Ezekieli 26 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 26:1-21

Za Chilango cha Turo

1Pa chaka cha khumi ndi chimodzi, tsiku loyamba la mwezi, Yehova anandiyankhula kuti: 2“Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Turo ananyogodola Yerusalemu kuti ‘Hii! Uja amene anali chipata choloweramo anthu a mitundu ina wawonongeka. Zitseko zake zatsekukira ife. Tidzalemera popeza wasanduka bwinja.’ 3Nʼchifukwa chake, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakulangani, inu anthu a ku Turo. Ndidzakuyitanirani anthu a mitundu ina kuti adzakulangeni monga momwe mafunde amawombera pa Nyanja. 4Anthuwo adzawononga makoma a Turo ndi kugwetsa nsanja zake. Ndidzapala dothi lake ndipo ndidzamusandutsa thanthwe losalala. 5Udzakhala poyanikapo makoka pakati pa nyanja. Ine Ambuye Yehova ndayankhula zimenezo. Udzasanduka chofunkha cha anthu a mitundu ina. 6Anthu okhala ku mtunda adzasakazidwa ndi lupanga. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

7“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Iwe Turo, ndidzakubweretsera Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni mfumu ya mafumu, kuchokera kumpoto pamodzi ndi akavalo ndiponso magaleta, anthu okwera pa akavalo ndi gulu lalikulu la ankhondo. 8Anthu okhala ku mtunda adzawapha ndi lupanga. Adzapanga mitumbira yankhondo ndi kukukwezera zishango kuti alimbane nawe. 9Adzagwetsa makoma ako ndi zida zogumulira khoma ndi kugwetsa nsanja zako ndi nkhwangwa zake. 10Akavalo ake adzakhala ochuluka kwambiri kotero kuti adzakukwirira ndi fumbi lawo. Makoma ako adzagwedezeka ndi mdidi wa akavalo, ngolo ndi magaleta pamene iye adzalowa pa zipata monga mmene amalowera mu mzinda umene makoma ake agwetsedwa. 11Akavalo ake adzapondaponda mʼmisewu yako yonse ndi ziboda zawo. Adzapha anthu ako ndi lupanga. Mizati yako yolimba idzagwetsedwa. 12Iwo adzafunkha chuma chako ndipo adzalanda zinthu zako za malonda. Adzagwetsa makoma ako ndi kuwononga nyumba zako zabwino. Adzaponya miyala yako, matabwa ako ndi dothi lako mʼnyanja. 13Choncho ndidzathetsa phokoso la nyimbo zanu, ndipo kulira kwa apangwe ako sikudzamvekanso. 14Ndidzakusandutsa thanthwe losalala, ndipo udzakhala malo woyanikapo makoka a nsomba. Sudzamangidwanso, pakuti Ine Yehova ndayankhula, akutero Ambuye Yehova.

15“Ine Ambuye Yehova ndikukuwuza, iwe mzinda wa Turo, kuti zilumba zidzagwedezeka pakumva za kugwa kwako ndiponso poona anthu opweteka akubuwula ndipo anthu akuphedwa pakati pako. 16Pamenepo mafumu a mʼmbali mwa nyanja adzatsika pa mipando yawo yaufumu. Adzayika pambali mikanjo yawo ndi kuvala zovala zawo zamakaka. Adzachita mantha ndipo adzakhala pansi akunjenjemera kosalekeza. Adzathedwa nzeru poona zimene zakugwera. 17Pamenepo adzayimba nyimbo yokudandaula ndipo adzati kwa iwe:

“ ‘Nʼkuchita kuwonongeka chotere, iwe mzinda wotchuka,

wodzaza ndi anthu a ku nyanja!

Unali wamphamvu pa nyanja,

iwe ndi nzika zako;

unkaopseza anthu onse amene

ankakhala kumeneko.

18Tsopano mayiko a mʼmbali mwa nyanja akunjenjemera

chifukwa cha kugwa kwako;

okhala pa zilumba nawonso agwidwa ndi mantha aakulu

chifukwa cha kugwa kwako.’

19“Mawu a Ine Ambuye Yehova ndi awa: Ndidzakusandutsa bwinja, ngati mizinda imene anthu sangathe kukhalamo. Ndidzakuphimba ndi madzi ozama a mʼnyanja, madzi amphamvu woti akumize. 20Ndidzakugwetsa pansi kuti ukhale pamodzi ndi anthu amvulazakale amene akutsikira ku manda. Ine ndidzakusunga ku dzenjeko ngati ku bwinja losiyidwa kalekale, pamodzi ndi anthu amene anafa kale motero sudzabwererako kukhala pakati pa anthu amoyo. 21Ine ndidzakuthetsa mochititsa mantha, ndipo sudzakhalaponso. Anthu adzakufunafuna, koma sudzapezekanso, akutero Ambuye Yehova.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

以西結書 26:1-21

預言泰爾遭審判

1第十一年十一月一日,耶和華對我說: 2「人子啊,泰爾譏笑耶路撒冷說,『哈哈!那通往列國的門戶已遭破壞,城門向我大開,她已荒涼,我必興盛。』 3所以主耶和華說,『泰爾啊,我要跟你作對,我要激起多國來攻擊你,就像大海掀起波浪一樣。 4他們要破壞你的牆垣,拆毀你的城樓。我要鏟淨你的瓦礫,使你成為光禿禿的磐石, 5在海中做曬網的地方,你必被列國擄掠,因為我已宣告。這是主耶和華說的。 6你陸地上的居民必死於刀下,這樣你就知道我是耶和華。』

7「主耶和華說,『我要使那王中之王的巴比倫尼布甲尼撒率領大隊人馬、戰車和騎兵從北方來攻打泰爾8他必用刀劍殺戮你陸地上的居民,建壘築臺圍困你,舉著盾牌攻擊你。 9他必用撞城錘擊破你的城牆,用鐵錘搗毀你的城樓。 10他人馬眾多,揚起的塵土足以遮蓋你。他要攻破你的城池,進入你的城門,他的騎兵、軍需車和戰車要震動你的城牆。 11他戰馬的鐵蹄必踏遍你的街道。他必揮刀屠殺你的居民,推倒你堅固的神柱, 12掠奪你的財物,摧毀你的城牆,夷平你華麗的房屋,把你的石頭、木頭和瓦礫拋到海裡。 13我必使你的歌聲消逝,琴音斷絕。 14我要使你成為光禿禿的磐石,做曬網的地方,你必不得重建,因為我耶和華已經宣告。這是主耶和華說的。』

15「主耶和華對泰爾這樣說,『你傾覆的時候,你中間的殺戮聲和受傷之人的慘叫聲豈不震動沿海地區嗎? 16沿海諸王因你而恐懼,都從寶座上下來,除去王袍,脫掉錦衣,坐在地上發抖。 17他們必為你唱哀歌說,

『你這海上眾民居住的名城,

向來稱雄海上,威震鄰邦,

現在怎麼被毀滅了呢?

18你傾覆的日子,

沿海各國都戰戰兢兢,

眾海島看見你被毀滅,

都心驚膽戰。』

19「主耶和華說,『我要使你成為荒無人煙的城邑,我要使海水上升淹沒你。 20那時,我要使你與那些墮入陰間的人一同下到作古之人那裡,使你與那些墮入陰間的人一同住在大地深處久已荒涼的地方,好讓你荒無人煙,在活人之地毫無尊榮。 21我使你遭受可怕的災難,你便不復存在,就是有人尋找你,也永遠找不到,這是主耶和華說的。』」