Ezekieli 11 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 11:1-25

Chiweruzo pa Atsogoleri a Israeli

1Pamenepo Mzimu wa Mulungu unandinyamula ndi kubwera nane ku chipata cha kummawa cha Nyumba ya Yehova. Kumeneko pa khomo la chipata panali anthu 25, ndipo ndinaona pakati pawo atsogoleri awa: Yaazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya. 2Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, awa ndi anthu amene akukonza zoyipa ndi kupereka malangizo oyipa mu mzindamo. 3Iwo amawuza anthu kuti, ‘Nthawi sinafike yoti timange Nyumba? Mzindawu uli ngati mʼphika umene uli pa moto ndipo ife tili ngati nyama mu mʼphikamo. 4Choncho iwe mwana wa munthu, unenere mowadzudzula. Nenera ndithu.’ ”

5Ndipo Mzimu wa Yehova unandigwera ndipo unandiwuza kuti, “Unene kuti zimene akunena Yehova ndi izi. Iye akuti. ‘Izi ndi zimene mukunena, Inu Aisraeli, koma Ine ndikudziwa zimene zili mu mtima mwanu.’ 6Mwapha anthu ambiri mu mzinda muno ndipo mwadzaza misewu yake ndi mitembo.

7“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Mitembo imene mwayiponya mʼmisewuyo ndiyo nyama ndipo mzinda uno ndiwo mʼphika, koma Ine ndidzakuthamangitsanimo. 8Inu mumaopa lupanga, koma lupangalo ndi limene ndidzakubweretsereni, akutero Ambuye. 9Ine ndidzakuthamangitsani mu mzinda ndipo ndidzakuperekani mʼdzanja la alendo kuti akulangeni. 10Mudzaphedwa ndi lupanga ndipo ndidzakulangani mpaka kumalire a Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 11Mzinda uno sudzakhala ngati mʼphika wokutetezani ndipo simudzakhalanso ngati nyama ya mʼmenemo. Ndidzakulangani mpaka kumalire a Israeli. 12Ndipo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Inu simunatsatire malangizo anga kapena kusunga malamulo anga koma mwakhala mukutsata zochita za mitundu ina ya anthu imene yakuzungulirani.’ ”

13Tsono pamene ndinkanenera, Pelatiya mwana wa Benaya anafa. Pomwepo ndinadzigwetsa pansi chafufumimba ndipo ndinafuwula ndi mawu aakulu kuti “Mayo, Ambuye Yehova! Kodi mudzawatheratu Aisraeli onse otsala?”

14Yehova anayankhula nane kuti, 15“Anthu okhala ku Yerusalemu akuwanena abale ako, anthu a ku ukapolo, onse a banja la Israeli, kuti, ‘Anthu onse amene anatengedwa ukapolo ali kutali ndi Yehova. Dziko lanu Yehova anatipatsa kuti likhale lathulathu.’ ”

Mulungu Alonjeza za Kubwerera kwa Israeli

16“Nʼchifukwa chake nena kwa anzako a ku ukapolo kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Ine ndinawatumiza kutali pakati pa anthu a mitundu ina. Ndinawabalalitsa ku mayiko ambiri. Komabe ndakhala ndikuwasunga ku mayiko kumene anapitako!’

17“Nʼchifukwa chake uwawuze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena kuti, Ndidzawasonkhanitsa kuchokera kwa anthu a mitundu inayo ndi kuwasonkhanitsira pamodzi kuchokera ku mayiko kumene ndinawabalalitsirako. Pambuyo pake ndidzawapatsa dziko la Israeli.

18“Akadzalowa mʼdzikomo adzachotsa mafano awo onse oyipa ndi onyansa. 19Ndidzawapatsa mtima watsopano ndipo ndidzayika mzimu watsopano mwa iwo. Ndidzachotsa mtima wowuma ngati mwala mwa iwo, ndipo ndidzawapatsa mtima wofewa ngati mnofu. 20Motero adzatsata malamulo anga ndipo adzasunga mosamala malamulo anga. Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo. 21Koma kunena za amene akupembedza mafano oyipa ndi onyansa, ndidzawalanga chifukwa cha zimene achita. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”

22Tsono akerubi aja anatambasula mapiko awo kuyamba kuwuluka, mikombero ili mʼmbali mwawo. Ulemerero wa Mulungu wa Israeli unali pamwamba pawo. 23Ulemerero wa Yehova unakwera ndi kusiya mzindawo ndipo unakayima pa phiri cha kummawa kwake kwa mzindawo. 24Pambuyo pake Mzimu wa Mulungu unandinyamula ndi kukandifikitsa. Zimenezi zinkachitika mʼmasomphenya monga mmene Mzimu wa Mulungu unkandionetsera.

