Ezekieli 16 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 16:1-63

Kusakhulupirika kwa Yerusalemu

1Yehova anayankhula nane kuti, 2“Iwe mwana wa munthu, udzudzule Yerusalemu za ntchito zake zonyansa. 3Umuwuze kuti, ‘Ambuye Yehova akukuwuza, iwe Yerusalemu kuti: Kwawo kwa makolo ako ndi ku Kanaani ndipo iwe unabadwira komweko. Abambo ako anali Mwamori, amayi ako anali Mhiti. 4Pa tsiku lomwe unabadwa sanadule mchombo wako. Sanakusambitse mʼmadzi kuti uyere. Sanakuthire mchere kapena kukukulunga mʼnsalu. 5Palibe ndi mmodzi yemwe anakusamala kapena kukumvera chisoni kuti akuchitire zimenezi. Mʼmalo mwake anakutaya panja poyera, chifukwa ananyansidwa nawe pa tsiku lako lobadwa.

6“ ‘Tsono pamene ndinkadutsa, ndinakuona ukuvimvinizika mʼmagazi ako. Ndinakuyankhula uli mʼmagazi ako omwewo kuti, ‘Khala ndi moyo,’ 7ndi kuti ukule ngati mbewu ya mʼmunda. Iwe unakula ndipo unatalika ndi kutha msinkhu. Mawere ako anayamba kumera ndi tsitsi lakonso linayamba kutalika. Komabe unali wamaliseche ndi wausiwa.

8“ ‘Tsono pamene ndinkadutsanso ndinaona kuti nthawi yako yomanga banja inakwana. Tsono ndinakufunditsa chovala changa ndi kubisa umaliseche wako. Ndinachita nawe pangano la ukwati ndipo unakhala wanga, akutero Ambuye Wamphamvuzonse.

9“ ‘Ine ndinakusambitsa mʼmadzi kutsuka magazi ako ndikukudzoza mafuta. 10Ndinakuveka zovala zopetapeta ndi nsapato za chikopa. Ndinakuveka zovala zabafuta ndi kukuveka zovala za bafuta. 11Ndinakukongoletsa ndi zokometsera zamtengowapatali: ndinakuveka zibangiri mʼmanja mwako ndi mkanda mʼkhosi mwako, 12ndipo ndinakuveka chipini pa mphuno yako, ndolo ku makutu ako ndiponso chipewa chaufumu pa mutu wako. 13Choncho unavala zokongoletsa zagolide ndi siliva. Zovala zako zinali zabafuta, zasilika ndi za nsalu zopetapeta. Chakudya chako chinali ufa wosalala uchi ndi mafuta a olivi. Motero unakhala wokongola kwambiri ndipo unasanduka mfumukazi. 14Ndipo mbiri ya kukongola kwako inawanda pakati pa anthu a mitundu ina, chifukwa ulemerero umene ndinakupatsa unapititsa patsogolo kukongola kwako, akutero Ambuye Yehova.

15“ ‘Koma iwe unatama kukongola kwako ndipo unayamba kuchita zadama chifukwa cha kutchuka kwako. Unkachita chigololo ndi kumangodzipereka kwa aliyense wodutsa ndipo kukongola kwako kunakhala kwake. 16Unatenga zovala zako zina nukakongoletsera malo opembedzerako mafano, ndipo kumeneko umachitirako zigololo. Zinthu izi sizinachitikepo nʼkale lomwe ndipo sizidzachitikanso. 17Unatenga zokongoletsera zopangidwa ndi golide ndi siliva zimene ndinakupatsa ndipo unadzipangira wekha mafano aamuna amene unkachita nawo za dama. 18Ndipo iwe unatenga zovala zako zopetapeta ndi kuveka mafano. Mafuta anga ndi lubani wanga unapereka kwa mafanowo. 19Chakudya chimene ndinakupatsa, ufa, mafuta ndi uchi, zimene ndinkakudyetsa nazo unazitenga nʼkuzipereka kwa mafanowo ngati nsembe ya fungo lokoma. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.

20“ ‘Ndipo unatenga ana ako aamuna ndi ana aakazi amene unandibalira ine, ndipo unakawapereka ngati nsembe kwa mafanowo. Kodi zigololo zakozo sizinakukwanire 21kuti uziphanso ana anga ndi kuwapereka ngati nsembe kwa mafano akowo? 22Chifukwa cha zadama zako zonyansazi unayiwala masiku a ubwana wako pamene unali wamaliseche, wausiwa ndiponso womangovivinizika mʼmagazi.

