Eksodo 24 – CCL & KLB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 24:1-18

Kutsimikizira kwa Pangano

1Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Bwera ku phiri kuno kwa Yehova, iwe pamodzi ndi Aaroni, Nadabu, Abihu ndi akuluakulu a Israeli makumi asanu ndi awiri. Enanu mundipembedze muli chapatali. 2Koma Mose yekha ayandikire Yehova, ndipo enawo asayandikire. Komanso anthu ena onse asakwere nawe ku phiri kuno.”

3Tsono Mose anapita kukawuza anthu mawu onse a Yehova ndi malamulo onse, ndipo anthu onse anayankha mogwirizana kuti, “Tidzachita zonse zimene Yehova wanena.” 4Ndipo Mose analemba zonse zimene Yehova ananena.

Mmawa mwake Mose anadzuka nayamba kumanga guwa lansembe mʼmunsi mwa phirilo ndipo anayimika miyala khumi ndi iwiri ngati zipilala kuyimira mafuko khumi ndi awiri a Israeli. 5Kenaka Mose anatuma Aisraeli achinyamata kuti aphe ndi kukapereka kwa Yehova nsembe zopsereza zachiyanjano. 6Mose anatenga theka la magazi ndi kuyika mʼmbale, ndipo theka linalo analiwaza pa guwa lansembe. 7Anatenganso Buku la Chipangano ndi kuwerengera anthu. Anthuwo anayankha kuti, “Zonse zimene Yehova wanena tamva, ndipo tidzazichita.”

8Kenaka Mose anatenga magazi, nawaza anthuwo ndipo anati, “Awa ndi magazi a pangano limene Yehova wapanga ndi inu molingana ndi mawu ake onsewa.”

9Kenaka Mose pamodzi ndi Aaroni, Nadabu, Abihu ndi akuluakulu makumi asanu ndi awiri a Israeli aja anakwera ku phiri, 10ndipo anaona Mulungu wa Israeli. Pansi pa mapazi ake panali njira yoyendamo yopangidwa ndi mwala wa safiro woyalidwa bwino wa maonekedwe owala ngati thambo. 11Ngakhale anaona Yehova koma sanafe, mʼmalo mwake anadya ndi kumwa.

12Yehova anati kwa Mose, “Bwera kwa ine ku phiri kuno, ndipo udikire konkuno. Ndidzakupatsa miyala imene ndalembapo malemba kuti ndiwaphunzitse.”

13Ndipo anayamba ulendo wopita ku phiri la Mulungu pamodzi ndi womuthandiza wake Yoswa. 14Apa nʼkuti Mose atawawuza akuluakulu aja kuti, “Mudikire pano mpaka titabweranso. Aaroni ndi Huri ali nanu, aliyense amene ali ndi milandu apite kwa iwo.”

15Mose atakwera ku phiri kuja mtambo unaphimba phirilo. 16Ulemerero wa Yehova unakhala pa phiri la Sinai, ndipo mtambo unaphimba phirilo kwa masiku asanu ndi limodzi. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri Yehova anayitana Mose kuchokera mu mtambowo. 17Ulemerero wa Yehova uja unkaoneka ngati malawi a moto pamwamba pa phirilo. 18Ndipo Mose analowa mʼmitambo nakwera phiri. Iye anakhala ku phiriko 40 usana ndi usiku.

Korean Living Bible

출애굽기 24:1-18

계약의 확인

1그리고 여호와께서 모세에게 말씀하셨다. “너는 아론과 나답과 아비 후와 이스라엘 장로 70명과 함께 나 여호와에게 올라와 멀리서 경배하고

2너만 나에게 가까이 오너라. 그러나 다른 사람이 가까이 와서는 안 되며 또 백성들이 너와 함께 올라와서도 안 된다.”

3모세가 내려와 백성들에게 여호와의 모든 말씀과 법을 전하자 그들이 한 목소리로 “여호와께서 말씀하신 모든 것을 우리가 다 지키겠습니다” 하고 대답하였다.

4모세는 여호와께서 말씀하신 모든 것을 기록하고 다음날 아침 일찍 일어나 산기슭에 단을 쌓고 이스라엘의 열두 지파대로 열두 기둥을 세웠다.

5그리고 청년들을 보내 불로 태워 바치는 번제와 소로 화목제를 여호와께 드리게 하였다.

6그런 다음 모세는 짐승의 피를 가져다가 반은 여러 그릇에 담아 놓고 반은 단에 뿌렸다.

7그리고 그가 여호와의 말씀이 기록된 계약의 책을 가져다가 백성들에게 낭독하자 그들은 “우리가 여호와의 말씀에 순종하여 그대로 행하겠습니다” 하고 말하였다.

8그러자 모세가 그릇의 피를 가져다가 백성에게 뿌리며 “이것은 여호와께서 이 모든 말씀에 따라 여러분과 맺은 계약의 피입니다” 하였다.

시내산에 올라간 모세

9모세와 아론과 나답과 아비후와 이스라엘의 장로 70명이 산으로 올라가서

10이스라엘의 하나님을 보니 그의 발 아래에는 청옥을 깔아 놓은 것 같았고 하늘처럼 맑았다.

11그러나 하나님은 손을 들어 이스라엘의 이 지도자들을 치지 않으셨고 그들은 하나님을 보고서도 먹고 마셨다.

1224:12 암시됨.그 후 여호와께서 모세에게 말씀하셨다. “너는 산에 올라 나에게 와서 여기 머물러 있거라. 네가 백성들을 가르칠 수 있도록 내가 법과 명령을 직접 기록한 두 돌판을 너에게 주겠다.”

13그래서 모세는 그의 보좌관 여호수아와 함께 하나님의 산으로 올라가면서

14장로들에게 말하였다. “여러분은 우리가 돌아올 때까지 여기서 기다리십시오. 아론과 훌이 여러분과 함께 있을 것입니다. 그러니 해결할 문제가 있는 사람은 그들에게 가도록 하십시오.”

15모세가 산에 오르자 구름이 산을 가리며

1624:16 원문에는 ‘여호와의영광이’여호와의 영광의 광채가 시내산 위에 머물러 있고 구름이 6일 동안 산을 가리더니 7일째 되는 날에 여호와께서 구름 가운데서 모세를 부르셨다.

17이때 이스라엘 백성의 눈에는 그 영광스러운 광채가 산꼭대기에서 무섭게 타오르는 불처럼 보였다.

18모세는 구름이 뒤덮인 산으로 계속 올라가서 거기서 40일 동안 밤낮 머물러 있었다.