Eksodo 26 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 26:1-37

Chihema cha Mapemphero

1“Panga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso apete pa nsaluzo Akerubi. 2Nsalu zonse zikhale zofanana. Mulitali mwake zikhale mamita khumi ndi atatu, mulifupi mamita awiri. 3Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi. Uchite chimodzimodzi ndi nsalu zisanu zinazo. 4Panga zokolowekamo za nsalu yobiriwira mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsiriza ya mbali ina. Uchitenso chimodzimodzi ndi nsalu yotsiriza ya mbali inayo. 5Upange zokolowekamo 50 pa nsalu yoyamba ndi zokolowekamo makumi asanu zinanso pa nsalu inayo. Upange motero kuti zokolowekamozo ziziyangʼanana. 6Kenaka upange ngowe zagolide makumi asanu zolumikizira nsalu ziwirizo kuti zipange chihema chimodzi.

7“Upange nsalu za ubweya wambuzi zophimba pamwamba pa chihemacho. Nsalu zonse pamodzi zikhale khumi ndi imodzi. 8Nsalu zonse khumi ndi imodzi zikhale zofanana. Mulitali mwake mukhale mamita khumi ndi anayi ndipo mulifupi mwake mukhale mamita awiri. 9Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi ndipo zina zisanu ndi imodzi uzilumikizenso kuti ikhale nsalu imodzinso. Nsalu yachisanu ndi chimodzi imene ili kutsogolo kwa tenti uyipinde pawiri. 10Upange zokolowekamo 50 mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsirizira ya nsalu yoyamba yolumikiza ija. Upangenso zokolowekamo zina 50 mʼmphepete mwa nsalu yotsirizira ya nsalu inanso yolumikiza ija. 11Kenaka upange ngowe 50 zamkuwa ndipo uzilowetse mu zokolowekazo. Ndiye uphatikize nsalu ziwirizo kuti tentiyo ikhale imodzi. 12Theka lotsalira la nsaluyo lidzalendewera kumbuyo kwa chihemacho. 13Nsalu yotsalira ya masentimita 46 mulitali mwake mʼmbali zonse ziwiri idzalendewere kuphimba mbali ziwirizo. 14Upange chikopa cha nkhosa zazimuna cha utoto wofiira chophimbira tentiyo ndipo pamwamba pake upangireponso chophimbira china cha zikopa za akatumbu.

15“Upange maferemu amatabwa amtengo wa mkesha oyimikira chihemacho. 16Feremu iliyonse ikhale yotalika mamita anayi ndipo mulifupi mwake mukhale masentimita 69. 17Thabwa lililonse likhale ndi zolumikizira ziwiri. Upange maferemu onse a chihemacho ndi matabwa otere. 18Upange maferemu makumi awiri a mbali yakummwera kwa chihemacho. 19Ndipo upange matsinde 40 asiliva ndipo uwayike pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse pakhale matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija. 20Ndipo mbali yakumpoto ya chihemacho upangenso maferemu makumi awiri. 21Upangenso matsinde 40 asiliva, awiri pansi pa feremu iliyonse. 22Upange maferemu asanu ndi imodzi a kumbuyo kwa tenti, kumbali yakumadzulo. 23Ndipo upangenso maferemu awiri a pa ngodya yakumbuyo kwenikweni kwa tenti. 24Pa ngodya ziwirizi pakhale maferemu awiri, kuyambira pansi mpaka pamwamba ndipo alumikizidwe pa ngowe imodzi. Maferemu onse akhale ofanana. 25Choncho pakhale maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri akhale pansi pa feremu iliyonse.

26“Upange mitanda ya matabwa amtengo wa mkesha: mitanda isanu ikhale ya maferemu a mbali imodzi ya chihema, 27mitanda isanu inanso ikhale ya maferemu a mbali inayo. Pakhalenso mitanda ina isanu ya mbali yakumadzulo, kumapeto kwenikweni kwa chihema. 28Mtanda wapakati pa maferemuwo uchokere pa maferemu a mbali ina mpaka mbali inanso. 29Maferemuwo uwakute ndi golide ndiponso upange mphete zagolide zogwiriziza mitandayo. Ndipo mitandayonso uyikute ndi golide.

30“Upange chihema mofanana ndi momwe ndinakuonetsera pa phiri paja.

