Ezara 3 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezara 3:1-13

Kumangidwanso kwa Guwa la Nsembe

1Utafika mwezi wa chisanu ndi chiwiri Aisraeli atakhala kale mʼmidzi yawo, anthu anasonkhana ku Yerusalemu ndi cholinga chimodzi. 2Kenaka Yesuwa mwana wa Yozadaki ndi ansembe anzake pamodzi ndi Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi abale ake anayamba kumanga guwa lansembe la Mulungu wa Israeli. Anatero pofuna kuti aziperekapo nsembe zopsereza monga analembera mʼbuku la Mose, munthu wa Mulungu uja. 3Ndi mantha ndi mantha chifukwa cha anthu a mʼmayikomo, iwo anamanga guwalo pa maziko ake akale, ndipo anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu pa guwapo mmawa ndi madzulo. 4Ankasunga tsiku la chikondwerero cha misasa monga momwe zinalembedwera. Ankaperekanso nsembe za tsiku ndi tsiku monga mwa chiwerengero chake potsata mwambo wake wa tsiku ndi tsiku monga zinalembedwa. 5Pambuyo pake, ankapereka nsembe zopsereza, nsembe zopereka pa nthawi ya mwezi watsopano ndi za pa masiku onse a chikondwerero oyikidwa kutamandira Yehova, kudzanso nsembe zaufulu zopereka kwa Yehova. 6Kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, iwo anayambanso kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova, ngakhale kuti maziko a Nyumba ya Yehova anali asanamangidwe.

Kumangidwanso kwa Nyumba ya Mulungu

7Ndipo anapereka ndalama kwa amisiri a miyala ndi kwa amisiri a matabwa, ndi chakudya, chakumwa ndi mafuta kwa anthu a ku Sidoni ndi a ku Turo, kuti abweretse mitengo ya mkungudza pa nyanja kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Yopa. Zonsezi anachita malinga ndi chilolezo chimene analandira kuchokera kwa Koresi, mfumu ya Peresiya.

8Tsono mu chaka chachiwiri atabwera ku Yerusalemu, ku malo akale a Nyumba ya Yehova, mwezi wachiwiri Zerubabeli mwana wa Sealatieli, Yesuwa mwana wa Yozadaki pamodzi ndi abale awo onse, ansembe, Alevi ndi onse amene anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo, anayamba kugwira ntchito. Iwo anasankha Alevi a zaka zoyambira makumi awiri kuti aziyangʼanira ntchito ya kumanga Nyumba ya Yehova. 9Yesuwa ndi ana ake aamuna kudzanso abale ake, Kadimieli ndi ana ake (ana a Yuda) onse pamodzi anasenza udindo woyangʼanira antchito ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizanso ana a Henadadi komanso Alevi, ana awo ndi abale awo.

10Amisiri omanga nyumba atamanga maziko a Nyumba ya Yehova, ansembe anabwera akuyimba malipenga, atavala zovala zaunsembe. Ndipo Alevi, zidzukulu za Asafu, anadza akuyimba matambolini ndi kutenga udindo wawo wotamanda Yehova, potsata malangizo a Davide mfumu ya Aisraeli. 11Iwo ankayimba motamanda ndi mothokoza Yehova nyimbo iyi:

“Yehova ndi wabwino;

chikondi chake pa Israeli ndi chamuyaya.”

Ndipo anthu onse ankafuwula kwambiri kumutamanda Yehova, chifukwa maziko a Nyumba ya Yehova anali kumangidwa. 12Koma ambiri mwa ansembe, Alevi ndiponso atsogoleri amabanja, akuluakulu amene anaona Nyumba ya Yehova yakale, analira mokweza pamene anaona maziko a nyumbayi akumangidwa. Komanso ena ambiri ankafuwula mosangalala. 13Choncho panalibe amene ankatha kusiyanitsa liwu lofuwula mokondwerera ndi liwu la anthu olira, chifukwa anthuwo ankafuwula kwambiri. Ndipo liwu lofuwulalo limamveka kutali.