Ezekieli 22 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 22:1-31

Machimo a Yerusalemu

1Yehova anandiyankhula nati: 2“Iwe mwana wa munthu, kodi udzaweruza mzinda uwo wa anthu akupha anzawo? Tsono uwudzudzule chifukwa cha machitidwe ake onse onyansa 3ndipo unene kuti, ‘Ambuye akuti: Iwe mzinda umene wadzigwetsa wekha mʼtsoka pa kukhetsa magazi pakati pako ndi kudziyipitsa popanga mafano, 4wapezekatu wolakwa chifukwa cha magazi amene wakhetsa, ndipo wadziyipitsa chifukwa cha mafano amene wapanga. Choncho wachepetsa masiku ako, ndipo zaka zako zafika kumapeto. Nʼchifukwa chake ndalola kuti anthu a mitundu ina akunyoze ndiponso kuti anthu a mayiko onse akuseke. 5Mayiko amene ali pafupi ndi mayiko omwe ali kutali adzakunyoza, iwe mzinda wa mbiri yoyipa, wodzaza ndi chiwawa.

6“ ‘Taona momwe aliyense wa atsogoleri a Israeli amagwiritsira mphamvu zake kupha anthu. 7Mu mzindamo anthu amanyoza abambo ndi amayi awo. Iwo amapondereza alendo ndi kuzunza ana amasiye ndi akazi amasiye. 8Wanyoza zinthu zanga zopatulika ndi kuyipitsa Masabata anga. 9Mwa iwe muli anthu onenera anzawo zabodza kuti aphedwe. Mwa iwe mulinso amene amadyera zansembe pa mapiri a chipembedzo. Enanso amachita zonyansa. 10Mwa iwe muli ena ogonana ndi akazi a abambo awo, muli enanso amene amavuta akazi pamene ali woyipitsidwa ndi msambo. 11Ena amachita chigololo ndi akazi a anzawo, ndipo ena, mopanda manyazi, amayipitsa mkazi wa mwana wawo. Palinso ena amene amayipitsa alongo awo, ana aakazi a abambo awo. 12Mwa iwe muli anthu amene amalandira ziphuphu kuti aphe anzawo; ena amachita katapira ndi kupeza phindu loposera muyeso; enanso amapeza phindu mwachinyengo poopseza anzawo. Ndipo mwandiyiwala Ine, akutero Ambuye Yehova.

13“ ‘Koma Ine ndachita kuwomba mʼmanja kuti phuu nʼkudabwa chifukwa cha phindu lachinyengo limene mwapeza ndiponso chifukwa cha kuphana kumene kumachitika pakati panu. 14Kodi mtima wako udzakhala wolimbabe kapena manja ako adzakhalabe amphamvu ndikadzatsiriza kukulanga iwe? Ine Yehova ndayankhula, ndipo ndidzazichitadi. 15Ndidzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukumwazirani ku mayiko onse. Umu ndi mmene ndidzachotsere zoyipa zako. 16Udzanyozedwa pamaso pa anthu a mitundu ina. Pambuyo pake udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”

17Yehova anandiyankhula nati: 18“Iwe mwana wa munthu, Aisraeli asanduka chinthu cha chabechabe kwa Ine. Onse ali ngati mkuwa, chitini, chitsulo ndi mtovu zotsala mʼngʼanjo atayeretsa siliva. 19Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: ‘Pakuti nonse mwasanduka chinthu cha chabechabe, Ine ndidzakusonkhanitsani mu Yerusalemu. 20Monga momwe anthu amasonkhanitsira siliva, mkuwa, chitsulo, mtovu ndi chitini mʼngʼanjo ndi kusonkhetsa moto kuti azisungunule, motero Inenso ndidzakusonkhanitsani ndili wokwiya ndi waukali, ndipo ndidzakuyikani mʼkati mwa mzinda, ndikukusungunurani. 21Ndidzakusonkhanitsani mu mzindamo ndi kukoleza moto wa mkwiyo wanga, ndipo inu mudzasungunuka mu mzindamo. 22Monga siliva amasungunulidwa mʼngʼanjo, kotero inunso mudzasungunuka mʼkati mwa mzinda ndipo Inu mudzadziwa kuti Ine Yehova ndakukwiyirani.’ ”

