Ezara 8 – CCL & KLB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezara 8:1-36

Mʼndandanda wa Akuluakulu a Mabanja Amene Anabwera ndi Ezara

1Nawa mayina a atsogoleri a mabanja amene anabwera nane kuchokera ku Babuloni nthawi ya ulamuliro wa mfumu Aritasasita:

2Geresomu wa fuko la Finehasi;

Danieli wa fuko la Itamara;

Hatusi 3mwana wa Sekaniya wa fuko la Davide;

Zekariya wa fuko la Parosi. Pamodzi ndi iyeyu panalembedwa anthu ena 150;

4Elihunai mwana wa Zerahiya, wa fuko la Pahati-Mowabu. Pamodzi ndi iyeyu panalinso anthu ena 400.

5Sekaniya, mwana wa Yahazieli wa fuko la Zatu. Pamodzi ndi iyeyu panalembedwanso anthu 300.

6Ebedi, mwana wa Yonatani wa fuko la Adini. Pamodzi naye analembedwanso anthu ena makumi asanu.

7Yesaiya, mwana wa Ataliya wa fuko la Elamu. Pamodzi naye panali anthu ena 70.

8Zebadiya, mwana wa Mikayeli wa fuko la Sefatiya. Pamodzi naye panalinso anthu 80.

9Obadiya, mwana wa Yehieli wa fuko la Yowabu. Pamodzi naye panalinso anthu 218.

10Selomiti mwana wa Yosifiya wa fuko la Bani. Pamodzi ndi iyeyu panalinso anthu 160.

11Zekariya, mwana wa Bebai wa fuko la Babai. Pamodzi naye analembedwanso anthu 28.

12Yohanani, mwana wa Hakatani wa fuko la Azigadi. Pamodzi naye panalinso anthu 110.

13Atsogoleri a fuko la Adonikamu, anthu amene anabwera pambuyo pake mayina awo anali Elifeleti, Yeiyeli ndi Semaya. Pamodzi ndi iwowa panalinso anthu 60.

14Atsogoleri a fuko la Bigivai anali Utai ndi Zakuri. Pamodzi ndi iwowa panali anthu 70.

Kubwerera ku Yerusalemu

15Anthu onse ndinawasonkhanitsa ku mtsinje umene umapita mpaka ku Ahava, ndipo kumeneko tinagona mʼmisasa masiku atatu. Nditayangʼana pakati pa anthu ndi ansembe, ndinapeza kuti panalibe Alevi. 16Choncho ndinayitana atsogoleri awa: Eliezara, Arieli, Semaiya, Elinatani, Yaribu, Elinatani, Natani, Zekariya ndi Mesulamu, pamodzi ndi aphunzitsi awiri, Yoyaribu ndi Elinatani, 17ndipo ndinawatuma kwa Ido, mtsogoleri wa malo otchedwa Kasifiya. Ine ndinawawuza zoti akanene kwa Ido ndi kwa abale ake, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ku Kasifiyako, kuti atitumizire anthu odzatumikira ku Nyumba ya Mulungu. 18Chifukwa cha kutikomera mtima kwa Mulungu wathu, Ido anatitumizira munthu wanzeru, Serabiya, wa fuko la Mahili, mwana wa Levi, mwana wa Israeli, pamodzi ndi ana ake aamuna ndi abale ake, anthu 18. 19Anatitumiziranso Hasabiya ndi Yesaiya wa fuko la Merari pamodzi ndi abale ake ndi adzukulu ake, anthu makumi awiri. 20Panalinso anthu ena 220 mwa anthu ogwira ntchito mʼNyumba ya Mulungu amene Davide ndi nduna zake anawasankha kuti azitumikira Alevi. Anthu onsewa analembedwa potsata mayina awo.

21Ku mtsinje wa Ahava, ndinalengeza kuti anthu onse asale zakudya, adzichepetse pamaso pa Mulungu wathu ndi kupempha kuti atiyendetse bwino ife ndi ana athu, ndi kuteteza katundu wathu yense. 22Ine ndinali ndi manyazi kupempha mfumu kuti atipatse asilikali oyenda pansi ndi ena okwera pa akavalo kuti atiteteze kwa adani athu pa ulendo wathuwu popeza tinali titawuza kale mfumu kuti “Yehova amateteza aliyense amene amamudalira, koma amakwiyira onse amene amamukana.” 23Choncho tinasala zakudya ndi kupemphera kwa Mulungu wathu kuti atiteteze ndipo Iye anamva pemphero lathu.

