Eksodo 15 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 15:1-27

Nyimbo ya Mose ndi Miriamu

1Ndipo Mose ndi Aisraeli anayimbira Yehova nyimbo iyi:

“Ine ndidzayimbira Yehova

pakuti wakwezeka mʼchigonjetso.

Kavalo ndi wokwera wake,

Iye wawaponya mʼnyanja.

2Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;

ndiye chipulumutso changa.

Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamutamanda,

Mulungu wa makolo anga, ine ndidzamukweza.

3Yehova ndi wankhondo;

Yehova ndilo dzina lake.

4Magaleta a Farao ndi asilikali ake ankhondo

Iye wawaponya mʼnyanja.

Akatswiri ankhondo amphamvu a Farao

amizidwa mʼNyanja Yofiira.

5Nyanja yakuya inawaphimba;

Iwo anamira pansi ngati mwala.”

6Yehova, dzanja lanu lamanja

ndi laulemerero chifukwa cha mphamvu zake.

Ndithu Yehova, dzanja lanu lamanja

linaphwanya mdani.

7Ndi ulemerero wanu waukulu,

munagonjetsa okutsutsani.

Inu munatumiza mkwiyo wanu waukulu;

ndipo unawapsereza ngati udzu.

8Ndi mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu

madzi anawunjikana pamodzi.

Nyanja yakuya ija inasanduka

madzi owuma gwaa kufika pansi.

9Mdaniyo anati,

“Ine ndidzawalondola, ndipo ndidzawagwira.

Ndidzagawa chuma chawo;

ndiye chokhumba changa chidzakwaniritsidwa.

Ine ndidzasolola lupanga langa,

ndi mkono wanga ndidzawawononga.”

10Koma Inu munawuzira mphepo yanu,

ndipo nyanja inawaphimba.

Iwo anamira ngati chitsulo

mʼmadzi amphamvu.

11Ndithu Yehova, pakati pa milungu,

ndani afanana nanu? Inu amene muli woyera,

ndiponso wotamandika wolemekezeka,

chifukwa cha ntchito zanu,

zazikulu ndi zodabwitsa?

12Munatambasula dzanja lanu lamanja

ndipo dziko linawameza.

13Ndi chikondi chanu chosasinthika mudzatsogolera

anthu amene munawawombola.

Ndi mphamvu zanu munawatsogolera

ku malo anu woyera.

14Anthu amitundu ina anamva za mbiriyi ndipo ananjenjemera ndi mantha,

mantha woopsa agwira anthu a dziko la Filisiti.

15Tsopano mafumu a ku Edomu agwidwa ndi mantha aakulu,

otsogolera a dziko la Mowabu akunjenjemera ndi mantha,

ndipo anthu a ku Kanaani asungunuka ndi mantha.

16Onse agwidwa ndi mantha woopsa.

Popeza anaona mphamvu zanu zazikulu,

iwo ayima chilili ngati mwala mpaka anthu anu,

Inu Yehova atadutsa;

inde mpaka atadutsa anthu amene munawagula.

17Inu mudzawalowetsa ndi kuwakhazikitsa

pa phiri lanu.

Pa malo pamene Inu Yehova munawapanga kuti muzikhalapo;

malo wopatulika amene Inu Ambuye munawakonza ndi manja anu.

18“Yehova adzalamula

mpaka muyaya.”

19Akavalo a Farao, magaleta ndi oyendetsa akavalo atalowa mʼnyanja, Yehova anawabwezera madziwo mʼnyanja ndi kuwamiza, koma Aisraeli anawoloka nyanjayo powuma. 20Ndipo Miriamu mneneri wamkazi, mlongo wa Aaroni anatenga zoyimbira ndipo akazi onse anamutsatira pambuyo, akuyimba ndi zoyimbira ndi kuvina. 21Miriamu anawayimbira nyimbo iyi:

“Imbirani Yehova,

chifukwa iye wapambana.

Kavalo ndi wokwerapo wake

Iye wawamiza mʼnyanja.”

Madzi a ku Mara ndi Elimu

22Ndipo Mose anatsogolera Israeli kuchoka ku nyanja yofiira ndi kupita ku chipululu cha Suri. Anayenda mʼchipululu masiku atatu wosapeza madzi. 23Ndipo anafika ku Mara. Koma sanathe kumwa madzi akumeneko chifukwa anali owawa. (Ndi chifukwa chake malowo amatchedwa Mara). 24Tsono anthu aja anadandaulira Mose ndi kumufunsa kuti, “Kodi tikumwa chiyani?”

25Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, ndipo Yehova anamuonetsa kamtengo. Iye anakaponya mʼmadzimo ndipo madzi anakhala abwino.

Kumeneko Yehova anawayikira lamulo ndi maweruziro. Kumenekonso Yehova anawayesa. 26Yehova anati, “Ngati inu mudzamvetsa bwino mawu anga, kuchita zolungama, kumvera malamulo anga ndi kusamalitsa zimene ndikukuwuzani ndiye kuti Ine sindidzayika pa inu matenda amene ndinayika pa anthu a ku Igupto popeza ndine Yehova amene ndimakuchiritsani.”

27Kenaka anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa makumi asanu ndi awiri, ndipo anamanga misasa yawo kumeneko pafupi ndi madzi.