Ezara 10 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezara 10:1-44

Anthu Avomereza Tchimo Lawo

1Pamene Ezara ankapemphera ndi kuvomereza tchimo lawo, akulira ndipo atadzigwetsa pansi ku Nyumba ya Mulungu, anthu ambiri anabwera kwa iye kudzasonkhana naye. Panali amuna, akazi ndi ana, kuchokera mʼdziko lonse la Israeli ndipo ankalira kwambiri. 2Ndipo Sekaniya, mwana wa Yehieli, wa fuko la Elamu, anawuza Ezara kuti, “Ife takhala osakhulupirika kwa Mulungu wathu ndipo takhala tikukwatira akazi achilendo a mayiko akunowa. Koma ngakhale zili chomwechi, chikhulupiriro chilipobe pakati pa Aisraeli. 3Tsopano tiyeni tichite naye pangano Mulungu wathu, kuti tichotse akazi onsewa ndi ana awo, potsata malangizo a inu mbuye wanga ndi wa anthu amene amaopa malamulo a Mulungu wathu. Lolani kuti zichitike motsatira malamulo. 4Tsono dzukani, imeneyi ndi ntchito yanu. Ife tikuthandizani. Limbani mtima ndipo gwirani ntchitoyi.”

5Choncho Ezara anayimirira ndipo analumbiritsa akulu a ansembe, Alevi ndi Aisraeli onse, kuti adzachitedi monga Sekaniya ananenera. Tsono onse analumbira. 6Ezara anachoka ku Nyumba ya Mulungu napita ku chipinda cha Yehohanani, mwana wa Eliyasibu. Anatandala kumeneko usiku wonse ndipo sanadye chakudya kapena kumwa madzi popeza ankalira chifukwa cha kusankhulupirika kwa anthu obwera ku ukapolo.

7Tsono anthu analengeza mʼdziko lonse la Yuda ndi mʼmizinda yonse ya Yerusalemu kwa onse ochokera ku ukapolo aja kuti asonkhane ku Yerusalemu. 8Ananena kuti wina aliyense amene saonekera pakutha pa masiku atatu, adzalandidwa katundu wake, potsata malangizo a nduna ndi akuluakulu, ndipo adzachotsedwa mʼgulu la anthu obwerako ku ukapolo.

9Choncho anthu onse a mʼdziko la Yuda ndi a mʼdziko la Benjamini anasonkhana ku Yerusalemu asanathe masiku atatu. Limeneli linali tsiku la 20 la mwezi wa 9. Anthu onse anakhala pansi pa bwalo la Nyumba ya Mulungu akunjenjemera chifukwa cha mvula yambiri imene inagwa. 10Ndipo wansembe Ezara anayimirira nawuza anthuwo kuti, “Inu mwachimwa pomakwatira akazi achikunja ndi kumawonjezera pa tchimo la Aisraeli. 11Tsopano lapani kwa Yehova, Mulungu wa makolo anu ndi kuchita zimene akufuna. Dzipatuleni kwa anthu a mayiko enawa ndi kwa akazi achikunjawa.”

12Gulu lonse la anthu linayankha ndi mawu ofuwula kuti, “Nʼzoona! Tichita monga mwaneneramu. 13Koma pano pali anthu ambiri ndiponso mvula ikugwa kwambiri, choncho sitingakayime panja. Ndiponso ntchitoyi si ya tsiku limodzi kapena awiri, chifukwa tachimwa kwambiri pa zimene tachitazi. 14Tsono mulole kuti atsogoleri athu ayimirire mʼmalo mwa anthu onse. Aliyense wa mʼmizinda yathu amene anakwatira mkazi wachikunja abwere pa nthawi imene inu munene, ndipo abwere pamodzi ndi akuluakulu ndi oweruza a mzindawo. Choncho mkwiyo wa Mulungu wathu udzatichoka.” 15Koma Yonatani yekha mwana wa Asaheli ndi Yahazieli mwana wa Tikiva ndiwo anatsutsapo pa zimenezi. Tsono Mesulamu ndi Mlevi Sebetai anawayikira kumbuyo.

