Ezara 9 – CCL & NSP

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezara 9:1-15

Pemphero la Ezara pa za Kukwatirana ndi a Mitundu Ina

1Zitachitika izi, atsogoleri anabwera kwa ine nati, “Aisraeli, kuphatikizanso ansembe ndi Alevi, sanadzipatule ku makhalidwe onyansa a anthu a mitundu ina amene ayandikana nafe: Akanaani, Ahiti, Aperezi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aigupto ndi Aamori. 2Zomwe zikuchitika ndi izi. Aisraeli ena ndi ana awo aamuna anayamba kukwatira ana aakazi a anthuwa. Choncho mtundu wopatulika wadzisokoneza ndi mitundu ya anthu a mʼderali. Ndipo atsogoleri ndi akuluakulu ndiwo akupambana pa makhalidwe osakhulupirikawa.”

3Nditamva zimenezi, ndinangʼamba chovala changa ndi mwinjiro wanga ndipo ndinamwetula tsitsi la kumutu kwanga ndi ndevu zanga nʼkukhala pansi ndili wokhumudwa. 4Ndinakhala pansi chomwecho wokhumudwa mpaka nthawi ya nsembe ya madzulo. Ndipo onse amene ankaopa mawu a Mulungu wa Israeli chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu obwerako ku ukapolo anayamba kubwera kwa ine kudzasonkhana.

5Ndipo pa nthawi ya nsembe ya madzulo, ndinadzidzimuka mu mtima wanga wokhumudwa nʼkuyimirira, zovala zanga ndi mwinjiro wanga zikanali zongʼambika ndipo ndinagwada ndi kukweza manja anga kwa Yehova Mulungu wanga 6ndipo ndinapemphera kuti,

“Inu Mulungu wanga, ndine wamanyazi ndi wachisoni moti sindingathe kukweza nkhope yanga kwa Inu Mulungu wanga, chifukwa machimo athu akwera kupambana mitu yathu, ndipo kulakwa kwathu kwafika ku thambo. 7Ndipo chifukwa cha machimo athu, ifeyo, mafumu athu, ndi ansembe athu takhala akutipereka mʼmanja mwa mafumu a mitundu ina ya anthu kuti atiphe pa nkhondo, atitenge ku ukapolo, atilande zinthu zathu ndi kutichititsa manyazi monga zilili leromu.

8“Koma tsopano, pa kanthawi kochepa, Inu Yehova Mulungu wathu mwaonetsa kukoma mtima. Inu mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke ku ukapolo ndi kutipatsa cholowa mʼmalo anu oyera. Mwatipulumutsa ku ukapolo ndi kutipatsa mpumulo pangʼono mu ukapolo wathu. 9Ndifedi akapolo. Koma Inu Yehova simunatileke mu ukapolo wathu. Mwationetsa chikondi chanu chosasinthika pamaso pa mafumu a ku Perisiya. Mwatitsitsimutsa kuti timange Nyumba yanu pokonzanso mabwinja ake. Mwatitchinjiriza mʼdziko la Yuda ndi Yerusalemu.

10“Koma tsopano, Inu Mulungu wathu, kodi tinganene chiyani titachita zoyipa zonsezi? Ife taphwanya malamulo anu 11amene munawapereka kudzera mwa atumiki anu aneneri. Inu munati, ‘Dziko limene mukulowamolo kuti likhale cholowa chanu, ndi dziko lodetsedwa ndi zonyansa za mitundu ya mʼmayikomo. Ndipo adzaza dzikolo ndi zochita zawo zonyansa. 12Nʼchifukwa chake, musapereke ana anu aakazi kuti akwatiwe ndi ana awo aamuna kapena kulola kuti ana awo aakazi akwatiwe ndi ana anu aamuna. Musagwirizane nawo, kapena kuchita nawo malonda kuti mukhale amphamvu ndi kudya zokoma za mʼdzikomo ndi kusiyira ana anu dzikoli ngati cholowa chawo mpaka kalekale.’

