Ezekieli 28 – CCL & CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 28:1-26

Mawu Odzudzula Mfumu ya Turo

1Yehova anandiyankhula nati: 2“Iwe mwana wa munthu, iwuze mfumu ya ku Turo mawu a Ine Ambuye Yehova akuti,

“ ‘Iwe ndi mtima wako wodzikuza

umanena kuti, ‘Ine ndine mulungu;

ndimakhala pa mpando wa mulungu

pakati pa nyanja.’

Koma ndiwe munthu chabe osati mulungu,

ngakhale ukuganiza kuti ndiwe wanzeru ngati mulungu.

3Taona, ndiwedi wanzeru kupambana Danieli.

Ndipo palibe chinsinsi chobisika kwa iwe.

4Mwa nzeru zako ndi kumvetsa kwako

unadzipezera chuma

ndipo unasonkhanitsa golide ndi siliva

mʼnyumba zosungira chuma chako.

5Ndi nzeru zako zochitira malonda

unachulukitsa chuma chako

ndipo wayamba kunyada

chifukwa cha chuma chakocho.

6“ ‘Choncho Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Popeza umadziganizira

kuti ndiwe mulungu,

7Ine ndidzabwera ndi anthu achilendo, anthu ankhanza,

kuti adzalimbane nawe.

Adzakuthira nkhondo kuti awononge zonse zimene unazipeza ndi nzeru zako,

ndipo adzawononga kunyada kwakoko.

8Iwo adzakuponyera ku dzenje

ndipo udzafa imfa yoopsa

mʼnyanja yozama.

9Kodi udzanenabe kuti, ‘Ine ndine mulungu,’

pamaso pa iwo amene akukupha?

Iwe udzaoneka kuti ndiwe munthu chabe, osati mulungu,

mʼmanja mwa iwo amene akukuphawo.

10Udzafa imfa ya anthu osachita mdulidwe

mʼmanja mwa anthu achilendo.

Ine ndayankhula zimenezi, akutero Ambuye Yehova.’ ”

11Yehova anandiyankhula kuti: 12“Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yodandaulira mfumu ya Turo ndipo uyiwuze mawu a Ine Ambuye Yehova akuti,

“ ‘Iwe unali chitsanzo cha ungwiro weniweni,

wodzaza ndi nzeru ndi wokongola kwambiri.

13Iwe unkakhala ngati mu Edeni,

munda wa Mulungu.

Miyala yokongola ya mitundu yonse:

rubi, topazi ndi dayimondi,

kirisoliti, onikisi, yasipa,

safiro, kalineliyoni ndi berili ndiwo inali zofunda zako.

Ndipo zoyikamo miyalayo zinali zagolide.

Anakupangira zonsezi pa tsiku limene unalengedwa.

14Ndinayika kerubi kuti azikulondera.

Unkakhala pa phiri langa lopatulika,

ndipo unkayendayenda

pakati pa miyala ya moto.

15Makhalidwe ako anali abwino

kuyambira pamene unalengedwa

mpaka nthawi imene unayamba kuchita zoyipa.

16Unatanganidwa ndi zamalonda.

Zotsatira zake zinali zoti unachulukitsa zandewu

ndi kumachimwa.

Choncho ndinakuchotsa ku phiri langa lopatulika.

Mkerubi amene ankakulondera uja anakupirikitsa

kukuchotsa ku miyala yamoto.

17Unkadzikuza mu mtima mwako

chifukwa cha kukongola kwako,

ndipo unayipitsa nzeru zako

chifukwa chofuna kutchuka.

Kotero Ine ndinakugwetsa pansi

kuti ukhala chenjezo pamaso pa mafumu.

18Ndi malonda ako achinyengo unachulukitsa machimo ako.

Motero unayipitsa malo ako achipembedzo.

Choncho ndinabutsa moto pakati pako,

ndipo unakupsereza,

ndipo unasanduka phulusa pa dziko lapansi

pamaso pa anthu onse amene amakuona.

19Anthu onse amitundu amene ankakudziwa

akuchita mantha chifukwa cha iwe.

Watheratu mochititsa mantha

ndipo sudzakhalaponso mpaka muyaya.’ ”

Za Chilango cha Sidoni

20Yehova anandiyankhula nati: 21“Iwe mwana wa munthu, utembenukire ku mzinda wa Sidoni ndipo unenere mowudzudzula kuti, 22‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Ndine mdani wako, iwe Sidoni,

ndipo ndidzalemekezedwa chifukwa cha iwe.

Anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova

ndikadzakulanga ndi kudzionetsa kuti

ndine woyera pakati pako.

23Ndidzatumiza mliri pa iwe

ndi kuchititsa magazi kuti ayende mʼmisewu yako.

Anthu ophedwa ndi lupanga

adzagwa mbali zonse.

Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

24“ ‘Nthawi imeneyo Aisraeli sadzakhalanso ndi anthu pafupi achipongwe amene ali ngati nthula zowawa ndi ngati minga zopweteka. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

25“ ‘Ine Ambuye Yehova mawu anga ndi awa: Nditasonkhanitsa Aisraeli kuchoka ku mayiko kumene anamwazikira, ndidzadzionetsa kuti ndine woyera pakati pawo pamaso pa anthu a mitundu ina. Adzakhala mʼdziko lawo, limene ndinalipereka kwa mtumiki wanga Yakobo. 26Adzakhala kumeneko mwamtendere ndipo adzamanga nyumba ndi kulima minda ya mpesa. Adzakhala kumeneko mwamtendere pamene ndidzalange anthu oyandikana nawo, amene ankawanyoza. Motero iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo.’ ”