31“Upange nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo ikhale yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso apetepo zithunzi za Akerubi. 32Nsaluyo uyikoloweke pa nsanamira zinayi zamtengo wa mkesha zokutidwa ndi golide zomwe zili ndi ngowe zagolide, zomwe zayima pa matsinde asiliva anayi. 33Ukoloweke kataniyo ku ngowe ndipo uyike Bokosi la Chipangano mʼkatimo. Kataniyo idzalekanitse malo wopatulika ndi malo wopatulika kwambiri. 34Uyike chivundikiro pa bokosi laumboni ku malo wopatulika kwambiri. 35Uyike tebulo kunja kwa katani yotchinga cha kumpoto kwa chihema ndipo uyike choyikapo nyale chija kummwera moyangʼanana ndi tebulolo.

36“Pa chipata cholowera mu chihema, uyikepo nsalu yamtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira, yomwe ndi yofewa ndi yosalala, yopetedwa bwino ndi amisiri aluso. 37Upange ngowe zagolide za nsaluyo ndi nsanamira zisanu zamtengo wa mkesha ndipo uzikute ndi golide. Upangenso matsinde asanu amkuwa a nsanamirazo.”

New Russian Translation

Исход 26:1-37

Скиния

(Исх. 36:8-38)

1– Сделай скинию из десяти покрывал крученого льна голубой, пурпурной и алой пряжи, с искусно вышитыми на них херувимами. 2Все покрывала пусть будут одинаковыми: двадцать восемь локтей в длину и четыре локтя в ширину26:2 Около 14 м в длину и 2 м в ширину.. 3Сшей пять из них друг с другом и сделай то же самое с пятью остальными. 4Сделай петли из голубой ткани по краю последнего покрывала каждого ряда. 5Сделай пятьдесят петель на первом покрывале первого ряда и пятьдесят парных им петель на последнем покрывале второго ряда. 6Сделай пятьдесят золотых крючков и сцепи ими покрывала, чтобы скиния стала одним целым.

7Сделай одинадцать покрывал из козьей шерсти – покров скинии. 8Пусть все одиннадцать покрывал будут одинаковые: тридцать локтей в длину и четыре локтя в ширину26:8 Около 15 м в длину и 2 м в ширину.. 9Сшей пять из этих покрывал в один ряд, а шесть других – в другой ряд. Сложи шестое покрывало вдвое перед входом в шатер. 10Сделай по пятьдесят петель по краю последних покрывал в обоих рядах. 11Сделай пятьдесят бронзовых крючков и вложи их в петли, чтобы соединить покров скинии в одно целое. 12Остаток шатровых покрывал, оставшуюся половину покрывала – нужно свесить позади скинии. 13Локоть26:13 Около 50 см. лишней длины шатровых покрывал с обеих сторон нужно свесить по обе стороны скинии так, чтобы накрывать ее. 14Сделай для шатра покрытие из бараньих кож, покрашенных красным цветом, и кож дюгоней.

15Сделай для скинии прямые брусья из акации. 16Каждый брус должен быть десять локтей в длину и полтора локтя в ширину26:16 Около 5 м в длину и 75 см в ширину., 17с двумя выступами, параллельными друг другу. Сделай такими все брусья скинии. 18Сделай двадцать брусьев для южной стороны скинии 19и сорок серебряных оснований под них – по два основания на каждый брус, по одному под выступ. 20Для другой, северной стороны скинии, сделай двадцать брусьев 21и сорок серебряных оснований – по два под каждый брус. 22Сделай шесть брусьев для дальнего, западного конца скинии 23и два бруса для ее углов. 24Пусть эти угловые брусья будут соединены внизу и скреплены вверху одним кольцом; пусть так будет сделано с обоими угловыми брусьями. 25Такими будут восемь брусьев и шестнадцать серебряных оснований – по два под каждый брус.

26Еще сделай перекладины из акации: пять для брусьев на одной стороне скинии, 27пять для брусьев на другой стороне и пять для брусьев в дальнем, западном конце скинии. 28Пусть центральная перекладина тянется из конца в конец скинии посередине брусьев. 29Позолоти брусья и сделай золотые кольца, чтобы держать перекладины. Позолоти и перекладины.

30Поставь скинию по образцу, показанному тебе на горе.

31Сделай завесу из голубой, пурпурной и алой пряжи и крученого льна, с искусно вышитыми на ней херувимами. 32Повесь ее на золотых крюках четырех позолоченных столбов из акации, которые стоят на серебряных основаниях. 33Повесь завесу на крючках и внесите туда, за завесу, ковчег свидетельства. Завеса будет отделять Святое место от Святого Святых. 34Положи крышку искупления на ковчег свидетельства в Святом Святых. 35Поставь стол вне завесы на северной стороне скинии. Поставь светильник напротив него, на южной стороне.

36Для входа в шатер сделай завесу из голубой, пурпурной и алой пряжи и крученого льна, украшенную шитьем. 37Сделай для этой завесы пять позолоченных столбов из акации с золотыми крюками. Сделай для них пять бронзовых оснований.