Ezara 4 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezara 4:1-24

Atsutsa za Kumanganso Nyumba ya Yehova

1Adani a Yuda ndi Benjamini anamva kuti anthu obwera ku ukapolo aja akumangira Nyumba Yehova, Mulungu wa Israeli. 2Tsono anapita kwa Zerubabeli ndi kwa atsogoleri a mabanja awo ndi kunena kuti, “Mutilole kuti tikuthandizeni kumangaku chifukwa ife timapembedza Mulungu wanu monga momwe mumachitira inu, ndipo takhala tikupereka nsembe kwa Iye kuyambira nthawi ya Esrahadoni, mfumu ya ku Asiriya, amene anabwera nafe kuno.”

3Koma Zerubabeli, Yesuwa ndi atsogoleri ena otsala a mabanja a Aisraeli anayankha kuti, “Inu simungatithandize kumangira Nyumba Yehova, Mulungu wathu. Tokha tidzamumangira Nyumba Yehova, Mulungu wa Aisraeli, monga mfumu Koresi, mfumu ya Perisiya inatilamulira.”

4Tsono anthu a mʼdzikomo anayamba kuchititsa ulesi anthu a ku Yuda, ndi kuwachititsa mantha kuti aleke ntchito yomangayo. 5Analemba alangizi ena kuti alepheretse cholinga chawo pa ntchitoyo pa nthawi yonse ya Koresi, mfumu ya ku Perisiya, ndiponso mpaka pamene Dariyo mfumu ya ku Perisiya ankalamulira dzikolo.

Kutsutsa Kwina pa Nthawi ya Ahasiwero ndi Aritasasita

6Mfumu Ahasiwero atangoyamba kulamulira dzikolo, adani aja analemba kalata yoneneza anthu a Yuda ndi Yerusalemu.

7Ndiponso mʼnthawi ya Aritasasita mfumu ya Perisiya, Bisilamu, Mitiredati, Tabeeli ndi anzawo ena analemba kalata inanso kwa Aritasasita. Kalatayo inalembedwa mʼChiaramu ndipo ankatanthauzira poyiwerenga.

8Rehumu mkulu wankhondo ndi Simisai mlembi, nawonso analemba kalata yawo yoneneza anthu a ku Yerusalemu kwa mfumu Aritasasita. Anayilemba motere:

9Kalata yochokera kwa Rehumu, mkulu wa gulu lankhondo, mlembi Simisai ndi anzawo awa: oweruza, nduna, akuluakulu ena, anthu a ku Peresiya, Ereki, Babuloni, Susa mʼdziko la Elamu, 10ndi mitundu ina imene mkulu wolemekezeka, Osanipara anayisamutsa ndi kuyikhazika mʼmizinda ya Samariya ndi mʼmadera ena apatsidya la Yufurate.

11Mawu a mʼkalata ya kwa Aritasasita anali awa:

Kwa mfumu Aritasasita:

Kuchokera kwa atumiki anu, anthu a kutsidya kwa Yufurate:

12Amfumu tati mudziwe kuti Ayuda amene anabwera kuno kuchokera kwanuko apita ku Yerusalemu ndipo akumanganso mzinda wa anthu owukira ndi oyipa uja. Akumaliza makoma ake ndipo akukonzanso maziko.

13Kuwonjeza apo amfumu mudziwe kuti ngati amalize kumanganso mzindawu ndi kukonzanso makoma ake, adzaleka kukhoma msonkho, kulipira ndalama zakatundu olowa mʼdziko kapena msonkho wina uliwonse, ndipo chuma cha thumba la ufumu chidzachepa. 14Popeza tsono ife timadya nawo kwa mfumu sitiyenera tizingoonerera zinthu zochititsa mfumu manyazi. Nʼchifukwa chake tikutumiza uthenga kwa inu a mfumu kuti mudziwe zonse. 15Choncho pachitike kafukufuku mʼbuku la mbiri yakale ya makolo anu. Mʼbuku la mbiri zakale mudzapezamo ndi kuwerenga kuti mzinda umenewu ndi waupandu, wosautsa mafumu ndi nduna zamʼmadera zomwe. Kuyambira kale wakhala ukuwukira ulamuliro uliwonse. Nʼchifukwa chake mzinda umenewu anawuwononga. 16Tsono tikukudziwitsani amfumu kuti ngati mzinda umenewu umangidwanso ndi makoma ake nʼkutsirizidwanso ndiye kuti inu simudzalamuliranso chigawo cha patsidya pa Yufurate.