24Tsono ndinasankha atsogoleri a ansembe khumi ndi awiri awa, Serebiya, Hasabiya ndi abale awo khumi 25ndipo ndinawayezera siliva ndi golide, ndiponso ziwiya ndi zopereka za ku Nyumba ya Mulungu wathu zimene mfumu ndi alangizi ake, nduna zake ndi Aisraeli onse amene anali kumeneko anazipereka. 26Nditayeza zonse, ndinapereka mʼmanja mwawo, matani 22 asiliva, ziwiya zasiliva zolemera makilogalamu 70, ndiponso makilogalamu 3,400 a golide, 27mbale zagolide makumi awiri zolemera makilogalamu asanu ndi atatu ndi theka ndiponso ziwiya ziwiri zamkuwa wosalala, wonyezimira bwino ngati golide wamtengowapatali.

28Kenaka ndinawawuza kuti, “Inu ndi opatulika a Yehova, ndiponso mphatso zonsezi ndi zopatulika. Siliva ndi golideyu ndi zopereka zaufulu kwa Yehova, Mulungu wa makolo anu. 29Muzisamale bwino mpaka mutaziyeza pamaso pa atsogoleri a ansembe ndi Alevi ndi akulu a mabanja a Israeli mʼzipinda za mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu.” 30Choncho ansembe ndi Alevi analandira zonse zoyezedwa zija, siliva, golide pamodzi ndi ziwiya kuti apite nazo ku Nyumba ya Yehova ku Yerusalemu.

31Pa tsiku la khumi ndi chiwiri la mwezi woyamba, tinachoka ku mtsinje wa Ahava kupita ku Yerusalemu. Ndipo Mulungu wathu anali nafe, ndipo anatiteteza kwa adani athu makamaka otibisalira pa njira. 32Tinafika ku Yerusalemu, komwe tinapumula masiku atatu.

33Pa tsiku la chinayi lake, mʼNyumba ya Mulungu wathu, tinayeza siliva ndi golide ndi ziwiya zija nʼkuzipereka mʼmanja mwa Meremoti mwana wa wansembe Uriya. Pamodzi ndi iyeyo panali Eliezara mwana wa Finehasi ndiponso Alevi awa: Yozabadi mwana wa Yesuwa ndi Nowadiya mwana wa Binuyi. 34Zonsezi anaziwerenga ndi kuziyeza ndipo analemba kulemera kwa chinthu chilichonse.

35Pamenepo anthu amene anatengedwa ukapolo aja anabwerera, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israeli: ngʼombe zazimuna khumi ndi ziwiri, kuperekera Aisraeli onse, nkhosa zazimuna 96, ana ankhosa 77, ndiponso mbuzi zazimuna khumi ndi ziwiri ngati nsembe yopepesera machimo. Zonsezi zinali nsembe yopsereza zopereka kwa Yehova. 36Iwo anaperekanso chidziwitso cha mfumu chija kwa akuluakulu a mfumu ndi kwa akazembe a mʼdera la Patsidya pa Yufurate. Pamenepo iwo anathandiza Ayuda ndiponso ntchito za pa Nyumba ya Mulungu.

Korean Living Bible

에스라 8:1-36

에스라와 함께 돌아온 족장들

1아르타크셀크세스황제 때에 에스라와 함께 바빌로니아에서 예루살렘으로 돌 아온 족장들과 그 집안 사람들은 다음과 같다:

2비느하스 집안에서 게르솜,

3이다말 집안에서 다니엘, 다윗 집안에서 스가냐의 자손인 핫두스, 바로스 집안에서 스가랴와 그리고 그와 함께 족보에 기록된 남자 150명,

4바핫 – 모압 집안에서 스라히야의 아들 엘여호에내와 그 밖의 남자 200명,

58:5 원문에는이말이빠져있음.삿두 집안에서 야하시엘의 아들 스가냐와 그 밖의 남자 300명,

6아딘 집안에서 요나단의 아들 에벳과 그 밖의 남자 50명,

7엘람 집안에서 아달랴의 아들 여사야와 그 밖의 남자 70명,

8스바댜 집안에서 미가엘의 아들 스바댜와 그 밖의 남자 80명,

9요압 집안에서 여히엘의 아들 오바댜와 그 밖의 남자 218명,

108:10 원문에는이말이빠져있음.바니 집안에서 요시뱌의 아들 슬로밋과 그 밖의 남자 160명,

11베배 집안에서 베배의 아들 스가랴와 그 밖의 남자 28명,

12아스갓 집안에서 학가단의 아들 요하난과 그 밖의 남자 110명,

13아도니감 집안에서 마지막으로 돌아온 엘리벨렛과 여우엘과 스마야와 그 밖의 남자 60명,

14비그왜 집안에서 우대와 8:14 또는 ‘사붓’삭굴과 그 밖의 남자 70명이었다.