16Choncho anthu obwerako ku ukapolo aja anachita zimene zimafunika. Ndipo wansembe Ezara anasankha amuna amene anali atsogoleri a mabanja potsata mafuko awo ndipo onsewo analembedwa mayina awo. Tsiku loyamba la mwezi wa khumi anayambapo kuyifufuza nkhani imeneyi. 17Ndipo pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba anali atathana nawo anthu amene anakwatira akazi achilendo aja.

Okwatira Akazi Achilendo

18Nawu mʼndandanda wa ansembe amene anakwatira akazi achikunja:

Pa banja la Yesuwa ndi abale ake, ana a Yozadaki, panali awa: Maaseiya, Eliezara, Yaribu ndi Gedaliya. 19Iwo anatsimikiza zochotsa akazi awo ndipo chifukwa cha kulakwa kwawo aliyense anapereka nkhosa yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo.

20Pa banja la Imeri panali awa:

Hanani ndi Zebadiya.

21Pa banja la Harimu panali awa:

Maseya, Eliya, Semaya, Yehieli ndi Uziya.

22Pa banja la Pasuri panali awa:

Eliyoenai, Maseya, Ismaeli, Netaneli, Yozabadi ndi Eleasa.

23Pakati pa Alevi panali:

Yozabadi, Simei, Kelaya (ndiye kuti, Kelita). Petaya, Yuda ndi Eliezara.

24Pakati pa oyimba nyimbo panali

Eliyasibu.

Ochokera kwa alonda a zipata:

Salumu, Telemu ndi Uri.

25Ochokera pakati pa Aisraeli ena:

a fuko la Parosi anali

Ramiya, Iziya, Malikiya, Miyamini, Eliezara, ndi Benaya.

26A fuko la Elamu anali

Mataniya, Zekariya, Yehieli, Abidi, Yeremoti ndi Eliya.

27A fuko la Zatu anali

Eliyoenai, Eliyasibu, Mataniya, Yeremoti, Zabadi ndi Aziza.

28A fuko la Bebai anali

Yehohanani, Hananiya, Zabayi ndi Atilayi.

29A fuko la Bani anali

Mesulamu, Maluki, Adaya, Yasubu, Seali ndi Yeremoti.

30A fuko la Pahati-Mowabu anali

Adina, Kelali, Benaya, Maseya, Mataniya, Bezaleli, Binuyi ndi Manase.

31A fuko la Harimu anali

Eliezara, Isiya, Malikiya, Semaya, Simeoni, 32Benjamini, Maluki ndi Semariya.

33A fuko la Hasumu anali

Mataneyi, Matata, Zabadi, Elifeleti, Yeremayi, Manase ndi Simei.

34A fuko la Bani anali

Madai, Amramu, Uweli, 35Benaya, Bediya, Keluhi, 36Vaniya, Meremoti, Eliyasibu, 37Mataniya, Matenayi ndi Yasu.

38A fuko la Binuyi anali

Simei, 39Selemiya, Natani, Adaya, 40Makinadebayi, Sasai, Sarai, 41Azaleli, Selemiya, Semariya, 42Salumu, Amariya ndi Yosefe.

43A fuko la Nebo anali

Yeiyeli, Matitiya, Zabadi, Zebina, Yadai, Yoweli ndi Benaya.

44Onsewa anakwatira akazi achilendo. Tsono anawasudzula akaziwo ndi kuwatumiza kwawo pamodzi ndi ana awo.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

以斯拉記 10:1-44

終止雜婚

1以斯拉禱告、認罪、哭泣、俯伏在上帝的殿前時,一大群以色列人,包括男女和孩子,都聚集到他那裡,與他一起痛哭。 2以攔宗族耶歇的兒子示迦尼以斯拉說:「我們對我們的上帝不忠,娶這地方的外族女子為妻,但以色列還有希望。 3現在,我們來與我們的上帝立約,聽從你和那些敬畏我們上帝誡命之人的指示,遵照律法而行,送走這些妻子和她們的兒女。 4起來吧!這事由你處理,我們支持你,放膽去做吧!」

