Ezara 5 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezara 5:1-17

Kalata ya Tatenai Yopita kwa Dariyo

1Nthawi imeneyo aneneri Hagai ndi Zekariya, mwana wa Ido, ankayankhula kwa Ayuda okhala mʼdziko la Yuda ndi mu Yerusalemu mʼdzina la Mulungu wa Israeli, amene anali nawo. 2Pambuyo pake Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki ananyamuka nakayambanso kumanga Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Ndipo aneneri a Mulungu anali nawo pamodzi, kuwathandiza.

3Pa nthawi imeneyo Tatenai, bwanamkubwa wa chigawo cha patsidya pa Yufurate pamodzi ndi Setari-Bozenai ndi anzawo anapita kwa iwo ndi kukawafunsa kuti, “Anakulolani ndani kuti mumangenso Nyumba imeneyi ndi kutsiriza khoma lake?” 4Anawafunsanso kuti, “Kodi anthu amene akumanga nyumbayi mayina awo ndani?” 5Koma Mulungu wawo amayangʼanira atsogoleri Ayuda, motero kuti anthu aja anaganiza kuti asawaletse kumanga Nyumbayo mpaka atalembera mfumu Dariyo kalata ndi kulandira yankho lake.

6Iyi ndi kalata imene Tatenai bwanamkubwa wa dera la patsidya pa Yufurate, ndiponso Setari-Bozenai ndi anzake, akazembe amene anali mʼchigawo cha patsidya pa Yufurate, anatumiza kwa mfumu Dariyo 7Analemba kalatayo motere:

Kwa mfumu Dariyo:

Mukhale ndi mtendere wonse.

8Amfumu mudziwe kuti ife tinapita ku dziko la Yuda ku Nyumba ya Mulungu wamkulu. Nyumbayo ikumangidwa ndi miyala ikuluikulu ndipo akuyala matabwa pa makoma. Ntchitoyi ikugwiridwa mwachangu ndipo ikuyenda bwino kwambiri mwautsogoleri wawo.

9Ndipo tinawafunsa atsogoleriwo kuti, “Anakulolezani kuti mumangenso Nyumbayi ndi kutsiriza makoma ake ndani?” 10Tinawafunsanso mayina a atsogoleri awo, kuti tikalemba mayina atsogoleriwo tidzakudziwitseni kuti muwadziwe.

11Yankho limene anatipatsa ndi ili:

“Ife ndife atumiki a Mulungu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi, ndipo tikumanganso Nyumba imene mfumu ina yamphamvu ya Israeli inamanga ndi kuyitsiriza zaka zambiri zapitazo. 12Koma chifukwa chakuti makolo athu anakwiyitsa Mulungu wakumwamba, Iye anawapereka kwa Nebukadinezara Mkalideya, mfumu ya Babuloni, amene anawononga Nyumbayi ndi kutenga anthu onse kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni.

13“Komabe chaka choyamba cha Koresi, mfumu ya ku Babuloni, mfumu Koresiyo anapereka lamulo lakuti Nyumba ya Mulunguyi imangidwenso. 14Ndipo ziwiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara anazitenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu ndi kukaziyika mʼnyumba ya milungu ya ku Babuloni, anakazichotsa ku nyumba ya milungu ya ku Babuloniko ndi kuzipereka kwa Sesibazara, amene mfumu inamusankha kukhala bwanamkubwa. 15Tsono mfumuyo inamuwuza kuti, ‘Tenga ziwiyazi ukaziyike mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Ndipo Nyumba ya Mulunguyo ikamangidwenso pa maziko ake akale.’

16“Choncho Sesibazarayo anabwera ndi kumanga maziko a Nyumba ya Mulunguyo mu Yerusalemu. Kuyambira tsiku limenelo mpaka lero yakhala ikumangidwa ndipo sinathebe.”

17Nʼchifukwa chake ngati chingakukomereni amfumu, pachitike kafukufuku mʼnyumba yaufumu mosungira chuma ndi mabuku okhudza mbiri ya Babuloni kuti tione ngati mfumu Koresi inalamuladi za kumanganso Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Kenaka amfumu mutiwuze zomwe zikukondweretsani kuti mugamule pa nkhani imeneyi.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以斯拉记 5:1-17

1那时,先知哈该易多的子孙撒迦利亚以色列上帝的名,向犹大耶路撒冷犹大人宣讲上帝的话。 2于是,撒拉铁的儿子所罗巴伯约萨达的儿子耶书亚开始在耶路撒冷重建上帝的殿,上帝的先知在他们身边帮助他们。

3当时,河西总督达乃示他·波斯乃及其同僚来问他们:“谁批准你们重建这殿、修复这墙的?” 4又问道:“建造这殿的人们叫什么名字。” 5然而,上帝看顾犹太人的长老,工程没有被叫停,直到事情呈报给大流士王、收到王的回谕后才停止。

6河西的官员们——河西总督达乃示他·波斯乃及其同僚上奏大流士王, 7奏章如下:

“愿大流士王一切平安! 8王该知道,我们去了犹大省,到了伟大上帝的殿。人们正在用大石建殿,木料已经安在墙里,工程进展迅速、顺利。 9我们问那些长老,‘谁批准你们重建这殿、修复这墙的?’ 10我们又问他们的名字,好记下他们首领的名字禀告王。

11“他们回答说,‘我们是天地之上帝的仆人,我们正在重建这座多年前由以色列的一位伟大君王建造的殿。 12但因为我们的祖先触怒了天上的上帝,上帝把他们交在迦勒底人——巴比伦尼布甲尼撒的手中,他摧毁了这殿,把他们掳到巴比伦13然而,巴比伦塞鲁士在其统治元年,降旨重建这座上帝的殿。 14尼布甲尼撒王曾掳去耶路撒冷上帝殿里的金银器皿,放在巴比伦神庙里,塞鲁士王从巴比伦神庙取出这些器皿,交给他委派做省长的设巴萨15吩咐他把这些器皿带去,重新陈设在耶路撒冷的殿里,在旧址上重建上帝的殿。 16于是,这位设巴萨就在耶路撒冷为上帝的殿立了根基,从那时到如今,殿一直在重建中,还没有竣工。’

17“现在,王若愿意,请查阅巴比伦的王室记录,看看塞鲁士王是否降旨重建耶路撒冷的上帝之殿。王对此事如何决断,请告知我们。”