예루살렘으로 돌아옴

15우리는 아하와 강가에 모여 천막을 치고 거기서 3일을 머물면서 백성들과 제사장들의 인원을 점검했는데 그때 레위 사람은 하나도 없었다.

16그래서 나 에스라는 레위 사람의 지도자인 엘리에셀, 아리엘, 스마야, 엘라단, 야립, 또 다른 엘라단, 나단, 스가랴, 므술람, 그리고 지혜로운 사람 요야립과 엘라단을 불러오게 하여

17그들을 가시뱌 지방의 지도자 잇도에게 보내며 그와 그의 친척들과 성전 봉사자들에게 성전에서 하나님을 섬길 사람들을 보내 달라고 부탁하였다.

18하나님이 우리를 도우셨으므로 그들은 마흘리 집안의 레위 사람인 유능한 세레뱌와 그리고 그의 아들들과 형제들을 합하여 모두 18명을 보내 주었고

19또 하사뱌와 함께 므라리 집안의 8:19 또는 ‘여사야와 그 형제와 저의 아들들’여사야와 그의 친척 20명도 보내 주었다.

20그 외에도 다윗과 그의 신하들이 레위인을 도와 잡일을 하게 한 성전 봉사자들 220명도 함께 보내 주었으며 그들의 이름은 귀환자 명단에 다 기록되었다.

21그때 우리는 아하와 강가에서 금식하고 우리 하나님 앞에서 자신을 낮추며 여행하는 동안 우리를 인도하여 우리 자녀들과 우리의 모든 소유물을 보호해 달라고 기도하였다.

22나는 전에 황제에게 우리 하나님은 자기를 신뢰하는 모든 사람을 축복하시지만 자기를 저버리는 사람은 누구든지 벌하시는 분이라고 말한 적이 있었기 때문에 황제에게 군대를 보내서 도중에 원수들로부터 우리를 지켜 달라고 부탁하는 것을 부끄럽게 여겼다.

23그래서 우리는 이 문제를 놓고 금식하며 하나님께 기도하여 우리를 보호해 주시겠다는 응답을 받았다.

24그때 나는 세레뱌와 하사뱌를 포함한 12명의 지도자급 제사장들을 뽑아 세우고

25황제와 그의 자문관들과 신하들과 이스라엘 백성이 우리 하나님의 성전을 위해 바친 은과 금과 그 밖의 그릇들을 그들에게 주었다.

26내가 그들에게 준 것은 8:26 히 ‘은 650달란트’은 약 22톤, 8:26 히 ‘은 기명 100달란트’은그릇 3,400킬로그램, 금 3,400킬로그램,

27금대접만큼 값진 놋그릇 2개, 그리고 금대접 20개였는데 이 금대접들은 금 8:27 히 ‘1,000다릭’8.4킬로그램의 값에 해당하는 것이었다.

28그러고서 나는 그들에게 이렇게 말하였다. “여러분은 이 그릇과 마찬가지로 여호와께 거룩한 자들입니다. 이 모든 금과 은은 우리 조상의 하나님 여호와께 기쁘게 바친 예물이므로

29여러분은 이 모든 것을 예루살렘의 성전까지 가지고 가서 지도급 제사장들과 레위인들과 이스라엘 백성의 지도자들 앞에서 이것을 달아 인계할 때까지 잘 간수하고 지켜야 합니다.”

30그래서 제사장들과 레위인들은 그 금과 은과 그릇을 예루살렘 성전까지 가져갈 책임을 맡았다.

31우리가 아하와 강가를 떠나 예루살렘을 향해 출발한 때는 월 12일이었다. 우리 하나님께서는 우리와 함께하셔서 도중에 적의 공격과 도적떼로부터 우리를 지켜 주셨으므로

32우리는 예루살렘에 무사히 도착하여 3일 동안의 휴식을 취하였다.

33그런 다음 4일째 되는 날 우리는 성전으로 가서 비느하스의 아들 엘르아살과 두 레위인 예수아의 아들 요사밧과 빈누이의 아들 노아댜가 보는 가운데 우리아의 아들 제사장 므레못에게 그 은과 금과 그릇을 넘겨 주었으며

34그 모든 것은 개수를 세고 무게를 달아 즉석에서 장부에 기록하였다.

35그러고서 포로 생활을 하다가 돌아온 모든 사람들이 이스라엘의 하나님께 불로 태워 바치는 번제를 드렸다. 그들이 바친 제물은 모든 이스라엘 백성을 위한 수송아지 12마리와 숫양 96마리, 어린 양 77마리, 그리고 속죄제물로 숫염소 12마리였다.

36그런 다음 그들이 유프라테스강 서쪽 지방의 총독과 관리들에게 황제의 명령이 적힌 편지를 전하자 그들은 하나님의 성전을 짓는 일에 적극 협조하였다.