17Mfumu inatumiza yankho ili:

Mkulu wa gulu lankhondo Rehumu, mlembi Simisai ndi anzanu onse amene akukhala ku Samariya ndi mʼzigawo zina zonse za Patsidya pa Yufurate.

Landirani moni.

18Kalata imene munatumiza ija yawerengedwa bwino lomwe pamaso panga. 19Ine nditalamula kuti afufuze nkhaniyi kwapezekadi kuti mzinda umenewu uli ndi mbiri yowukira mafumu ndi kuti zaupandu ndi zowukira zinkachitikadi mʼmenemo. 20Mafumu amphamvu akhala akulamulira Yerusalemu ndi chigawo chonse cha Patsidya pa Yufurate. Iwo ankalandira msonkho ndi kulipira ndalama zakatundu olowa mʼdziko pa kanthu kena kalikonse. 21Tsopano inu khazikitsani lamulo kuti anthu amenewo asiye ntchitoyo, asamangenso mzindawo mpaka ine nditalamula 22Musachedwe kuchita zimenezi. Kodi ine ndingalole bwanji kuti zowononga zotere zikule ndi kupweteka ine mfumu?

23Kalata ya mfumu Aritasasitayi itangowerengedwa pamaso pa Rehumu ndi Simisai mlembi uja, ndi anzawo onse, iwo anapita msangamsanga ku Yerusalemu kukawaletsa Ayuda aja mwamphamvu kuti asapitirire ntchito yawo.

24Motero ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu inayimitsidwa mpaka chaka cha chiwiri cha ulamuliro wa Dariyo mfumu ya ku Perisiya.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以斯拉记 4:1-24

建殿工作受阻

1犹大便雅悯的敌人听说流亡者回来要为以色列的上帝耶和华建殿, 2就去见所罗巴伯以色列的族长,对他们说:“请让我们与你们一同建造,因为我们像你们一样也寻求你们的上帝。自从亚述以撒哈顿带我们到这里以后,我们就一直献祭给上帝。” 3所罗巴伯耶书亚以色列其余的族长回答说:“你们不能参与建殿。遵照波斯塞鲁士的吩咐,我们要自己为以色列的上帝耶和华建殿。”

4于是,当地人阻挠犹大人,使他们不敢建殿, 5波斯塞鲁士统治年间,一直到波斯大流士统治期间,当地人收买谋士,破坏他们的计划。

阻扰重建耶路撒冷

6亚哈随鲁统治初期,他们写信控告犹大耶路撒冷的居民。

7波斯亚达薛西统治年间,比施兰米特利达他别及其同党上奏亚达薛西。奏章是用亚兰文写的,经过翻译后呈上。 8利宏省长和伸帅书记也写了奏本给亚达薛西王,控告耶路撒冷人,内容如下: 9利宏省长、伸帅书记和我们的同僚底拿人、亚法萨提迦人、他毗拉人、亚法撒人、亚基卫人、巴比伦人、书珊迦人、底亥人、以拦人, 10以及伟大尊贵的亚斯那巴迁来并安置在撒玛利亚各城与幼发拉底河西一带的人民, 11上奏亚达薛西王,

“‘幼发拉底河西的臣民奏告亚达薛西王, 12王该知道,从王那里到我们这里来的犹太人已经去了耶路撒冷,如今正在重建这座叛逆、罪恶之城,正在重建地基,修筑城墙。 13王该知道,如果这城建好,城墙完工,他们将不再进贡、交赋、纳税,王的税收必受亏损。 14我们既食王禄,就不能坐视王遭受损失,因此上奏于王。 15请王查看先王的记录,必从中获悉这城是叛逆之城,危害列王和各省。自古以来,城中叛乱不断,因此才被毁灭。 16我们愿王知道,这城一旦建好,城墙完工,幼发拉底河西之地就不再为王所有了。’”

17王回复利宏省长、伸帅书记及其住在撒玛利亚幼发拉底河西一带的同僚,说:“愿你们平安! 18你们呈上的奏章,经过翻译已奏报给我。 19我已命人查考,发现这城自古以来屡屡背叛列王,是悖逆和叛乱之地。 20强大的君王曾经统管耶路撒冷幼发拉底河西全境,并向人们征收贡物和赋税。 21现在你们要下令让这些人停止建造这城,等候我的谕旨。 22要认真办理这事,不可迟延,何必容事情恶化,使王受亏损呢?”

23利宏伸帅书记及其同僚接到谕旨后,急忙赶往耶路撒冷,用武力强迫犹太人停工。

恢复建殿工作

24于是,耶路撒冷上帝殿的重建工程停止了,一直停到波斯大流士第二年。