23Yehova anandiyankhulanso nati, 24“Iwe mwana wa munthu, uza dziko la Israeli kuti, ‘Iwe ndiwe dziko losayeretsedwa, ndiponso losavumbidwa ndi mvula chifukwa cha mkwiyo wanga.’ 25Atsogoleri ake mu mzindamo ali ngati mkango wobangula pogwira nyama. Apha anthu, alanda chuma ndi zinthu za mtengowapatali, ndiponso asandutsa amayi ambiri kukhala amasiye. 26Ansembe ake amaphwanya lamulo langa ndi kuyipitsa zinthu zanga zopatulika. Sasiyanitsa pakati pa zinthu zopatulika ndi zinthu wamba. Saphunzitsa anthu kusiyana kwa zinthu zoyenera pa chipembedzo ndi zinthu zosayenera. Sasamalira za kusunga masabata anga. Motero Ine ndimanyozedwa pakati pawo. 27Atsogoleri ake ali ngati mimbulu yokhadzula nyama; amakhetsa magazi ndi kupha anthu kuti apeze phindu loyipa. 28Aneneri ake amabisa zonsezi monga muja amachitira anthu popaka njereza. Amazimphimba ndi zabodza zimene aona mʼmasomphenya awo ndi zonama za mʼmawula awo. Iwo amati, ‘Ambuye Yehova akuti,’ pamene Ine Yehova sindinayankhule. 29Anthu a mʼdzikomo amasautsa anzawo ndi kulanda anthu osowa. Amazunza anthu osauka ndi amphawi. Amavutitsa alendo posawachitira zinthu mwachilungamo.

30“Ndinafunafuna munthu pakati pawo woti amange linga, woti ayimirire dziko pamaso panga kundipepesa kuti ndisaliwononge, koma sindinamupeze. 31Nʼchifukwa chake ndawakwiyira kwambiri. Ndawawonongeratu ndi mkwiyo wanga woyaka ngati moto. Ndawalanga molingana ndi zimene anachita. Akutero Ambuye Yehova.”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以西结书 22:1-31

耶路撒冷的罪恶

1耶和华对我说: 2“人子啊,你要审判耶路撒冷这杀人流血的城。你要审判她,使她知道自己一切可憎的行为。 3你要向她宣告主耶和华的话,说,‘唉,你这杀人流血、制造偶像玷污自己的城啊,你的末日到了。 4你既犯罪杀人、制造偶像玷污自己、自招审判,我要使你成为列国列邦侮辱和讥讽的对象。 5你这声名狼藉、混乱不堪的城将要受到远近各国的耻笑。

6“‘看啊,在你城中的以色列首领各逞权势,杀人流血。 7他们轻慢父母,压迫寄居者,欺负孤儿寡妇。 8他们藐视我的圣物,亵渎我的安息日。 9在你这城中,有人好诽谤、杀人流血,有人在山上吃祭物,有人淫乱, 10有人与继母通奸,羞辱父亲,有人奸污经期不洁的妇女, 11有人与邻居的妻子干出可憎之事,有人玷污自己的儿媳妇,有人奸污自己的同父姊妹。 12在你这城中,他们受贿杀人,放债取利,压榨邻居,早把我忘了。这是主耶和华说的。

13“‘我见你谋财害命,就击掌叹息。 14在我惩罚你的日子,你还有勇气和力量吗?我耶和华言出必行, 15我要把你驱散到列国,分散到列邦,我要除掉你的污秽。 16你必在列国面前受凌辱,你便知道我是耶和华。’”

17耶和华对我说: 18“人子啊,在我看来,以色列人已经变成了渣滓。他们是炉中的铜、锡、铁、铅,都是银渣滓。 19所以主耶和华说,‘你们既是渣滓,我要把你们聚集在耶路撒冷城。 20我要在烈怒中把你们聚集在城里熔化,就像人把银、铜、铁、铅、锡聚在高温的炉中熔化一样。 21我要聚集你们,把我的怒火倒在你们身上,熔化你们。 22你们要在城中熔化,就像银在炼炉中熔化。你们就知道我耶和华已将我的烈怒倾倒在你们身上。’”

23耶和华对我说: 24“人子啊,你要对以色列说,‘在我发怒的日子,将没有雨水滋润你这不洁之地。 25你的首领图谋恶事,好像咆哮着撕碎猎物的狮子,他们草菅人命,抢夺财宝,使多人变成寡妇。 26你的祭司强解我的律法,亵渎我的圣物。他们圣俗不分,也不教导人分辨洁净的和污秽的。他们藐视我的安息日,亵渎我。 27你的首领好像撕碎猎物的豺狼,杀人流血,谋取不义之财。 28你的先知对他们说虚假的异象和占卜,像用白灰刷墙一样掩盖他们的罪恶,说,耶和华这样说,其实耶和华没有说。 29你的居民强取豪夺,欺压贫困的,虐待寄居的,无法无天。 30我想在他们中间寻找一位重修城墙的人,站在我面前为这地方堵住缺口,免得我毁灭这里。可是,我一个也找不到。 31因此,我要向他们倾倒我的烈怒,用怒火灭尽他们,照他们的所作所为报应他们。这是主耶和华说的。’”