira nkhondo mzinda wa Turo, mpaka munthu aliyense anachita dazi chifukwa chosenza katundu, ndipo ananyuka pa phewa. Komabe ngakhale iyeyo, kapena gulu lake lankhondo sanaphulepo kanthu pa ntchito yonse imene anayigwira polimbana ndi mzindawo. 19Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndidzapereka Igupto kwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, ndipo iyo idzatenga chuma chake ndi kuchifunkha ngati malipiro a gulu lake lankhondo. 20Ndamupatsa Nebukadinezara Igupto ngati mphotho ya kulimbika kwake chifukwa iyo ndi gulu lake lankhondo anandigwirira ntchito, akutero Ambuye Yehova.

21“Pa nthawi imeneyo ndidzapereka mphamvu yatsopano pa Aisraeli, ndipo ndidzatsekula pakamwa pako, iwe, Ezekieli kuti uthe kuyankhula pakati pawo. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

New International Version

Ezekiel 29:1-21

A Prophecy Against Egypt

Judgment on Pharaoh

1In the tenth year, in the tenth month on the twelfth day, the word of the Lord came to me: 2“Son of man, set your face against Pharaoh king of Egypt and prophesy against him and against all Egypt. 3Speak to him and say: ‘This is what the Sovereign Lord says:

“ ‘I am against you, Pharaoh king of Egypt,

you great monster lying among your streams.

You say, “The Nile belongs to me;

I made it for myself.”

4But I will put hooks in your jaws

and make the fish of your streams stick to your scales.

I will pull you out from among your streams,

with all the fish sticking to your scales.

5I will leave you in the desert,

you and all the fish of your streams.

You will fall on the open field

and not be gathered or picked up.

I will give you as food

to the beasts of the earth and the birds of the sky.

6Then all who live in Egypt will know that I am the Lord.

“ ‘You have been a staff of reed for the people of Israel. 7When they grasped you with their hands, you splintered and you tore open their shoulders; when they leaned on you, you broke and their backs were wrenched.29:7 Syriac (see also Septuagint and Vulgate); Hebrew and you caused their backs to stand

8“ ‘Therefore this is what the Sovereign Lord says: I will bring a sword against you and kill both man and beast. 9Egypt will become a desolate wasteland. Then they will know that I am the Lord.

“ ‘Because you said, “The Nile is mine; I made it,” 10therefore I am against you and against your streams, and I will make the land of Egypt a ruin and a desolate waste from Migdol to Aswan, as far as the border of Cush.29:10 That is, the upper Nile region 11The foot of neither man nor beast will pass through it; no one will live there for forty years. 12I will make the land of Egypt desolate among devastated lands, and her cities will lie desolate forty years among ruined cities. And I will disperse the Egyptians among the nations and scatter them through the countries.

13“ ‘Yet this is what the Sovereign Lord says: At the end of forty years I will gather the Egyptians from the nations where they were scattered. 14I will bring them back from captivity and return them to Upper Egypt, the land of their ancestry. There they will be a lowly kingdom. 15It will be the lowliest of kingdoms and will never again exalt itself above the other nations. I will make it so weak that it will never again rule over the nations. 16Egypt will no longer be a source of confidence for the people of Israel but will be a reminder of their sin in turning to her for help. Then they will know that I am the Sovereign Lord.’ ”

Nebuchadnezzar’s Reward

17In the twenty-seventh year, in the first month on the first day, the word of the Lord came to me: 18“Son of man, Nebuchadnezzar king of Babylon drove his army in a hard campaign against Tyre; every head was rubbed bare and every shoulder made raw. Yet he and his army got no reward from the campaign he led against Tyre. 19Therefore this is what the Sovereign Lord says: I am going to give Egypt to Nebuchadnezzar king of Babylon, and he will carry off its wealth. He will loot and plunder the land as pay for his army. 20I have given him Egypt as a reward for his efforts because he and his army did it for me, declares the Sovereign Lord.

21“On that day I will make a horn29:21 Horn here symbolizes strength. grow for the Israelites, and I will open your mouth among them. Then they will know that I am the Lord.”