Ezekieli 21 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 21:1-32

Babuloni, Lupanga la Mulungu

1Yehova anandiyankhula nati: 2“Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyangʼane ku Yerusalemu ndipo ulalike mawu odzudzula malo ake opatulika. Unenere zodzudzula anthu a ku Yerusalemu. 3Uwawuze kuti, Ambuye Yehova akuti, ‘Taona, Ine ndidzalimbana nawe. Ndidzasolola lupanga langa mʼchimake ndi kuwononga anthu olungama ndi ochimwa omwe. 4Motero ndidzapha aliyense kuchokera kummawa mpaka kumpoto. 5Pamenepo anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndasolola lupanga langa mʼchimake; sindidzalilowetsanso mʼchimakemo.’

6“Tsono iwe mwana wa munthu, buwula. Buwula pamaso pawo ndi mtima wosweka ndi wachisoni chachikulu. 7Ndipo akadzakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukubuwula?’ Iwe udzayankhe kuti, ‘Ndikubuwula chifukwa cha nkhani imene ndamva. Zikadzachitika zimenezi, mitima yonse idzangoti fumu, manja onse adzangolefuka, mpweya wawo udzawathera, ndipo mawondo onse adzangoti zii.’ Izi zikubwera! Ndipo zidzachitika ndithu, akutero Ambuye Yehova.”

8Yehova anandiyankhulanso kuti, 9“Iwe mwana wa munthu, unenere ndipo unene kuti, Ambuye Yehova akuti,

“Izi ndi zimene Yehova akunena:

Lupanga, lupanga, lanoledwa ndipo lapukutidwa.

10Lanoledwa kuti likaphe,

lapukutidwa kuti lingʼanime ngati mphenzi!

“ ‘Kodi tingakondwere bwanji? Wanyoza ndodo, mwana wanga ndi chilichonse cha mtengo.

11“ ‘Lupanga laperekedwa kuti lipukutidwe,

ndi kuti linyamulidwe,

lanoledwa ndi kupukutidwa,

kuti liperekedwe mʼmanja mwa munthu amene amapha.

12Fuwula ndi kulira, iwe mwana wa munthu,

pakuti zimenezi zidzagwera anthu anga;

zidzagweranso akalonga onse a Israeli.

Adzaphedwa ndi lupanga

pamodzi ndi anthu anga.

Chifukwa chake udzigugude pa chifuwa ndi chisoni.

13“ ‘Ambuye Wamphamvuzonse akuti: Ndikuwayesa anthu anga, ndipo ngati satembenuka mtima, ndiye kuti zimenezi sizidzalephera kuwagwera.’

14“Tsono mwana wa munthu, nenera

ndipo uwombe mʼmanja.

Lupanga likanthe kawiri

ngakhale katatu.

Limenelo ndilo lupanga lophera anthu.

Inde ndilodi lupanga lophera anthu koopsa

limene likuwazungulira.

15Ndawayikira pa zipata zawo zonse

lupanga laphuliphuli

kuti ataye mtima

ndiponso kuti anthu ambiri agwe.

Aa! Lapangidwa lupanga kuti lizingʼanima ngati mphenzi

ndi kuti azilisolola kuphera anthu.

16Iwe lupanga, ipha anthu kumanja,

kenaka kumanzere,

kulikonse kumene msonga yako yaloza.

17Inenso ndidzawomba mʼmanja mwanga,

ndipo ndidzaziziritsa ukali wanga

Ine Yehova ndayankhula.”

18Yehova anandiyankhulanso kuti, 19“Iwe mwana wa munthu, ulembe zizindikiro za misewu iwiri imene lupanga la mfumu ya ku Babuloni lingathe kudzeramo. Misewu yonse ikhale yochokera mʼdziko limodzi. Ika chikwangwani pa mphambano yopita mu mzinda. 20Ulembe chizindikiro pa msewu umene lupanga lidzadzere popita ku Raba wa ku Amoni, ndiponso ku Yuda ndi ku Yerusalemu, mzinda wotetezedwa. 21Pakuti mfumu ya ku Babuloni yayima pa msewu, pa mphambano ya misewu iwiriyo. Ikuwombeza ndi mivi yake kuti idziwe njira yoyenera kudzeramo. Ikupempha nzeru kwa milungu yake ndipo ikuyangʼana chiwindi cha nyama yoperekedwa ku nsembe. 22Mʼdzanja lake lamanja muli muvi waula wolembedwa Yerusalemu. Kumeneko mfumuyo idzayika zida zogumulira, idzalamula kupha anthu ndiponso kufuwula mfuwu wa nkhondo. Mfumuyo idzapanga zida zogumulira makoma, kuwunda mitumbira ya nkhondo ndi kumanga nsanja za nkhondo. 23Koma kwa anthu a ku Yerusalemu zidzaoneka ngati zowombeza zabodza chifukwa cha malumbiro amene anachita kwa mfumuyo. Koma mfumuyo idzawakumbutsa za zolakwa zawo kuti atengedwe ku ukapolo.

24“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Popeza mwandikumbutsa zolakwa, moti kundiwukira kwanu kwaonekera poyera ndi kuti mu zochita zanu zonse mukuonetsa machimo anu, nʼchifukwa chake mudzagwidwa ndi kutengedwa ukapolo.

25“ ‘Tsono iwe kalonga wonyozedwa ndi woyipa wa Israeli, amene tsiku lako lafika, amene nthawi yako yolangidwa yafika penipeni, 26Ambuye Yehova akuti: Vula nduwira, chotsa chipewa chaufumu. Zinthu sizidzakhala monga zinalili: anthu wamba adzakwezedwa ndipo okwezedwa adzatsitsidwa. 27Chipasupasu! Chipasupasu! Ine ndidzawupasula mzindawo! Ndipo sadzawumanganso mpaka atafika amene ali woyenera kuwulandira; Ine ndidzawupereka kwa iyeyo.’

28“Ndipo iwe mwana wa munthu, nenera kuti, ponena za Aamoni ndi zonyoza zawo, Ambuye Yehova akuti,

“ ‘Lupanga, lupanga,

alisolola kuti liphe anthu,

alipukuta kuti liwononge

ndi kuti lingʼanime ngati mphenzi.

29Zimene akuti akuona mʼmasomphenya zokhudza inu ndi zabodza.

Mawula awo okhudza inu ndi abodzanso.

Mudzakhala pamodzi ndi anthu oyipa

amene tsiku lawo lafika,

ndiye kuti nthawi

ya kulangidwa kwawo komaliza.

30“ ‘Bwezerani lupanga mʼchimake.

Ku malo kumene inu munabadwira,

mʼdziko la makolo anu,

ndidzakuweruzani.

31Ndidzakhuthula ukali wanga pa inu,

ndipo mkwiyo wanga udzakuyakirani.

Ndidzakuperekani mʼmanja mwa anthu ankhanza;

anthu odziwa bwino kuwononga zinthu.

32Mudzakhala ngati nkhuni pa moto.

Ena adzakhetsa magazi anu mʼdziko lanu lomwe.

Simudzakumbukiridwanso

pakuti Ine Yehova ndayankhula.’ ”