23“ ‘Tsoka! Tsoka kwa iwe, akutero Ambuye Yehova chifukwa powonjezera pa zoyipa zako zonse, 24wadzimangira wekha nsanja ndi guwa pa mabwalo onse. 25Pa msewu uliwonse wamanga nsanjazo. Motero wanyazitsa kukongola kwako podzipereka kwa aliyense amene adutsapo. 26Umachita chigololo ndi Aigupto, anthu adama oyandikana nawe. Choncho unandikwiyitsa chifukwa unachulukitsa za dama zako. 27Nʼchifukwa chake ndinatambasula dzanja langa kukukantha ndi kuchepetsa dziko lako. Ndinakupereka kwa adani ako, Afilisti amene amayipidwa ndi makhalidwe ako onyansa. 28Chifukwa cha chilakolako chako unachitanso zadama ndi Aasiriya. Ngakhale unachita nawo chigololo koma sunakhutitsidwebe. 29Choncho unapitirirabe kuchita chigololo ndi Ababuloni, anthu a mʼdziko lokonda zamalonda. Ngakhale unachita izi, komabe sunakhutitsidwe.

30“ ‘Ambuye Yehova akuti: Mtima wako ndi wofowoka kwambiri chifukwa unachita zonsezo monga ngati mkazi wopanga manyazi. 31Unamanga nsanja pa msewu uliwonse. Unamanganso kachisi pabwalo lililonse. Komabe sunachite ngati mkazi wadama chifukwa unakana malipiro.

32“ ‘Iwe mkazi wachigololo! Umakonda amuna achilendo kupambana mwamuna wakowako! 33Amuna ndiwo amapereka malipiro kwa mkazi wadama. Koma iwe ndi amene ukupereka mphatso kwa zibwenzi zako zonse. Choncho umazinyengerera kuti zizibwera kwa iwe kuchokera mbali zonse kudzagona nawe. 34Chotero iwe ukusiyana ndi akazi ena achigololo, pakuti palibe amene ankakunyengerera kuti uchite naye chigololo. Iweyo ndiye unkapereka ndalama osati ena kukupatsa ndalama ayi. Motero unalidi wosiyana kwambiri ndi akazi ena.

35“ ‘Tsono mkazi wachigololo iwe, imva mawu a Yehova! 36Ambuye Yehova akuti, popeza unavula ndi kuonetsa umaliseche wako mopanda manyazi, unachita chigololo ndi zibwenzi zako pamodzi ndi mafano ako onyansa, komanso popeza unapereka ana ako kuti aphedwe ngati nsembe zoperekedwa kwa mafano, 37nʼchifukwa chake Ine ndidzasonkhanitsa zibwenzi zako zonse, zimene unkasangalala nazo, amene unkawakonda ndi amene unkawada. Ndidzawasonkhanitsa motsutsana nawe kuchokera ku madera onse okuzungulira ndipo Ine ndidzakuvula pamaso pawo, ndipo iwo adzaona umaliseche wako wonse. 38Ine ndidzakulanga monga mmene amalangira akazi amene amachita chigololo ndiponso opha anthu. Chifukwa cha ukali wanga ndi nsanje yanga, ndidzakhetsa magazi ako mokwiya kwambiri. 39Ndidzakupereka mʼmanja mwa zibwenzi zako ndi kuwononga nyumba zopembedzera mafano ako. Iwo adzakuvula zovala zako ndi kutenga zodzikometsera zako zabwino. Choncho adzakusiya wa maliseche ndi wausiwa. 40Iwo adzabweretsa gulu la anthu limene lidzakuponya miyala ndi kukutematema ndi malupanga awo. 41Adzatentha nyumba zako ndi kukulanga iwe pamaso pa akazi ambiri. Ndidzathetsa chigololo chako, ndipo sudzalipiranso zibwenzi zako. 42Ukali wanga udzalekera pamenepo ndipo sindidzakuchitiranso nsanje. Ndidzakhala chete osakwiyanso.

