Ezekieli 2 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 2:1-10

Kuyitanidwa kwa Ezekieli

1Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, imirira kuti ndiyankhule nawe.” 2Pamene ankayankhula nane, Mzimu wa Mulungu unalowa mwa ine ndipo unandiyimiritsa, ndipo ndinamva Iye akundiyankhula.

3Iye anati, “Iwe mwana wa munthu, Ine ndikukutuma kwa Aisraeli, mtundu wa anthu owukira umene wandiwukira Ine; Iwo ndi makolo awo akhala akundiwukira Ine mpaka lero lino. 4Ndikukutuma kwa anthu okanika ndiponso nkhutukumve. Ndikukutuma kuti akawawuze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena. 5Kaya akamva kaya sakamvera, pakuti iwo ndi anthu opanduka, komabe adzadziwa kuti mneneri ali pakati pawo. 6Tsono iwe mwana wa munthu, usachite nawo mantha kapena kuopa zimene azikanena. Usachite mantha, ngakhale minga ndi mkandankhuku zikuzinge ndipo ukukhala pakati pa zinkhanira. Usachite mantha ndi zimene akunena kapena kuopsedwa ndi nkhope zawo, popeza anthuwa ndi awupandu. 7Ukawawuze ndithu mawu anga, kaya akamva kaya sakamva. Paja anthuwa ndi awupandu. 8Koma iwe mwana wa munthu, mvetsera zimene ndikukuwuza. Usakhale wowukira ngati iwowo. Tsono yasama pakamwa pako kuti udye chimene ndikukupatsa.”

9Nditayangʼana ndinangoona dzanja litaloza ine, litagwira mpukutu wolembedwa. 10Anawufunyulura pamaso panga. Mpukutu wonse unali wolembedwa kuseri nʼkuseri. Ndipo mawu amene analembedwa mʼmenemo anali a madandawulo, maliro ndi matemberero.