Kenaka masomphenya amene ndinkawaonawo anayamba kuzimirira. 25Ndipo ndinafotokozera akapolowo zonse zimene Yehova anandionetsa.

New Russian Translation

Иезекииль 11:1-25

Суд над вождями Израиля

1Дух поднял меня и перенес к тем воротам Господнего дома, что смотрят на восток. Там, у входа в ворота, было двадцать пять человек, и среди них я увидел Иазанию, сына Азура, и Пелатию, сына Беная, вождей народа.

2Господь сказал мне:

– Сын человеческий, вот люди, которые замышляют зло и дают в этом городе злые советы. 3Они говорят: «Разве не скоро придет время строить дома? Этот город – котел, а мы – мясо». 4Поэтому пророчествуй против них; пророчествуй, сын человеческий.

5Дух Господень сошел на меня и сказал мне:

– Скажи: «Так говорит Господь: Вот о чем вы думаете, дом Израиля. Я знаю то, что приходит вам на ум. 6Вы многих убили в этом городе и завалили его улицы трупами. 7Поэтому так говорит Владыка Господь: Ваши убитые, которых вы положили в нем – это мясо, а этот город – котел, но вас Я изгоню из него. 8Вы страшитесь меча, и Я пошлю на вас меч, – возвещает Владыка Господь. – 9Я изгоню вас из города, отдам во власть чужеземцев и исполню над вами приговор. 10Вы падете от меча; Я буду судить вас на границе Израиля. Тогда вы узнаете, что Я – Господь. 11Этот город не будет для вас котлом, а вы не будете в нем мясом; Я буду судить вас на границе Израиля. 12Тогда вы узнаете, что Я – Господь, потому что вы не соблюдали Моих установлений и не исполняли законов, но поступали по обычаям народов, которые вокруг вас».

13Пока я пророчествовал, Пелатия, сын Бенаи, умер. Тогда я пал ниц и громко закричал:

– О Владыка Господи! Неужели Ты до конца погубишь всех оставшихся в живых в Израиле?

Утешение пленникам

14Было ко мне слово Господа:

15– Сын человеческий, твои сородичи, твоя родня, те, кто разделил с тобой плен11:15 Букв.: «те, кто с тобой в родстве»., и весь дом Израиля – это те, о ком жители Иерусалима говорят: «Они далеко от Господа; эта земля отдана во владение нам».

16– Поэтому скажи: «Так говорит Владыка Господь: Хотя Я и изгнал их к другим народам и рассеял по странам, Я Сам на время11:16 Или: «в некой мере». стал для них святилищем в тех странах, куда они ушли».

17Поэтому скажи: «Так говорит Владыка Господь: Я соберу вас из народов и верну из стран, по которым вы были рассеяны, и опять отдам вам землю Израиля».

18Когда они вернутся туда, они уберут из нее все мерзости и все ее гнусности. 19Я дам им единое сердце и вложу в них новый дух; Я возьму у них сердце из камня и дам им сердце из плоти. 20Тогда они будут соблюдать Мои установления, хранить Мои законы и исполнять их. Они будут Моим народом, а Я буду их Богом. 21Но на головы тех, чьи сердца обращены к их гнусным истуканам и омерзительным идолам11:21 Букв.: «Но к сердцу их гнусностей и мерзостей их сердце идет»., Я обрушу то, что они заслужили, – возвещает Владыка Господь.

Слава Господня покидает Иерусалим

22И херувимы, с колесами возле них, расправили крылья, и слава Бога Израилева была над ними. 23Слава Господня поднялась из города и остановилась над горой к востоку от него. 24Дух поднял меня и перенес к пленникам в Халдею11:24 То есть в Вавилон; евр.: «касдим»; также в остальных местах книги. в видении, которое было дано Духом Божьим.

Потом видение, которое я видел, покинуло меня, 25и я рассказал пленникам обо всем, что показал мне Господь.