43“ ‘Popeza sunakumbukire masiku a ubwana wako koma unandikwiyitsa ndi zinthu zonsezi, Ine ndidzakubwezera ndithu chilango pamutu pako chifukwa cha zimene wachita, akutero Ambuye Yehova. Paja unawonjezera chigololo pa machitidwe ako onyansa.

44“ ‘Taona, onse onena miyambi adzakuphera mwambi wakuti, ‘Make mbuu, mwana mbuu.’ 45Ndiwedi mwana weniweni wamkazi wa mayi wako, amene amanyoza mwamuna wake ndi ana ake. Ndiwe mʼbale weniweni wa abale ako, amene amanyoza amuna awo ndi ana awo. Amayi ako anali Mhiti ndipo abambo ako anali Mwamori. 46Mkulu wako anali Samariya, ndipo iye pamodzi ndi ana ake aakazi ankakhala cha kumpoto kwako. Mngʼono wako, Sodomu ankakhala cha kummwera kwako pamodzi ndi ana ake aakazi. 47Iwe sunangotsatira kokha njira zawo zoyipa ndi kuchita zonyansa zawo, koma patangopita nthawi pangʼono machitidwe ako oyipa anaposa awo. 48Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, ngakhale mʼbale wako Sodomu ndi ana ake aakazi sanachitepo zimene iwe ndi ana ako aakazi munachita.

49“ ‘Tsono tchimo la mʼbale wako Sodomu linali ili: Iye ndi ana ake aakazi ankanyadira kuchuluka kwa chakudya ndi chuma chawo. Koma sanalabadireko kuthandiza osauka ndi aumphawi. 50Anali odzitukumula ndipo ankachita zonyansa pamaso panga. Nʼchifukwa chake ndinawachotsa monga mmene waoneramu. 51Samariya sanachite ngakhale theka la machimo amene unachita. Iwe wachita zinthu zonyansa zambiri kuposa iwo, motero kuti abale ako awiriwo amaoneka ngati olungama kuyerekeza ndi iye. 52Tsono iwenso uyenera kuchita manyazi popeza waonetsa abale ako ngati osachimwa. Popeza kuti machimo ako ndi onyansa kwambiri kupambana awo, tsonotu iwowo akuoneka olungama kupambana iweyo. Choncho iwenso uchite manyazi ndi kunyozedwa popeza unaonetsa abale ako ngati olungama.

53“ ‘Koma, ndidzadalitsanso Sodomu ndi ana ake aakazi. Ndidzadalitsanso Samariya ndi ana ake aakazi. Pa nthawi yomweyo ndidzakudalitsanso iwe Yerusalemu. 54Ndidzatero kuti uchite manyazi ndi kunyozeka chifukwa cha zonse zimene unachita powatonthoza anthuwa. 55Motero mʼbale wako Sodomu ndi ana ake akadzakhala monga mmene analili poyamba paja, ndiponso mʼbale wako Samariya akadzakhalanso monga mmene anali poyamba paja, ndiye kuti iwenso ndi ana ako mudzakhala monga mmene munalili payamba paja. 56Kale lija pamene unkanyada, suja unkanyogodola mʼbale wako Sodomu 57kuyipa kwako kusanadziwike? Koma tsopano wafanana naye. Wasandukano chinthu chonyozeka kwa anthu a ku Edomu ndi kwa onse owazungulira ndiponso kwa Afilisti. Ndithu onse amene akuzungulira amakunyoza. 58Choncho udzalangidwa chifukwa cha zigololo zako ndi machitidwe anu onyansa, akutero Yehova.

59“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakulanga molingana ndi zimene unachita. Iwe unanyoza lumbiro lako pophwanya pangano langa. 60Komabe, Ine ndidzakumbukira pangano limene ndinachita nawe mʼmasiku a unyamata wako, ndipo ndidzakhazikitsa pangano losatha ndi iwe. 61Tsono udzakumbukira njira zako zakale. Udzachita manyazi polandiranso abale ako, wamkulu ndi wamngʼono yemwe. Ndidzawaperekanso kwa iwe kuti akhale ngati ana ako ngakhale kuti sali a mʼpangano langa ndi iwe. 62Kotero ndidzakhazikitsa pangano langa ndi iwe, ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 63Ndikadzakukhululukira zoyipa zako zonse zimene unachita, udzazikumbukira ndipo udzachita manyazi kwambiri, kotero kuti sudzatha nʼkuyankhula komwe, akutero Ambuye Yehova.’ ”