13“Tsono pambuyo pa zonse zimene zatigwera chifukwa cha ntchito zathu zoyipa ndi uchimo wathu waukulu, komanso pambuyo poona kuti Inu Mulungu wathu simunangotilanga kokha pangʼono kuyerekeza ndi kuchimwa kwathu komanso mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke, 14kodi ife nʼkuphwanyanso malamulo anu ndi kukwatirana ndi anthu amitundu ina amene amachita zonyansa zimenezi? Kodi simudzatikwiyira ndi kutiwononga kwathunthu popanda wina wotsala kapena wopulumuka? 15Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, ndinu wachifundo, pakuti ndife otsala amene tapulumuka monga mmene zilili lero lino. Ife tayima pamaso panu ngakhale tikudziwa kuchimwa kwathu pakuti palibe munthu amene angathe kuyima pamaso panu chifukwa cha machimo ake.”

New Serbian Translation

Јездрина 9:1-15

Јездрина молитва због женидбе са туђинкама

1Када се све ово завршило, приступили су ми главари и рекли: „Израиљски народ, свештеници и Левити се нису одвојили од народа земаљских и њихових одвратности, од Хананаца, Хетита, Фережана, Јевусеја, Амонаца, Моаваца, Египћана и Аморејаца. 2Узели су неке од њихових ћерки за себе и своје синове, па су помешали свети род са народима земаљским. У овом неверству су предњачили главари и достојанственици.“

3А ја, чим сам чуо за ову ствар, раздерао сам своју одећу и плашт, чупао косу са главе и браде, па сам сео као скамењен. 4Око мене су се окупили сви који су се бојали од речи Бога Израиља, због неверства повратника из изгнанства, а ја сам седео као скамењен све до вечерње жртве.

5А током вечерње жртве сам устао из своје понижености, па сам раздеране одеће и плашта, пао на колена и раширио руке Господу, мом Богу. 6Рекао сам:

„О, мој Боже! Срамота ме је и постиђен сам да бих подигао, о, мој Боже, своје лице к теби, јер су наше кривице нарасле преко главе и грех је наш велик до небеса. 7Још од времена наших очева у греху смо великом све до ових дана. Због наших кривица смо били дани ми, наши цареви и наши свештеници у руке царева земаљских – под мач, у изгнанство, за отимачину и срамоту све до данас.

8А сада, на трен нам је дошла милост од Господа, Бога нашег: да нам остави остатак; да нам да упориште у месту своје светости; да нам просветли очи наше Бог наш, и да нам да мало живнемо у свом робовању. 9Јер, ми смо робље, али у нашем робовању наш нас Бог није напустио: смиловао нам се пред царевима Персије да оживимо, да се подигне Дом нашег Бога и поправе његове рушевине, да нам да зид у Јуди и у Јерусалиму.

10И шта сад да кажемо, о, Боже наш, после овог?! Јер, напустили смо твоје заповести 11које си нам заповедио преко својих слугу, пророка: ’Земља у коју идете да је запоседнете је нечиста земља због нечистоће земаљских народа. Напунили су је својим одвратностима и нечистоћама с краја на крај. 12Зато не удајите своје ћерке за њихове синове нити узимајте њихове ћерке за своје синове. Не тражите трајни мир и корист са њима, да бисте остали јаки, да бисте јели добра земље и оставили је у наследство својим синовима довека.’

13И после свега тога што је дошло на нас, због наших злодела и наших великих греха, ипак си нас, Боже наш, поштедео више него што су наше кривице заслужиле, и дао нам остатак као што је овај. 14Зар да узвратимо кршењем твојих заповести и орођавамо се са народима оваквих одвратности? Зар се не би разгневио на нас и докрајчио нас тако да више не буде ни остатка ни преживелих? 15О, Господе, Боже Израиљев, ти си праведан јер смо преостали као остатак, као што је данас. Ево нас пред тобом у нашим гресима и због тога не можемо да стојимо пред тобом.“