Ezekieli 18 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 18:1-32

Munthu Wochimwa Adzafa

1Yehova anandiyankhula nati: 2“Kodi anthu inu mumatanthauza chiyani mukamabwerezabwereza kunena mwambi uwu wokhudza dziko la Israeli kuti:

“ ‘Nkhuyu zodya akulu zimapota

ndi ana omwe?’ ”

3“Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, simudzanenanso mwambi umenewu mu Israeli. 4Pakuti moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa abambo ndi wanga, wamwananso ndi wanga. Munthu wochimwa ndi amene adzafe.

5“Tiyerekeze kuti pali munthu wolungama

amene amachita zolungama ndi zolondola.

6Iye sadyera nawo pa mapiri a chipembedzo

kapena kupembedza mafano a Aisraeli.

Iye sayipitsa mkazi wa mnzake

kapena kugonana ndi mkazi pamene akusamba.

7Iye sapondereza munthu wina aliyense,

koma amabwezera wangongole nʼchigwiriro chake.

Iye salanda zinthu za osauka,

koma amapereka chakudya kwa anthu anjala,

ndipo amapereka zovala kwa anthu ausiwa.

8Iye sakongoletsa ndalama mwa katapira,

kapena kulandira chiwongoladzanja chachikulu.

Amadziletsa kuchita zoyipa

ndipo sakondera poweruza milandu.

9Iye amatsatira malangizo anga,

ndipo amasunga malamulo anga mokhulupirika.

Munthu ameneyo ndi wolungama;

iye adzakhala ndithu ndi moyo,

akutero Ambuye Yehova.

10“Tiyerekeze kuti munthu wolungama chotere wabala mwana chimbalangondo amene amakhalira kupha anthu ndi kuchita zinthu zina zotere. 11Iye nʼkumachita zinthu zimene ngakhale abambo ake sanachitepo.

“Amadyera nawo ku mapiri achipembedzo.

Amayipitsa mkazi wa mnzake.

12Iye amapondereza munthu wosauka ndi wosowa.

Amalanda zinthu za osauka.

Sabweza chikole cha munthu wa ngongole.

Iye amatembenukira ku mafano

nachita zonyansa.

13Iye amakongoletsa mwa katapira ndipo amalandira chiwongoladzanja chachikulu.

Kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu! Chifukwa wachita zinthu zonyansa zonsezi, adzaphedwa ndipo adzalandira chilango chomuyenera.

14“Tsono tiyerekeze kuti munthu woyipa uyu wabala mwana amene amaona machimo onse amene abambo ake ankachita. Ngakhale amaona koma osatsanzira ntchito zake zoyipazo.

15“Sadyera nawo pa mapiri achipembedzo.

Sapembedza mafano a ku Israeli.

Sayipitsa mkazi wa mnzake.

16Sapondereza munthu wina aliyense.

Satenga chikole akabwereketsa chinthu. Salanda zinthu za osauka.

Salanda zinthu za munthu.

Amapereka chakudya kwa anthu anjala.

Amapereka zovala kwa anthu aumphawi.

17Amadziletsa kuchita zoyipa.

Sakongoletsa kuti apezepo phindu. Salandira chiwongoladzanja.

Amasunga malangizo anga ndi kumvera malamulo anga.

Munthu wotereyo sadzafa chifukwa cha machimo a abambo ake. Adzakhala ndi moyo ndithu. 18Koma abambo ake, popeza kuti anazunza anthu ena ndi kubera mʼbale wawo ndiponso popeza kuti sanachitire zabwino anansi ake, adzafera machimo ake omwe.

19“Mwina inu mukhoza kufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mwana salangidwa chifukwa cha kulakwa kwa abambo ake? Ayi, mwanayo adzakhala ndi moyo chifukwa ankachita zolungama ndi zolondola ndipo ankasamala kumvera malamulo anga onse. 20Munthu wochimwa ndiye amene adzafe. Mwana sadzapezeka wolakwa chifukwa cha abambo ake, kapena abambo kupezeka wolakwa chifukwa cha mwana wawo. Chilungamo cha munthu wolungama ndicho chidzamupulutse, ndipo kuyipa kwa munthu wochimwa ndiko kudzamuwonongetse.

21“ ‘Munthu woyipa akatembenuka mtima ndi kusiya machimo amene ankachita ndi kuyamba kumvera malamulo anga ndi kumachita zolungama ndi zokhulupirika, ndiye kuti adzakhala ndi moyo. Sadzafa ayi. 22Zoyipa zake zonse zidzakhululukidwa. Chifukwa cha zinthu zolungama zimene anazichita adzakhala ndi moyo. 23Kodi Ine ndimakondwera ndi imfa ya munthu woyipa? Ayi, ndimakondwera pamene woyipa watembenuka mtima kuti akhale ndi moyo. Akutero Ambuye Yehova.

24“ ‘Koma ngati munthu wolungama apatuka kusiya zachilungamo ndi kuyamba kuchita tchimo ndi zonyansa za mtundu uliwonse zimene amachita anthu oyipa, kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu, zolungama zake zonse sizidzakumbukiridwa. Iye adzayenera kufa chifukwa cha machimo amene anachita.

25“Komabe inu mukunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Tamvani tsono inu Aisraeli: Kodi zochita zanga ndizo zosalungama? Kodi si zochita zanu zimene ndi zosalungama? 26Ngati munthu wolungama atembenuka kusiya chilungamo chake ndi kuchita tchimo, iye adzafa chifukwa cha tchimolo. 27Koma ngati munthu woyipa aleka zoyipa zake zimene anazichita ndi kuyamba kuchita zimene ndi zolungama ndi zolondola, iye adzapulumutsa moyo wake. 28Popeza waganizira za zolakwa zonse ankachita ndipo wazileka, iye adzakhala ndi moyo ndithu; sadzafa. 29Komabe Aisraeli akunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Kodi zochita zanga ndizo zopanda chilungamo, inu Aisraeli? Kodi si zochita zanu zimene ndi zopanda chilungamo?

30“Chifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: inu Aisraeli, Ine ndidzakuweruzani aliyense wa inu molingana ndi ntchito zake. Lapani! Lekani zoyipa zanu kuti musawonongeke nazo. 31Tayani zolakwa zanu zonse zimene munandichimwira nazo ndipo khalani ndi mtima watsopano ndi mzimu watsopano. Kodi muferanji inu Aisraeli? 32Ine sindikondwera ndi imfa ya munthu aliyense, akutero Ambuye Yehova. Chifukwa chake, lapani kuti mukhale ndi moyo.”