5於是,以斯拉起來,要祭司長、利未人和所有以色列人起誓照這話去做,他們就都起了誓。 6以斯拉從上帝的殿前起來,進了以利亞實的兒子約哈難的房間。他在那裡不吃不喝,為流亡歸來者的不忠而憂傷。

7他們在猶大耶路撒冷發出通告,要求所有流亡歸來的人在耶路撒冷集合。 8按照眾首領和長老的決定,三天之內未到者,其財產會被沒收,他本人也要被逐出流亡歸來者的會。

9三天內,所有的猶大人和便雅憫人都聚集在耶路撒冷。九月二十日,大家都坐在上帝的殿前面的廣場上。因為這事,加上當時下大雨,眾人都戰戰兢兢。

10以斯拉祭司站起來對他們說:「你們對上帝不忠,娶外族的女子為妻,加重了以色列的罪惡。 11現在,你們要向你們祖先的上帝耶和華認罪,遵行祂的旨意,與這地方的人和你們的外族妻子斷絕關係。」

12會眾都高聲回答說:「你說的對,我們必照你的話做。 13可是,人這麼多,又逢大雨季節,我們不能總站在外面,並且這事一兩天也解決不了,因為我們在這事上犯了大罪。 14不如讓我們的首領為全體會眾處理這事,讓那些娶了外族女子為妻的人在指定的時間與本城的長老和審判官一起來找首領解決,直到我們的上帝因這事而發的烈怒離開我們。」

15只有撒黑的兒子約拿單特瓦的兒子雅哈謝反對這事,支持他們的還有米書蘭利未沙比太

16流亡歸來的人都遵照建議而行。以斯拉祭司按家族選出各族長,都是點名指定的。他們從十月一日開始著手查辦這事, 17到次年一月一日才查清娶外族女子為妻的人。

18祭司中娶外族女子為妻的有耶書亞的子孫約薩達的兒子及其弟兄瑪西雅以利以謝雅立基大利19他們答應休掉自己的妻子,並從羊群中獻上一隻公綿羊為自己贖罪。 20音麥的子孫中有哈拿尼西巴第雅21哈琳的子孫中有瑪西雅以利雅示瑪雅耶歇烏西雅22巴施戶珥的子孫中有以利約乃瑪西雅以實瑪利拿坦業約撒拔以利亞撒

23利未人中有約撒拔示每基拉雅——又名基利他毗他希雅猶大以利以謝24歌樂手中有以利亞實。殿門守衛中有沙龍提聯烏利

25其他以色列人中有巴錄的子孫拉米耶西雅瑪基雅米雅民以利亞撒瑪基雅比拿雅26以攔的子孫中有瑪他尼撒迦利亞耶歇押底耶利末以利雅27薩土的子孫中有以利約乃以利亞實瑪他尼耶利末撒拔亞西撒28比拜的子孫中有約哈難哈拿尼雅薩拜亞勒29巴尼的子孫中有米書蘭瑪鹿亞大雅雅述示押耶利末30巴哈·摩押的子孫中有阿底拿基拉比拿雅瑪西雅瑪他尼比撒列賓內瑪拿西31哈琳的子孫中有以利以謝伊示雅瑪基雅示瑪雅西緬32便雅憫瑪鹿示瑪利雅33哈順的子孫中有瑪特乃瑪達他撒拔以利法列耶利買瑪拿西示每34巴尼的子孫中有瑪玳暗蘭烏益35比拿雅比底雅基祿36瓦尼雅米利末以利亞實37瑪他尼瑪特乃雅掃38賓內的子孫中有示每39示利米雅拿單亞大雅40瑪拿底拜沙賽沙賴41亞薩利示利米雅示瑪利雅42沙龍亞瑪利雅約瑟43尼波的子孫中有耶利瑪他提雅撒拔西比拿雅玳約珥比拿雅

44以上這些人都娶了外族女子為妻,其中有些還生了子女。