Eksodo 33 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 33:1-23

1Ndipo Yehova anati, “Chokani pa malo ano, iwe ndi anthu amene unawatulutsa mʼdziko la Igupto. Pitani ku dziko limene ine ndinalonjeza ndi lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo kuti, ‘Ine ndidzalipereka kwa zidzukulu zanu.’ 2Ndipo ndidzatumiza mngelo patsogolo panu kuthamangitsa Akanaani, Aamori, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. 3Pitani ku dziko loyenda mkaka ndi uchi. Koma ine sindidzapita nanu, chifukwa anthu inu ndinu nkhutukumve ndipo nditha kukuwonongani mʼnjiramo.”

4Anthu atamva mawu owopsawa, anayamba kulira ndipo palibe anavala zodzikometsera. 5Pakuti Yehova anali atanena kwa Mose kuti, “Awuze Aisraeli kuti, ‘Inu ndinu nkhutukumve.’ Ngati ine ndipita ndi inu kwa kanthawi, nditha kukuwonongani. Tsopano vulani zodzikometsera zanu ndipo ine ndidzaganiza choti ndichite nanu.” 6Kotero Aisraeli anavula zodzikometsera zawo pa phiri la Horebu.

Tenti ya Msonkhano

7Tsono Mose ankatenga tenti ndi kukayimanga kunja kwa msasa chapatalipo, ndipo ankayitcha “tenti ya msonkhano.” Aliyense wofuna kukafunsa kanthu kwa Yehova amapita ku tenti ya msonkhano kunja kwa msasa. 8Ndipo nthawi ina iliyonse imene Mose amapita ku tenti anthu onse amanyamuka ndi kuyimirira pa makomo amatenti awo, kumuyangʼana Mose mpaka atalowa mu tentimo. 9Mose akamalowa mu tenti, chipilala cha mtambo chimatsika ndi kukhala pa khomo pamene Yehova amayankhula ndi Mose. 10Nthawi zonse anthu akaona chipilala cha mtambo chitayima pa khomo la tentiyo amayimirira ndi kupembedza, aliyense ali pa khomo la tenti yake. 11Yehova amayankhula ndi Mose maso ndi maso ngati mmene munthu amayankhulira ndi bwenzi lake. Kenaka Mose amabwerera ku msasa koma womuthandiza wake, Yoswa, mwana wa Nuni samachoka pa tentiyo.

Mose ndi Ulemerero wa Yehova

12Mose anati kwa Yehova, “Inu mwakhala mukundiwuza kuti, ‘Tsogolera anthu awa,’ koma simunandiwuze amene mudzamutuma kuti apite pamodzi nane. Inu mwanena kuti, ‘Ndikukudziwa bwino kwambiri ndipo wapeza chisomo pamaso panga.’ 13Ngati mwakondwera nane ndiphunzitseni njira zanu kuti ndikudziweni ndi kupitiriza kupeza chisomo pamaso panu. Kumbukirani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.”

14Yehova anayankha kuti, “Ine ndemwe ndidzapita pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakupatsa mpumulo.”

15Kenaka Mose anati kwa Yehova, “Ngati inu simupita nafe, musatitumize kuti tipite, kutichotsa pano. 16Kodi wina adzadziwa bwanji kuti inu mwandikomera mtima pamodzi ndi anthu awa ngati simupita nafe? Kodi nʼchiyani chomwe chidzatisiyanitse pakati pa anthu onse amene ali pa dziko lapansi?”

17Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzachita zimene iwe wandipempha chifukwa Ine ndikukondwera nawe, ndikukudziwa bwino lomwe.”

18Kenaka Mose anati, “Tsopano ndionetseni ulemerero wanu.”

19Ndipo Yehova anati, “Ine ndidzakuonetsa ulemerero wanga wonse ndipo ndidzatchula dzina langa lakuti Yehova pamaso pako. Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.” 20Iye anati, “Koma iwe sungaone nkhope yanga, pakuti palibe munthu amene amaona Ine nakhala ndi moyo.”

21Ndipo Yehova anati, “Pali malo pafupi ndi ine pomwe ungathe kuyima pa thanthwe. 22Pamene ulemerero wanga udutsa, ndidzakuyika mʼphanga la thanthwe ndi kukuphimba ndi dzanja langa mpaka nditadutsa. 23Kenaka ine ndidzachotsa dzanja langa ndipo iwe udzaona msana wanga, koma nkhope yanga sidzaoneka.”